Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

6

Ndingatani Kuti Ndisamangotengera Zochita za Anzanga?

Ndingatani Kuti Ndisamangotengera Zochita za Anzanga?

KODI YANKHO LA FUNSOLI LINGAKUTHANDIZENI BWANJI?

Yankho la funsoli lingakuthandizeni kuti muzidziwa zoyenera kuchita m’malo momangotsatira zimene ena akuchita.

KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

Tiyerekezere kuti mnyamata wina dzina lake, Brian waona anyamata awiri a m’kalasi mwake akubwera. Nthawi yomweyo wayamba kutuluka tsembwe chifukwa cha mantha. Anyamatawa anamukakamizapo kawiri konse kuti asute fodya. Choncho akudziwiratu kuti akangokumana nawo, nkhani yake ikhalanso yomweyo.

Mnyamata woyamba akuti:

“Uli wekhanso lero? Ndakupezera mnzako woti uzicheza naye.”

Kenako akupisa m’thumba n’kutulutsa chinthu chinachake.

Brian akuona kuti ndi ndudu ya fodya ndipo zikungopangitsa kuti mantha ake aja awonjezeke.

Brian akunena kuti: “Ine zimenezo ayi. Paja ndinakuuzani kale kuti sindi . . . ”

Koma mnyamata wachiwiri akumudula n’kunena kuti: “Iwe mantha ngati khwangwala bwanji?”

Brian akuyesetsa kuyankha molimba mtima kuti: “Ayi, si ine khwangwala.”

Mnyamata wachiwiri akukoleka dzanja lake m’khosi mwa Brian n’kunena kuti: “Talandira aise.”

Mnyamata woyamba akuyandikizitsa ndudu pakamwa pa Brian ndipo monong’ona akumuuza kuti: “Sitiuza aliyense.”

Ndiye kodi inuyo mukanakhala Brian mukanatani?

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA

Kodi anyamatawa akudziwa zimene akuchita? Nanga anasankha okha kuti azisuta fodya? N’zokayikitsa. N’kutheka kuti anayamba kusuta chifukwa chongotengera zochita za anzawo n’cholinga choti anzawowo asamawasale.

Ndiye kodi inuyo mungatani kuti musayambe kusuta chifukwa chongotengera anzanu? Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni.

  1. MUZIDZIWIRATU ZIMENE ZINGACHITIKE

    Baibulo limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”—Miyambo 22:3.

    Nthawi zambiri mungathe kudziwiratu zimene anzanu angakuumirizeni kuchita. Mwachitsanzo, mungaone anzanu a kusukulu akubwera poteropo uku akusuta fodya. Mukhoza kudziwiratu kuti mukakumana akukakamizani kusuta. Ndiye mutakonzekereratu, sizingakuvuteni kukana.

  2. MUZIGANIZA MUSANASANKHE ZOCHITA

    Baibulo limati: “Khalani ndi chikumbumtima chabwino.”—1 Petulo 3:16.

    Mungadzifunse kuti, ‘Ndikachita zimene anzangawa akufuna, kodi ndimva bwanji?’ N’zoona kuti anzanuwo angakukondeni. Koma kodi mudzamva bwanji mukakhala ndi makolo anu kapena Akhristu anzanu? Nanga kodi mungakonde kusangalatsa anzanu a kusukulu m’malo mosangalatsa Mulungu?—Ekisodo 23:2.

  3. MUZISANKHA ZOCHITA MWANZERU

    Baibulo limati: “Munthu wanzeru amachita mantha ndipo amapatuka pa choipa.”—Miyambo 14:16.

    Aliyense angasankhe kukhala wokhulupirika n’kupeza madalitso kapena kukhala wosakhulupirika n’kukumana ndi mavuto. Anthu monga Yosefe, Yobu ndi Yesu anasankha mwanzeru pomwe Kaini, Esau ndi Yudasi sanasankhe bwino. Kodi inuyo mungafune kufanana ndi ndani?

Baibulo limati: “Khala wokhulupirika.” (Salimo 37:3) Ngati mwaganizira kale kuipa kwa zimene anzanu akufuna muchite ndipo mwasankha kale zochita, simungavutike kunena maganizo anu.

Sikuti mungafunike kulankhula zambirimbiri. Kungonena mwamphamvu kuti AYI n’kokwanira. Kapena mukhoza kungonena mawu osonyeza kuti simusintha maganizo, kuti:

  • “Zimenezo zisandikhudze.”

  • “Sindingachite zimenezo.”

  • “Inunso mumadziwa bwino kuti sindingasute.”

Chofunika n’kuyankha nthawi yomweyo ndiponso molimba mtima. Mukatero anzanuwo angasiye kukuvutitsani.

ZIMENE MUNGACHITE ANZANU AKAMAKUNYOZANI

Mukamangololera kuchita zimene anzanu akufuna, mumakhala ngati kachidole kawo

Bwanji ngati anzanu atamakunyozani kuti, “Ndiwe wamantha eti?” Anganene zimenezi pofuna kuti muchite zimene akufuna. Koma kodi mungawayankhe bwanji? Pali njira ziwiri.

  • Mukhoza kungovomereza zimene akunenazo. (“Simukunama, ndinedi wamantha.” Kenako fotokozani mwachidule chifukwa chimene mukuchitira mantha.)

  • Nanunso mutha kuwapanikiza. Fotokozani chifukwa chimene mukukanira, ndipo asonyezeni kuti zimene akuchitazo n’zopanda nzeru. (“Ndimakuonanitu ngati anthu ozindikira oti simungasute fodya.”)

Anzanuwo akapitiriza kukuvutitsani, mungochokapo chifukwa mukakhalabe pomwepo zinthu zikhoza kuipa kwambiri. Dziwani kuti mukachokapo, sikuti mwagonja chifukwa simunalole kuchita zimene iwo akufuna.

Kunena zoona n’zosatheka kupeweratu kuvutitsidwa. Komabe mutha kusankha zimene mungachite. Muthanso kunena maganizo anu kapena kuchita zilizonse zimene mungathe kuti anzanu asamakuvutitseni. Ndipo dziwani kuti ndi udindo wanu kusankha zochita.—Yoswa 24:15.