MUTU 8
Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
-
Kodi Baibulo limatiuza chiyani za Ufumu wa Mulungu?
-
Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani?
-
Kodi Ufumuwo udzakwaniritsa liti chifuniro cha Mulungu padziko lapansi?
1. Kodi tikambirana zokhudza pemphero liti?
ANTHU ambiri padziko lonse amalidziwa bwino pemphero limene ambiri amati ndi Pemphero la Atate Wathu, kapena Pemphero la Ambuye. Mayina onsewa amanena za pemphero lodziwika kwambiri limene Yesu Khristu anauza ophunzira ake ngati chitsanzo. Pempheroli lili ndi mfundo zofunika kwambiri ndipo tiyeni tikambirane mfundo zitatu zoyambirira. Kukambirana mfundo zotchulidwa mu pempheroli kungakuthandizeni kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa.
2. Kodi Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azipempherera zinthu zitatu ziti?
2 Poyamba pemphero lachitsanzoli, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.’” (Mateyu 6:9-13) Kodi mfundo zitatu za m’pempheroli n’zofunika bwanji?
3. Kodi tiyenera kudziwa chiyani za Ufumu wa Mulungu?
3 Tinaphunzira kale zambiri zokhudza dzina la Mulungu lakuti Yehova. Tinakambirananso zina ndi zina zokhudza cholinga cha Mulungu. Mwachitsanzo, tinakambirana zimene wachitira anthu komanso zimene adzawachitire m’tsogolo. Koma kodi Yesu ankanena za Ufumu uti pamene ankati tizipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere”? Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Kodi ukadzabwera udzayeretsa bwanji dzina la Mulungu? Komanso
kodi kubwera kwa Ufumuwo kukugwirizana bwanji ndi kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu?KODI UFUMU WA MULUNGU N’CHIYANI?
4. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, nanga Mfumu yake ndi ndani?
4 Ufumu wa Mulungu ndi boma lokhazikitsidwa ndi Yehova Mulungu ndipo Mfumu yake ndi yosankhidwa ndi Mulunguyo. Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndi ndani? Ndi Yesu Khristu. Yesu monga Mfumu, ndi wamphamvu kuposa mafumu onse a padziko lapansi ndipo amatchedwa “Mfumu ya olamulira monga mafumu ndi Mbuye wa olamulira monga ambuye.” (1 Timoteyo 6:15) Iye ali ndi mphamvu zoti angathe kutichitira zinthu zonse zimene timafunikira zomwe wolamulira aliyense sangakwanitse.
5. Kodi likulu la Ufumu wa Mulungu lili kuti, nanga Ufumuwo udzalamulira chiyani?
5 Kodi likulu la Ufumu wa Mulungu lili kuti? Lili kumene kuli Yesu. Muyenera mukukumbukira zimene munaphunzira zoti Yesu ataphedwa, anaukitsidwa ndipo pasanapite nthawi anabwerera kumwamba. (Machitidwe 2:33) Choncho likulu la Ufumu wa Mulungu lili kumwamba, n’chifukwa chake Baibulo limautchula kuti ndi “Ufumu . . . wakumwamba.” (2 Timoteyo 4:18) Ngakhale kuti Ufumu wa Mulungu uli kumwamba, udzalamulira dziko lapansi.—Werengani Chivumbulutso 11:15.
6, 7. Kodi Yesu akusiyana bwanji ndi mafumu ena?
6 Kodi Yesu akusiyana bwanji ndi mafumu ena? Chifukwa chimodzi n’choti Yesu sadzafa. Poyerekezera Yesu ndi mafumu a padziko lapansi, Baibulo limam’tchula kuti “iye yekha ndiye amene ali ndi moyo wosakhoza kufa, amene amakhala m’kuwala kosafikirika.” (1 Timoteyo 6:16) Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu apitiriza kuchitira anthu zabwino mpaka kalekale. Ndipotu m’tsogolomu adzachita zinthu zabwino zambiri zothandiza anthu ake.
7 Taganizirani ulosi uwu wa m’Baibulo wonena za Yesu: “Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzeru, womvetsa zinthu, wolangiza, wamphamvu, wodziwa zinthu ndi woopa Yehova. Iye adzasangalala ndi kuopa Yehova. Sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena Yesaya 11:2-4) Mawu amenewa akusonyeza kuti Yesu adzakhala Mfumu yachilungamo komanso yachifundo. Kodi simungasangalale kukhala ndi wolamulira ngati ameneyu?
kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi.” (8. Kodi ndi ndani omwe adzalamulire limodzi ndi Yesu?
