MUTU 4
Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani?
-
Kodi Yesu ali ndi udindo wapadera wotani?
-
Kodi anachokera kuti?
-
Kodi anali munthu wotani?
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani tingati kudziwa dzina la munthu winawake wotchuka sikumatanthauza kuti mumamudziwadi zenizeni? (b) Kodi anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana otani onena za Yesu?
PADZIKO lapansi pali anthu ambiri otchuka. Ena amangokhala odziwika kwambiri m’dera lawo, m’mzinda wawo, kapena m’dziko lawo. Koma ena amadziwika padziko lonse. Komatu kungodziwa dzina la munthu wotchuka sikumatanthauza kuti mukumudziwa bwino. Mumakhala kuti simukudziwa mbiri yake, khalidwe lake komanso kuti amachita zotani.
2 Anthu padziko lonse amva nkhani za Yesu Khristu, ngakhale kuti iye anakhala padzikoli zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Komabe anthu ambiri sadziwa bwinobwino kuti Yesu anali munthu wotani. Ena amati anangokhala munthu wabwino, ena amanena kuti anali mneneri ngati aneneri ena onse, pomwe enanso amakhulupirira kuti Yesu ndi Mulungu ndipo ndi woyenera kulambiridwa. Koma kodi zimenezi ndi zoona?
3. Kodi kudziwa Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu n’kofunika bwanji?
3 Muyenera kumudziwa Yesu molondola chifukwa Baibulo limanena kuti: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Lembali likusonyeza kuti kudziwa Yehova ndi Yesu Khristu molondola kungachititse kuti munthu adzapeze moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Yohane 14:6) Komanso, zimene Yesu ankachita ali padziko lapansi ndi chitsanzo chabwino cha mmene tiyenera kukhalira ndi ena. (Yohane 13: 34, 35) M’mutu woyamba wa bukuli tinakambirana mfundo zotithandiza kumudziwa Mulungu molondola. Tsopano tiyeni tikambirane zimene Baibulo limaphunzitsa zomwe zingatithandize kumudziwa bwino Yesu Khristu.
MESIYA AMENE MULUNGU ANANENERATU KUTI ADZABWERA
4. Kodi mayina akuti “Mesiya” ndi “Khristu” amatanthauza chiyani?
4 Zaka zambirimbiri Yesu asanabadwe, Baibulo linaneneratu kuti Mulungu adzatumiza Mesiya, kapena kuti Khristu. Mayina akuti “Mesiya” (kuchokera ku Chiheberi) ndi “Khristu” (kuchokera ku Chigiriki) amatanthauza “Wodzozedwa.” Munthu ameneyu anali woti adzadzozedwa, zomwe zikutanthauza
kuti adzapatsidwa udindo wapadera ndi Mulungu. M’mitu yakutsogoloku tidzaphunzira za udindo umene Mesiya ali nawo pokwaniritsa zimene Mulungu analonjeza. Tidzaphunziranso za madalitso amene Yesu angatipatse ngakhale panopo. Koma Yesu asanabadwe anthu ambiri ayenera ankadzifunsa kuti, ‘Kodi Mesiya ameneyu adzakhala ndani?’5. Kodi ophunzira a Yesu ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti iye anali ndani?
5 Pamene Yesu anali padziko lapansi pano, ophunzira ake ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti iye anali Mesiya yemwe ananenedweratu kuti adzabwera. (Yohane 1:41) Mmodzi wa ophunzirawo, dzina lake Simoni Petulo, anauza Yesu kuti: “Ndinu Khristu.” (Mateyu 16:16) Koma kodi n’chiyani chinawapangitsa ophunzirawo kutsimikizira kuti Yesu analidi Mesiya? Nanga ifeyo tingatsimikize bwanji?
