Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto 6:1-18

  • Osagwiritsa ntchito molakwa kukoma mtima kwa Mulungu (1, 2)

  • Utumiki wa Paulo (3-13)

  • Musamangidwe mʼgoli ndi osakhulupirira (14-18)

6  Pamene tikugwira naye ntchito limodzi,+ tikukulimbikitsani kuti musalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu nʼkuphonya cholinga cha kukoma mtimako.+ 2  Chifukwa iye anati: “Pa nthawi yovomerezedwa ndinakumvera, ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza.”+ Ndithudi, inoyo ndi nthawi yeniyeni yovomerezedwa. Lero ndi tsiku lachipulumutso. 3  Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa, kuti anthu asapezere chifukwa utumiki wathu.+ 4  Koma tikusonyeza mʼnjira iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.+ Tikuchita zimenezi popirira zinthu zambiri, pokumana ndi mavuto, pokhala opanda zinthu zofunika, pokumana ndi zinthu zovuta,+ 5  pomenyedwa, kuikidwa mʼndende,+ zipolowe, pogwira ntchito mwakhama, kusagona tulo ndiponso kukhala osadya.+ 6  Tikusonyezanso zimenezi pokhala oyera, odziwa zinthu, oleza mtima,+ okoma mtima,+ potsogoleredwa ndi mzimu woyera, posonyeza chikondi chopanda chinyengo,+ 7  polankhula zoona ndiponso pokhala ndi mphamvu ya Mulungu.+ Komanso tikuchita zimenezi ponyamula zida za chilungamo+ kudzanja lamanja* ndi lamanzere,* 8  popatsidwa ulemerero ndi kunyozedwa ndiponso poneneredwa zoipa ndi zabwino. Tikuonedwa ngati achinyengo koma ndife oona mtima, 9  ngati osadziwika koma ndife odziwika bwino, ngati oti tikufa* koma tikukhalabe ndi moyo,+ ngati olangidwa koma osaperekedwa kuti tikaphedwe,+ 10  ngati achisoni koma osangalala nthawi zonse, ngati osauka koma olemeretsa anthu ambiri komanso ngati opanda chilichonse koma okhala ndi zinthu zonse.+ 11  Takhala tikulankhula nanu inu Akorinto, ife tatsegula kwambiri* mtima wathu. 12  Ife sitikuumira pa nkhani yokusonyezani chikondi,+ koma inuyo ndi amene mukutikonda moumira. 13  Choncho ndikulankhula nanu ngati ana anga, inunso muzichita zomwezo, tsegulani kwambiri* mitima yanu.+ 14  Musamangidwe mʼgoli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana.+ Pali mgwirizano wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo?+ Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?+ 15  Ndiponso pali mgwirizano wotani pakati pa Khristu ndi Beliyali?*+ Nanga munthu wokhulupirira* ndi wosakhulupirira angafanane pa zinthu ziti?+ 16  Ndipo pali kugwirizana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?+ Chifukwa ifeyo ndife kachisi wa Mulungu wamoyo,+ ngati mmene Mulungu ananenera kuti: “Ndidzakhala pakati pawo+ ndiponso ndidzayenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga.”+ 17  “‘Choncho chokani pakati pawo ndipo musiyane nawo,’ watero Yehova.* ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa,’”+ “‘ndipo ndidzakulandirani.’”+ 18  “‘Ndidzakhala bambo anu+ ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,’+ watero Yehova* Wamphamvuyonse.”

Mawu a M'munsi

Mwina zogwiritsa ntchito polimbana ndi mdani.
Mwina zodzitetezera.
Kapena kuti, “oonedwa ngati oyenera kufa.”
Kapena kuti, “ife tafutukula.”
Kapena kuti, “futukulani.”
Kuchokera ku mawu a Chiheberi otanthauza, “Wopanda Pake,” ndipo akunena za Satana.
Kapena kuti, “wokhulupirika.”