Machitidwe a Atumwi 2:1-47
2 Tsopano onse anali atasonkhana pamodzi pa tsiku la Chikondwerero cha Pentekosite.+
2 Mwadzidzidzi, kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo phokoso lake linadzaza mʼnyumba yonse imene iwo anali.+
3 Kenako anaona malilime ooneka ngati malawi amoto, ndipo anagawanika nʼkukhala pa aliyense wa iwo limodzilimodzi.
4 Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana,* mogwirizana ndi mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.+
5 Pa nthawi imeneyo, Ayuda oopa Mulungu ochokera mʼmitundu yonse yapadziko lapansi ankakhala ku Yerusalemu.+
6 Choncho mkokomowu utamveka, panasonkhana gulu lalikulu la anthu. Iwo anadabwa kwambiri, chifukwa aliyense anawamva akulankhula mʼchilankhulo chake.
7 Zimenezi zinawadabwitsa kwambiri moti anayamba kufunsana kuti: “Anthuni, kodi onse akulankhulawa si anthu a ku Galileya?+
8 Ndiye zikutheka bwanji kuti aliyense pagulu lathuli akumva chilankhulo chake?
9 Pano pali Apati, Amedi+ ndi Aelamu.+ Palinso anthu ochokera ku Mesopotamiya, ku Yudeya, ku Kapadokiya, ku Ponto ndi kuchigawo cha Asia.+
10 Pali anthu ochokera ku Fulugiya, ku Pamfuliya, ku Iguputo ndi kumadera a Libiya amene ali pafupi ndi Kurene. Palinso alendo ochokera ku Roma, omwe ndi Ayuda ndiponso anthu amene analowa Chiyuda.+
11 Komanso pali Akerete ndi Aluya. Tonsefe tikuwamva akulankhula zinthu zazikulu za Mulungu mʼzilankhulo zathu.”
12 Onse anadabwa kwambiri ndipo anathedwa nzeru moti ankafunsana kuti: “Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?”
13 Koma ena ankawaseka nʼkumanena kuti: “Aledzera vinyo watsopano amenewa.”
14 Koma Petulo anaimirira pamodzi ndi atumwi 11 aja.+ Iye analankhula nawo mokweza mawu kuti: “Inu anthu a ku Yudeya ndi inu nonse a mu Yerusalemu, dziwani izi ndipo mvetserani mosamala zimene ndikufuna kukuuzani.
15 Sikuti anthuwa aledzera ngati mmene inu mukuganizira, chifukwa nthawi panopa ndi 9 koloko mʼmawa.*
16 Koma zimene zikuchitikazi ndi zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yoweli kuti:
17 ‘“Ndipo mʼmasiku otsiriza,” akutero Mulungu, “ndidzapereka* mzimu wanga kwa chamoyo chilichonse, ndipo ana anu aamuna ndi aakazi adzalosera. Anyamata adzaona masomphenya ndipo amuna achikulire adzalota maloto.+
18 Ngakhale akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndidzawapatsa mzimu wanga mʼmasiku amenewo ndipo iwo adzanenera.+
19 Ndidzachita zodabwitsa kumwamba ndiponso zizindikiro padziko lapansi. Padzakhala magazi, moto ndi utsi wokwera mʼmwamba.
20 Dzuwa lidzasanduka mdima ndipo mwezi udzasanduka magazi. Zimenezi zidzachitika tsiku lalikulu ndiponso laulemerero la Yehova* lisanafike.
21 Ndipo aliyense woitana pa dzina la Yehova* adzapulumuka.”’+
22 Amuna inu a mu Isiraeli, imvani mawu awa: Yesu wa ku Nazareti ndi munthu amene Mulungu anakuonetsani poyera. Anatero kudzera muntchito zamphamvu, zodabwitsa komanso zizindikiro, zimene Mulungu anachita pakati panu kudzera mwa iye,+ ngati mmene inunso mukudziwira.