8 Pali mfundo inanso yochititsa chidwi yokhudza Ufumu wa Mulungu. Mfundo yake ndi yoti Yesu sadzalamulira yekha. Iye adzakhala ndi ena amene adzamuthandize kulamulira. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti: “Tikapitiriza kupirira, tidzalamuliranso limodzi ndi iye monga mafumu.” (2 Timoteyo 2:12) Choncho Paulo, Timoteyo ndi anthu ena okhulupirika amene Mulungu wawasankha adzalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba. Kodi ndi anthu angati amene anapatsidwa mwayi umenewu?
9. Kodi ndi anthu angati amene adzalamulire limodzi ndi Yesu, nanga Mulungu anayamba liti kusankha anthu amenewa?
9 Monga mmene tinaonera m’mutu 7, mtumwi Yohane anaona masomphenya a “Mwanawankhosa ataimirira paphiri la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pawo.” Kodi anthu 144,000 amenewa ndi ndani? Yohane anafotokoza kuti: “Amenewa ndiwo amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita. Iwowa anagulidwa kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyambirira zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 14:1, 4) Anthu amenewa amatsatiradi Yesu Khristu mokhulupirika ndipo anasankhidwa kuti adzalamulire naye kumwamba. Iwo akadzaukitsidwa n’kupita kumwamba, “adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.” (Chivumbulutso 5:10) Kuchokera m’nthawi ya atumwi, Mulungu wakhala akusankha Akhristu okhulupirika kuti akwanitse chiwerengero cha 144,000.
10. N’chifukwa chiyani tingati Mulungu anasonyeza chikondi pokonza zoti Yesu ndi a 144,000 adzalamulire anthu?
10 Zimene Mulungu anakonza zoti Yesu ndi a 144,000 adzalamulire anthu zimasonyeza kuti Mulungu amakonda kwambiri anthu. Yesu ndi wolamulira wabwino chifukwa amadziwa mmene Aheberi 4:15; 5:8) A 144,000 amene adzalamulire naye limodzi nawonso anakumanapo ndi mavuto ali padziko lapansi pano ndipo anapirira. Komanso anakhalapo opanda ungwiro ndipo ankadwala. Choncho akudziwa bwino mavuto amene anthu amakumana nawo.
anthu amaganizira komanso mavuto amene timakumana nawo. Ponena za Yesu, Paulo anati: “Mkulu wa ansembe amene tili naye si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni pa zofooka zathu. Koma tili ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.” (KODI UFUMU WA MULUNGU UDZACHITA ZOTANI?
11. N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti ophunzira ake ayenera kumapemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike kumwamba?
11 Pamene Yesu anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere, anawauzanso kuti azipemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike, “monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” Mulungu ali kumwamba ndipo angelo ake omwe ali kumwambako akhala akuchita chifuniro chake nthawi zonse. Koma m’Mutu 3 tinaphunzira kuti mngelo wina woipa anasiya kuchita chifuniro cha Mulungu ndipo anachititsa kuti Adamu ndi Hava achimwe. M’Mutu 10 tidzaphunzira zinthu zina zimene Baibulo limanena zokhudza mngelo woipa ameneyu, yemwe amadziwika ndi dzina lakuti Satana Mdyerekezi. Satana limodzi ndi angelo ena omwe anayamba kumutsatira, amene amatchulidwa kuti ziwanda, analoledwa kukhalabe kumwambako kwa kanthawi. Choncho tingati pa nthawi imeneyi kumwambako kunali angelo ena omwe sankachita chifuniro cha Mulungu. Koma zimenezi zinali zoti zidzatha Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira. Zinali zoti Yesu Khristu akadzangokhazikitsidwa monga Mfumu, adzamenya nkhondo yolimbana ndi Satana.—Werengani Chivumbulutso 12:7-9.
12. Kodi lemba la Chivumbulutso 12:10 likufotokoza zinthu ziwiri zapadera ziti?
12 Mawu a ulosi otsatirawa akufotokoza zambiri za nkhondoyi: “Ndinamva mawu ofuula kumwamba, akuti: ‘Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamuliro Chivumbulutso 12:10) Kodi mwaona m’vesili zinthu ziwiri zapadera zimene zikuchitika? Choyamba, Yesu Khristu wayamba kulamulira mu Ufumu wa Mulungu. Chachiwiri, Satana waponyedwa padziko lapansi kuchokera kumwamba.
wa Khristu wake zafika, chifukwa woneneza abale athu [Satana] waponyedwa pansi. Iyeyo anali kuwaneneza usana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu.’” (13. Kodi n’chiyani chinachitika Satana atachotsedwa kumwamba?
