Amosi 3:1-15
3 “Tamverani mawu amene Yehova wanena okhudza inu Aisiraeli, mawu okhudza banja lonse limene ndinalitulutsa mʼdziko la Iguputo:
2 ‘Pa mabanja onse apadziko lapansi, ine ndimadziwa inu nokha.+
Choncho ndidzakulangani chifukwa cha zolakwa zanu zonse.+
3 Kodi anthu awiri amayenda pamodzi asanapangane kuti akumane?
4 Kodi mkango umabangula munkhalango usanagwire nyama?
Kodi mkango wamphamvu umalira mʼmalo amene umakhala usanagwire kalikonse?
5 Kodi mbalame imakodwa pamsampha, pamene palibe msampha?*
Kodi msampha umafwamphuka usanagwire kalikonse?
6 Lipenga la nyanga ya nkhosa likalira mumzinda, kodi anthu sanjenjemera?
Kodi tsoka likagwa mumzinda, si Yehova amene wachititsa?
7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, sangachite kalikonseAsanaulule chinsinsi chake kwa atumiki ake, aneneri.+
8 Mkango wabangula!+ Ndani sakuchita mantha?
Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa walankhula! Ndani sanenera?’+
9 ‘Lengezani izi pansanja zolimba za ku Asidodi,Ndiponso pansanja zolimba zamʼdziko la Iguputo.
Munene kuti: “Sonkhanani kuti muukire mapiri a ku Samariya.+Onani chisokonezo chimene chikuchitika mumzindawu,Komanso zachinyengo zimene zikuchitika mumzinda umenewo.+
10 Chifukwa sadziwa kuchita zolungama,” watero Yehova,“Iwo asonkhanitsa chiwawa ndi chiwonongeko munsanja zawo zolimba.”’
11 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti,‘Mdani adzazungulira dziko lonse,+Ameneyo adzakufoola,Ndipo adzatenga zinthu munsanja zako zolimba.’+
12 Yehova wanena kuti,‘Ngati mmene mʼbusa amapulumutsira miyendo iwiri ya chiweto kapena kachidutswa ka khutu mʼkamwa mwa mkango,Ndi mmenenso adzapulumukire Aisiraeli,Amene akukhala pamipando yapamwamba* ndiponso kugona pamabedi okongola ku Samariya.’+
13 ‘Tamverani ndipo muchenjeze* nyumba ya Yakobo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, Mulungu wa magulu a nkhondo akumwamba.
14 ‘Pa tsiku limene ndidzalanga Aisiraeli chifukwa chondigalukira,+Ndidzalanganso maguwa ansembe a ku Beteli.+Nyanga za guwa lansembe zidzadulidwa nʼkugwa pansi.+
15 Ndidzagwetsa nyumba yokhalamo nthawi yozizira ndiponso nyumba yokhalamo nthawi yotentha.’
‘Nyumba zaminyanga ya njovu zidzagwa.+Ndipo nyumba zikuluzikulu* zidzawonongedwa,’+ watero Yehova.”
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “nyambo.”
^ Kapena kuti, “pamipando yokhala ngati bedi ya ku Damasiko.”
^ Kapena kuti, “muchitire umboni wotsutsa.”
^ Mabaibulo ena amati, “zambiri.”