Salimo 33:1-22
33 Fuulani mosangalala chifukwa cha Yehova,+ olungama inu.
Mʼpoyenera kuti olungama atamande Mulungu.
2 Yamikani Yehova poimba zeze.Muimbireni nyimbo zomutamanda ndi choimbira cha zingwe 10.
3 Muimbireni nyimbo yatsopano.+Imbani mwaluso choimbira cha zingwe ndipo muzifuula mosangalala.
4 Chifukwa mawu a Yehova ndi oona,+Ndipo chilichonse chimene amachita ndi chodalirika.
5 Iye amakonda chilungamo ndipo amaweruza mosakondera.+
Dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chokhulupirika cha Yehova.+
6 Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova,+Ndipo analenga zinthu zonse zakumwamba* ndi mpweya wamʼkamwa mwake.
7 Amasonkhanitsa madzi amʼnyanja ngati damu,+Amaika madzi amphamvu mʼnyumba zosungiramo zinthu.
8 Dziko lonse lapansi liope Yehova.+
Anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi achite naye mantha.
9 Chifukwa iye analankhula ndipo zinachitika.+Iye analamula ndipo zinakhalapo.+
10 Yehova wasokoneza zolinga za mitundu ya anthu.+Walepheretsa mapulani* a mitundu ya anthu.+
11 Koma zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale.+Maganizo amumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo.
12 Wosangalala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova,+Anthu amene iye wawasankha kuti akhale cholowa chake.+
13 Yehova amayangʼana padziko lapansi, kuchokera kumwamba.Iye amaona ana onse a anthu.+
14 Kuchokera kumalo amene amakhala,Amayangʼanitsitsa anthu amene akukhala padziko lapansi.
15 Iye ndi amene amaumba mitima ya anthu onse,Ndipo amafufuza ntchito zawo zonse.+
16 Palibe mfumu imene inapulumuka chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo.+Munthu wamphamvu sapulumuka chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+
17 Si nzeru kudalira hatchi chifukwa singapulumutse munthu,+Mphamvu zake zochuluka sizingapulumutse munthu
18 Taonani! Diso la Yehova limayangʼana anthu amene amamuopa,+Amene amayembekezera chikondi chake chokhulupirika,
19 Kuti awapulumutse ku imfa,Komanso kuwathandiza kuti akhale ndi moyo pa nthawi ya njala.+
20 Tikuyembekezera Yehova.
Iye ndi amene amatithandiza komanso ndi chishango chathu.+
21 Mulungu amachititsa kuti mitima yathu isangalale,Chifukwa timadalira dzina lake loyera.+
22 Inu Yehova, chikondi chanu chokhulupirika chikhale pa ife,+Pamene tikupitiriza kuyembekezera inu.+