13 Kodi zotsatira za zinthu ziwiri zinachitikazi zinali zotani? Baibulo limafotokoza zomwe zinachitika kumwamba kuti: “Kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko!” (Chivumbulutso 12:12) Angelo okhulupirika anasangalala chifukwa Satana ndi ziwanda zake atachotsedwa kumwamba, aliyense kumwambako anali wokhulupirika kwa Yehova Mulungu. Panopa chifuniro cha Mulungu chikuchitika kumwamba chifukwa kuli mtendere komanso onse amachita zinthu mogwirizana.
14. Kodi chinachitika n’chiyani Satana ataponyedwa padziko lapansi?
14 Nanga n’chiyani chinachitika padziko lapansi? Baibulo limati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:12) Satana ndi wokwiya kwambiri chifukwa anachotsedwa kumwamba komanso chifukwa choti watsala ndi kanthawi kochepa kuti awonongedwe. Choncho akuchititsa mavuto kapena kuti “tsoka” padziko lapansi. Tidzaphunzira zambiri za “tsoka” limeneli m’mutu wotsatira. Poganizira mavuto amenewa, mwina tingakhale ndi funso lakuti, kodi zingatheke kuti Ufumu wa Mulungu uchititse chifuniro cha Mulungu kuchitika padziko lapansili?
15. Kodi Mulungu ali nalo cholinga chotani dziko lapansili?
15 Kumbukirani zimene Mulungu ankafuna pamene ankalenga dziko lapansi. Tinaphunzira m’mutu 3 kuti zimene Mulungu anachita m’munda wa Edeni, zinasonyeza kuti ankafuna kuti dziko lonse lapansi likhale paradaiso ndipo mukhale anthu olungama mpaka kalekale. Satana anachititsa kuti Adamu ndi Hava achimwe ndipo zimenezi zinasokoneza cholinga cha Mulungu ngakhale kuti cholingacho sichinasinthe. Yehova amafunabe kuti ‘olungama adzalandire dziko lapansi, ndipo adzakhale mmenemo kwamuyaya.’ (Salimo 37:29) Ufumu wa Mulungu ndi umene udzakwaniritse cholinga chimenechi. Koma kodi udzachikwaniritsa bwanji?
16, 17. Kodi lemba la Danieli 2:44 limatiuza chiyani za Ufumu wa Mulungu?
16 Taganizirani ulosi umene uli pa Danieli 2:44. Palembali timawerenga kuti: “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” Kodi lemba limeneli likutiuza chiyani za Ufumu wa Mulungu?
17 Choyamba, likutiuza kuti Ufumu wa Mulungu udzakhazikitsidwa “m’masiku a mafumu amenewo,” kapena kuti mafumu ena akulamulirabe. Chachiwiri, likutiuza kuti Ufumu umenewu udzakhalapo mpaka kalekale. Sudzagonjetsedwa n’kulowedwa m’malo ndi ufumu wina. Chachitatu, tikuona kuti padzakhala nkhondo pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maufumu a padziko lapansi. Ufumu wa Mulungu udzapambana pa nkhondoyi moti udzatsalapo wokha ndipo uzidzalamulira anthu onse a padziko lapansi. Pa nthawiyi anthu azidzasangalala chifukwa cholamuliridwa ndi Ufumu wabwino kwambiri umenewu.
18. Kodi nkhondo yomalizira imene idzakhale pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maboma a dzikoli imatchedwa chiyani?
18 Baibulo limafotokoza zambiri zokhudza nkhondo imeneyi ya pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maufumu a padziko lapansi. Mwachitsanzo, limafotokoza kuti mapeto akamayandikira, mizimu yoipa izidzafalitsa nkhani zabodza n’cholinga choti isocheretse “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” Mizimuyi idzachita zimenezi kuti ‘iwasonkhanitsire pamodzi kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ Mafumu a padziko lonse lapansi adzasonkhanitsidwa “kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo,” kapena kuti Aramagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Chifukwa cha zimene zafotokozedwa m’mavesi awiriwa, nkhondo ya pakati pa maufumu a padziko lapansi ndi Ufumu wa Mulungu imatchedwa nkhondo ya Aramagedo.
