Wolembedwa ndi Mateyu 19:1-30
19 Yesu atamaliza kulankhula zinthu zimenezi, anachoka ku Galileya nʼkupita kumalire a Yudeya kutsidya lina la Yorodano.+
2 Gulu lalikulu la anthu linamutsatira kumeneko ndipo iye anawachiritsa.
3 Ndiyeno Afarisi anabwera kwa iye nʼcholinga chodzamuyesa ndipo anamufunsa kuti: “Kodi mwamuna ali ndi ufulu wothetsa banja ndi mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”+
4 Yesu anayankha kuti: “Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pachiyambi anawalenga mwamuna ndi mkazi+
5 nʼkunena kuti: ‘Chifukwa cha zimenezi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake nʼkudziphatika kwa mkazi wake ndipo awiriwo adzakhala thupi limodziʼ?+
6 Moti sakhalanso kuti ndi awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi,* munthu asachilekanitse.”+
7 Iwo anamufunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipereka kalata yothetsera ukwati kwa mkazi nʼkumusiya?”+
8 Iye anawayankha kuti: “Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuti muzithetsa ukwati,+ koma kuyambira pachiyambi sizinali choncho.+
9 Ine ndikukuuzani kuti aliyense amene wasiya mkazi wake nʼkukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha chiwerewere.”*+
10 Kenako ophunzira ake ananena kuti: “Ngati zili choncho kwa munthu ndi mkazi wake, ndiyetu ndi bwino osakwatira.”
11 Iye anawauza kuti: “Si onse amene angathe kuchita zimenezi, koma okhawo amene ali ndi mphatso.+
12 Chifukwa ena sakwatira chifukwa chakuti anabadwa choncho ndipo ena chifukwa chakuti anafulidwa ndi anthu. Koma pali ena amene safuna kukwatira chifukwa cha Ufumu wakumwamba. Amene angathe kuchita zimenezi achite.”+
13 Kenako anthu anamubweretsera ana aangʼono kuti awaike manja nʼkuwapempherera, koma ophunzirawo anawakalipira.+
14 Koma Yesu anawauza kuti: “Asiyeni anawo ndipo musawaletse kuti abwere kwa ine, chifukwa Ufumu wakumwamba ndi wa anthu ngati amenewa.”+
15 Ndiyeno anaika manja ake pa anawo kenako anachoka kumeneko.
16 Tsopano munthu wina anabwera kwa iye nʼkumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene ndikuyenera kuchita kuti ndikapeze moyo wosatha?”+
17 Iye anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukundifunsa zokhudza zinthu zabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino.+ Choncho ngati ukufuna kukapeza moyo, uzisunga malamulo nthawi zonse.”+
18 Iye anafunsa kuti: “Malamulo ake ati?” Yesu anayankha kuti: “Musaphe munthu,*+ musachite chigololo,+ musabe,+ musapereke umboni wabodza.+
19 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu,+ komanso lakuti, Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+
20 Mnyamatayo anayankha Yesu kuti: “Ndakhala ndikutsatira zonsezi, nʼchiyaninso china chimene ndikuyenera kuchita?”
21 Yesu anamuuza kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwiro,* pita ukagulitse katundu wako yense ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba,+ ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+
22 Mnyamatayo atamva zimenezi anachoka ali ndi chisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.+
23 Ndiyeno Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndithu ndikukuuzani, zidzakhala zovuta kuti munthu wolemera adzalowe mu Ufumu wakumwamba.+
24 Ndiponso ndikukuuzani kuti, nʼzosavuta kuti ngamila ilowe pakabowo ka singano kusiyana nʼkuti munthu wolemera alowe mu Ufumu wa Mulungu.”+
25 Ophunzirawo atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anafunsa kuti: “Ndiye angapulumuke ndi ndani?”+
26 Yesu anawayangʼanitsitsa nʼkuwauza kuti: “Kwa anthu zimenezi nʼzosatheka, koma zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu.”+
27 Kenako Petulo ananena kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse nʼkukutsatirani, ndiye kodi tidzapeza chiyani?”+
28 Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, pa nthawi ya kulenganso zinthu, Mwana wa munthu adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero, inu amene mwakhala mukunditsatira mudzakhalanso mʼmipando yachifumu 12, nʼkumaweruza mafuko 12 a Isiraeli.+
29 Aliyense amene wasiya nyumba, azichimwene, azichemwali, abambo, amayi, ana kapena minda chifukwa cha dzina langa adzalandira zochuluka kuwirikiza maulendo 100 kuposa zimenezi ndiponso adzapeza moyo wosatha.+
30 Koma ambiri amene ali oyamba adzakhala omaliza ndipo omaliza adzakhala oyamba.”+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wachimanga mugoli limodzi.”
^ MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.
^ Kapena kuti, “kukhala wokwanira pamaso pa Mulungu.”