23 Munthu ameneyu, amene anaperekedwa mwa kufuna kwa Mulungu+ ndi kudziwiratu kwake zamʼtsogolo, munachititsa kuti aphedwe pokhomeredwa pamtengo ndi anthu osamvera malamulo.+
24 Koma Mulungu anamuukitsa+ pomumasula ku zopweteka* za imfa, chifukwa zinali zosatheka kuti imfa imugwire mwamphamvu.+
25 Paja Davide ananena za iyeyu kuti, ‘Ndimaika Yehova* patsogolo panga nthawi zonse. Chifukwa iye ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
26 Pa chifukwa chimenechi mtima wanga unasangalala ndipo ndinalankhula mosangalala kwambiri. Komanso ine ndidzakhala ndi chiyembekezo,
27 chifukwa simudzandisiya* mʼManda,* ndipo simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.*+
28 Mwandidziwitsa njira za moyo, ndipo mudzachititsa kuti ndizisangalala kwambiri ndikakhala nanu pafupi.’*+
29 Abale anga, ndilankhula ndithu momasuka za kholo lathu Davide. Iye anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda,+ ndipo manda ake tili nawo mpaka lero.
30 Iye anali mneneri ndipo ankadziwa kuti Mulungu anamulonjeza polumbira, kuti pampando wake wachifumu adzakhazikapo mmodzi wa mbadwa zake.+
31 Iye anadziwiratu zamʼtsogolo ndipo ananeneratu za kuuka kwa Khristu kuti sanasiyidwe mʼManda,* komanso thupi lake silinavunde.+
32 Yesu ameneyo Mulungu anamuukitsa, ndipo tonsefe ndife mboni za nkhani imeneyi.+
33 Iye anakwezedwa nʼkukhala kudzanja lamanja la Mulungu+ ndipo analandira mzimu woyera wolonjezedwawo kuchokera kwa Atate.+ Choncho iye watipatsa* mzimu woyera umene mukuuona ndi kuumvawu.
34 Ndipotu Davide sanapite kumwamba, koma iyeyo anati, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja
35 mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”’+
36 Choncho nyumba yonse ya Isiraeli idziwe ndithu kuti Yesu ameneyu, amene inu munamuphera pamtengo,+ Mulungu anamuika kukhala Ambuye+ ndi Khristu.”
37 Iwo atamva mawu amenewa, anavutika kwambiri mumtima ndipo anafunsa Petulo ndi atumwi enawo kuti: “Abale athu, tichite chiyani pamenepa?”
38 Petulo anawayankha kuti: “Lapani,+ ndipo aliyense abatizidwe+ mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe.+ Mukatero mudzalandira mphatso yaulere ya mzimu woyera.
39 Chifukwa lonjezoli+ laperekedwa kwa inu, kwa ana anu ndiponso kwa anthu onse akutali, onse amene Yehova* Mulungu wathu angawasankhe.”+
40 Ndipo ndi mawu enanso ambiri, Petulo anachitira umboni mokwanira. Komanso sanaleke kuwadandaulira kuti: “Dzipulumutseni ku mʼbadwo wa maganizo olakwikawu.”+
41 Choncho amene analandira mawu akewo mosangalala anabatizidwa,+ moti tsiku limenelo chiwerengero cha ophunzirawo chinawonjezereka ndi anthu pafupifupi 3,000.+
42 Choncho iwo anapitiriza kutsatira zimene atumwiwo ankaphunzitsa, kucheza,* kudyera limodzi+ komanso kupemphera.+
43 Anthu onse anayamba kuchita mantha kwambiri ndipo atumwiwo anayamba kuchita zinthu zodabwitsa ndiponso zizindikiro zambiri.+
44 Onse amene anakhala okhulupirira ankakhala limodzi ndipo ankagawana zinthu zonse zimene anali nazo.
45 Ankagulitsa malo awo ndi zinthu zina zimene anali nazo+ nʼkugawa kwa onse zimene apeza, mogwirizana ndi zimene aliyense akufunikira.+
46 Tsiku lililonse ankasonkhana mʼkachisi mogwirizana. Ankaitanirana chakudya mʼnyumba zawo ndiponso ankagawana zakudya mosangalala komanso ndi mtima wonse.
47 Ankatamanda Mulungu ndiponso ankakondedwa ndi anthu onse. Komanso tsiku lililonse, Yehova* anapitiriza kuwonjezera anthu amene ankawapulumutsa.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “kulankhula malilime.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera 6 koloko mʼmawa.
^ Kapena kuti, “ndidzatsanulira.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Mabaibulo ena amati, “zingwe.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “simudzasiya moyo wanga.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “liwole.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndikakhala pafupi ndi nkhope yanu.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “watitsanulira.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “kugawana zinthu.”
^ Onani Zakumapeto A5.