19, 20. Kodi n’chiyani chikulepheretsa kuti panopo chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansili?
m’Mutu 5, Yesu anatifera n’cholinga choti tikhale ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha. Tikukhulupirira kuti mukukumbukira mawu a m’buku la Yohane akuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
19 Kodi cholinga chomenyera nkhondo ya Aramagedo n’chiyani? Kumbukiraninso cholinga chimene Mulungu anali nacho polenga dziko lapansi. Yehova Mulungu ankafuna kuti dziko lonse lapansi likhale Paradaiso ndipo lidzaze ndi anthu olungama oti azimutumikira mpaka kalekale. Koma panopa zinthu sizili choncho chifukwa ndife ochimwa ndipo timadwala komanso kufa. Koma monga tinaphunzirira20 Vuto lina limene likuchititsa kuti panopa zinthu zisakhale mmene Mulungu ankafunira ndi loti anthu ambiri amachita zinthu zoipa. Amanama, amachita zachinyengo ndiponso amachita zachiwerewere. Safuna kuchita chifuniro cha Mulungu. Anthu amene amachita zinthu zoipa zimenezi adzawonongedwa pa nkhondo ya Mulungu ya Aramagedo. (Werengani Salimo 37:10.) Vuto linanso ndi loti maboma samalimbikitsa anthu kuti azichita zimene Mulungu amafuna. Maboma ambiri alibe mphamvu, ndi ankhanza, ndiponso akatangale. Baibulo limanena zoona likamati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”—Mlaliki 8:9.
21. Kodi Ufumu wa Mulungu udzapangitsa bwanji kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi?
21 Pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, anthu onse azidzalamuliridwa ndi boma limodzi, lomwe ndi Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewu uzidzachita chifuniro cha Mulungu ndipo udzabweretsa madalitso ambiri kwa anthu. Mwachitsanzo, udzachotsa Satana ndi ziwanda zake. (Chivumbulutso 20:1-3) Chifukwa cha nsembe ya Yesu, anthu omwe azidzalamuliridwa ndi Ufumuwu sazidzadwala kapena kufa. Adzakhala ndi mwayi wosangalala ndi moyo mpaka kalekale. (Werengani Chivumbulutso 22:1-3.) Pa nthawi imeneyo dziko lonse lapansi lidzakonzedwa n’kukhala paradaiso. Choncho Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi ndiponso kuti dzina lake liyeretsedwe. Zimenezi zikusonyeza kuti m’kupita kwa nthawi anthu onse mu Ufumuwo azidzalemekeza dzina la Yehova Mulungu.
KODI UFUMU WA MULUNGU UDZATHETSA LITI MABOMA A PADZIKO LAPANSI?
22. Kodi tikudziwa bwanji kuti Ufumu wa Mulungu sunabwere pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi kapena atangoukitsidwa kumene?
22 Pamene Yesu ankauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti, “Ufumu wanu ubwere” ankasonyeza kuti pa nthawi imeneyo Ufumuwo unali usanabwere. Kodi unabwera iye atangobwerera kumwamba? Ayi, chifukwa Petulo ndi Paulo ananena kuti ulosi wa pa Salimo 110:1 unakwaniritsidwa Yesu ataukitsidwa. Ulosiwu umati: “Yehova wauza Ambuye wanga kuti: ‘Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.’” (Salimo 110:1; Machitidwe 2:32-35; Aheberi 10:12, 13) Izi zikusonyeza kuti Yesu anayenera kudikira kaye.
Mu Ufumu wa Mulungu, chifuniro cha Mulungu chidzachitika padziko lapansi ngati mmene chikuchitikira kumwamba
23. (a) Kodi Ufumu wa Mulungu unayamba liti kulamulira? (b) Kodi mutu wotsatira udzafotokoza chiyani?
23 Kodi anayenera kudikira kwa nthawi yaitali bwanji? M’zaka za m’ma 1800 ndi 1900, ophunzira Baibulo okhulupirika anayamba kuzindikira kuti nthawi yodikirayi idzatha mu 1914. (Kuti mumve zambiri za chaka chimenechi, onani Zakumapeto, tsamba 215-218.) Zinthu zosiyanasiyana zimene zinachitika padziko lonse lapansi kuyambira mu 1914, zimatsimikizira kuti zimene ophunzira Baibulowa ankakhulupirira zinali zoona. Kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo kumasonyeza kuti mu 1914, Khristu anakhala Mfumu ndipo Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira. Choncho tingati panopa tikukhala mu “kanthawi kochepa” kamene katsala kuti Satana awonongedwe. (Chivumbulutso 12:12; Salimo 110:2) Tinganenenso motsimikiza kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uchititsa kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi. Kodi mukuona kuti nkhani imeneyi ndi yosangalatsa? Kodi mukukhulupirira kuti zimenezi zidzachitikadi? Mutu wotsatira udzakuthandizani kudziwa kuti zimenezi zidzachitikadi.