Salimo 115:1-18
115 Ife sitikuyenera, inu Yehova, ife sitikuyenera,Koma ulemerero ukuyenera kupita ku dzina lanu+Chifukwa cha kukhulupirika kwanu komanso chikondi chanu chokhulupirika.+
2 Musalole kuti anthu a mitundu ina azinena kuti:
“Mulungu wawo ali kuti?”+
3 Mulungu wathu ali kumwamba.Iye amachita chilichonse chimene chamusangalatsa.
4 Mafano awo ndi opangidwa ndi siliva komanso golide,Ntchito ya manja a anthu.+
5 Pakamwa ali napo koma sangalankhule.+Maso ali nawo koma sangaone.
6 Makutu ali nawo koma sangamve.Mphuno ali nayo koma sanganunkhize.
7 Manja ali nawo koma sakhudza kanthu.Mapazi ali nawo koma sangayende.+Satulutsa mawu ndi mmero wawo.+
8 Anthu amene amawapanga adzafanana nawo,+Chimodzimodzinso anthu onse amene amakhulupirira mafanowo.+
9 Aisiraeli inu, khulupirirani Yehova,+Iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu.+
10 Inu nyumba ya Aroni,+ khulupirirani Yehova,Iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu.
11 Inu amene mumaopa Yehova, khulupirirani Yehova,+Iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu.+
12 Yehova akutikumbukira ndipo adzatidalitsa.Adzadalitsa nyumba ya Isiraeli.+Adzadalitsa nyumba ya Aroni.
13 Yehova adzadalitsa anthu onse amene amamuopa,Aangʼono ndi aakulu omwe.
14 Yehova adzakuchulukitsani,Inuyo komanso ana anu.*+
15 Yehova akudalitseni,+Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.+
16 Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova,+Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.+
17 Akufa satamanda Ya,+Ngakhalenso aliyense amene amatsikira kulichete.+
18 Koma ife tidzatamanda YaKuyambira panopa mpaka kalekale.
Tamandani Ya!*
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ana anu aamuna.”
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.