Salimo 112:1-10

  • Munthu wolungama amaopa Yehova

    • “Munthu amene amakongoza ena mosaumira, zinthu zimamuyendera bwino” (5)

    • “Wolungama adzakumbukiridwa mpaka kalekale” (6)

    • Wowolowa manja amathandiza anthu osauka (9)

112  Tamandani Ya!*+ א [Aleph] Wosangalala ndi munthu amene amaopa Yehova,+ב [Beth]Amene amasangalala kwambiri ndi malamulo ake.+ ג [Gimel]  2  Mbadwa zake zidzakhala zamphamvu padziko lapansi,ד [Daleth]Ndipo mʼbadwo wa anthu olungama udzadalitsidwa.+ ה [He]  3  Zinthu zamtengo wapatali ndiponso chuma zili mʼnyumba yake,ו [Waw]Ndipo chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya. ז [Zayin]  4  Kwa anthu owongoka mtima iye amawala ngati kuwala kumene kumaunika mumdima.+ ח [Heth] Iye ndi wokoma mtima,* wachifundo+ komanso wolungama. ט [Teth]  5  Munthu amene amakongoza ena mosaumira, zinthu zimamuyendera bwino.+ י [Yod] Iye amachita zinthu mwachilungamo. כ [Kaph]  6  Sadzagwedezeka ngakhale pangʼono.+ ל [Lamed] Wolungama adzakumbukiridwa mpaka kalekale.+ מ [Mem]  7  Sadzaopa uthenga woipa.+ נ [Nun] Mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.+ ס [Samekh]  8  Mtima wake sukugwedezeka* ndipo sakuchita mantha,+ע [Ayin]Pamapeto pake adzayangʼana adani ake, adaniwo atagonjetsedwa.+ פ [Pe]  9  Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu osauka.+ צ [Tsade] Chilungamo chake chidzakhalapo mpaka kalekale.+ ק [Qoph] Mphamvu zake zidzawonjezeka* chifukwa cha ulemerero. ר [Resh] 10  Woipa adzaona zimenezi ndipo adzakhumudwa. ש [Shin] Adzakukuta mano ndi kusungunuka. ת [Taw] Zimene anthu oipa amalakalaka sizidzachitika.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “wachisomo.”
Kapena kuti, “ndi wokhazikika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nyanga yake idzawonjezeka.”