Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 1:1-31
1 Ine Paulo, woitanidwa kukhala mtumwi+ wa Khristu Yesu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, pamodzi ndi Sositene mʼbale wathu,
2 ndikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto.+ Ndikulembera inu amene mwayeretsedwa mwa Khristu Yesu,+ amene mwaitanidwa kuti mukhale oyera, pamodzi ndi onse amene ali kulikonse omwe akuitana pa dzina la Ambuye wathu, Yesu Khristu,+ Ambuye wawo ndiponso wathu.
3 Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu zikhale nanu.
4 Nthawi zonse ndimathokoza Mulungu wanga chifukwa cha inu, poona kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kumene anakusonyezani kudzera mwa Khristu Yesu.
5 Chifukwa chogwirizana naye, ndinu olemera mʼzinthu zonse, ndipo wakuthandizani kukhala ndi luso la kulankhula ndiponso kudziwa zinthu zonse,+
6 popeza umboni wonena za Khristu+ wakhazikika pakati panu.
7 Palibe mphatso imene mukuperewera pamene mukuyembekezera mwachidwi kuululidwa kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+
8 Komanso Mulungu adzakulimbitsani mpaka pamapeto, kuti musakhale ndi chifukwa chokunenezerani mʼtsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu.+
9 Mulungu amene anakuitanani kuti mukhale ogwirizana ndi Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu, ndi wokhulupirika.+
10 Tsopano ndikukudandaulirani abale, mʼdzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti nonse muzilankhula mogwirizana ndipo pakati panu pasakhale kugawanika,+ koma mukhale ogwirizana kwambiri pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.+
11 Chifukwa anthu ena a mʼbanja la Kuloe andiuza za inu, abale anga, kuti pakati panu pali kugawanika.
12 Ndikutanthauza kuti, ena mwa inu akumanena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ena akuti, “Ine ndine wa Apolo,”+ enanso akuti, “Ine ndine wa Kefa,”* pamene ena akuti, “Ine ndine wa Khristu.”
13 Kodi Khristu wakhala wogawanika? Kodi Paulo anapachikidwa pamtengo wozunzikirapo* kuti inu mupulumutsidwe? Kapena kodi munabatizidwa mʼdzina la Paulo?
14 Ndikuthokoza Mulungu kuti sindinabatize aliyense wa inu kupatulapo Kirisipo+ ndi Gayo,+
15 moti wina sanganene kuti munabatizidwa mʼdzina langa.
16 Nʼzoona kuti ndinabatizanso anthu a mʼbanja la Sitefana.+ Koma za enawo, sindikudziwa ngati ndinabatizapo aliyense.
17 Khristu sananditume kuti ndizibatiza anthu, koma kuti ndizilengeza uthenga wabwino,+ osati mwa luso la kulankhula,* kuopera kuti mtengo wozunzikirapo* wa Khristu ungakhale wopanda ntchito.
18 Nkhani yokhudza mtengo wozunzikirapowo* ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akupita kukawonongedwa,+ koma kwa ife amene tikupulumutsidwa, imeneyi ndi mphamvu ya Mulungu.+
19 Chifukwa Malemba amati: “Ndidzathetsa nzeru za anthu anzeru ndipo ndidzakana* kuchenjera kwa anthu anzeru.”+
20 Kodi wanzeru ali kuti? Mlembi* ali kuti? Katswiri wa mtsutso wa nthawi* ino ali kuti? Kodi Mulungu sanapange nzeru zadzikoli kukhala zopusa?
21 Mwa nzeru zake, Mulungu sanalole kuti dziko ligwiritse ntchito nzeru zake+ pomudziwa.+ Mʼmalomwake, Mulungu anaona kuti ndi bwino kupulumutsa okhulupirira kudzera mu uthenga umene anthu ena amauona kuti ndi wopusa.+
22 Ayuda amafuna kuona zizindikiro+ ndipo Agiriki amafunafuna nzeru.
23 Koma ife timalalikira za Khristu amene anaphedwa popachikidwa pamtengo wozunzikirapo.* Ayuda amaona kuti zimenezi nʼzokhumudwitsa ndipo anthu a mitundu ina amaona kuti nʼzopusa.+
24 Ngakhale zili choncho, Ayuda ndi Agiriki amene anaitanidwa amaona kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru za Mulungu.+
25 Chifukwa chinthu cha Mulungu chimene anthu amachiona kuti nʼchopusa, nʼchanzeru kuposa anthu. Ndipo chinthu cha Mulungu chimene anthu amachiona kuti nʼchofooka, nʼchamphamvu kuposa anthu.+
26 Mukuona mmene anakuitanirani abale, kuti si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru+ omwe anaitanidwa, si ambiri amphamvu amene anaitanidwa, si ambiri a mʼmabanja olemekezeka.+
27 Koma Mulungu anasankha zopusa za dziko kuti achititse manyazi anthu anzeru, ndipo Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko kuti achititse manyazi zinthu zamphamvu.+
28 Mulungu anasankhanso zinthu zonyozeka za dziko ndi zinthu zimene anthu amaziona ngati zachabechabe, zinthu zimene palibe, kuti achititse zinthu zimene zilipo kukhala zopanda mphamvu.+
29 Anachita zimenezi kuti pasapezeke munthu wodzitama pamaso pa Mulungu.
30 Koma inu ndinu ogwirizana ndi Khristu Yesu chifukwa cha Mulunguyo. Yesuyo amatisonyeza nzeru za Mulungu ndiponso chilungamo cha Mulungu.+ Kudzera mwa Yesu, anthu akhoza kuyeretsedwa,+ ndipo kudzera mwa dipo* akhoza kumasulidwa,+
31 kuti zigwirizane ndi zimene Malemba amanena zoti: “Amene akudzitama, adzitame mwa Yehova.”*+
Mawu a M'munsi
^ Amatchedwanso Petulo.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “polankhula mochenjera.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “ndidzakankhira pambali.”
^ Kutanthauza katswiri wa Chilamulo.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Zakumapeto A5.