6. Fotokozani fanizo losonyeza mmene Yehova anathandizira anthu okhulupirika kuti adziwe Mesiya mosavuta.
6 Aneneri a Mulungu omwe analipo Yesu asanabadwe ananeneratu zinthu zambiri zokhudza Mesiya. Zimenezi n’zomwe zinathandiza kuti anthu amudziwe mosavuta. Tiyeni tiyerekezere kuti, mwatumidwa kudepoti ya basi, kusiteshoni ya sitima kapena kubwalo la ndege kuti mukachingamire munthu amene simunamuonepo. Kodi sizingakuthandizeni ngati munthu wina atakufotokozerani zina ndi zina zokhudza munthuyo? Zimenezi zikufanana ndi zimene Yehova anachita. Pogwiritsa ntchito aneneri, Yehova anafotokoza bwino zimene Mesiya adzachite ndiponso zimene zidzamuchitikire. Kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa kunathandiza anthu okhulupirika kudziwa Mesiya mosavuta.
7. Fotokozani zitsanzo ziwiri za maulosi onena za Yesu amene anakwaniritsidwa.
7 Tiyeni tione zitsanzo ziwiri zokha. Choyamba, kutatsala zaka zoposa 700 kuti Yesu abadwe, mneneri Mika ananeneratu kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu, yomwe inali tawuni yaing’ono ku Yuda. (Mika 5:2) Ndiyeno kodi Yesu anabadwira kuti? Anabadwiradi ku Betelehemu. (Mateyu 2:1, 3-9) Chachiwiri, kutatsala zaka zambirimbiri kuti Mesiya aonekere, ulosi wa pa Danieli 9:25 unatchula chaka chenicheni chimene Mesiyayo adzaonekere. Ulosiwo unanena kuti adzaonekera mu 29 C.E. * Kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa ndi enanso ambiri, kumatsimikizira kuti Yesu analidi Mesiya.
8, 9. Kodi zoti Yesu ndi Mesiya zinaonekera bwanji pa nthawi imene ankabatizidwa?
8 Umboni winanso wosonyeza kuti Yesu anali Mesiya unaoneka chakumapeto kwa chaka cha 29 C.E. Chimenechi ndi chaka chimene Yesu anapita kwa Yohane M’batizi kuti akabatizidwe mumtsinje wa Yorodano. Yehova analonjeza Yohane kuti amupatsa chizindikiro chomuthandiza kudziwa Mesiya. Ndipo Yohane anaonadi chizindikirocho pamene ankabatiza Yesu. Baibulo limati zimene zinachitika n’zakuti: “Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo. Pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzamutera. Panamvekanso mawu ochokera kumwamba onena kuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.’” (Mateyu 3:16, 17) Yohane ataona komanso kumva zimene zinachitikazo, sanakayikire zoti Yesu anatumidwa ndi Mulungu. (Yohane 1:32-34) Pa nthawi imene mzimu wa Mulungu, kapena kuti mphamvu imene amagwiritsa ntchito, unathiridwa pa Yesu, m’pamene anakhala Mesiya kapena kuti Khristu, kutanthauza kuti anasankhidwa ndi Mulungu kukhala Mtsogoleri ndi Mfumu.—Yesaya 55:4.
9 Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa m’Baibulo ndiponso zimene Yehova Mulungu analankhula yekha zimapereka umboni wakuti Yesu analidi Mesiya. Koma Baibulo limayankhanso mafunso ena awiri ofunika okhudza Yesu Khristu. Mafunso ake ndi akuti: Kodi anachokera kuti? Nanga anali munthu wotani?
KODI YESU ANACHOKERA KUTI?
10. Kodi Baibulo limatiuza chiyani za moyo wa Yesu asanabwere padziko lapansi?
10 Baibulo limatiuza kuti Yesu anali kumwamba asanabwere Mika 5:2) Yesu anafotokozanso yekha maulendo ambiri kuti anali kumwamba asanabadwe ngati munthu padziko lapansi. (Werengani Yohane 3:13; 6:38, 62; 17:4, 5) Yesu ali kumwamba anali mzimu ngati mmene angelo alili ndipo ankagwirizana kwambiri ndi Yehova.
padziko lapansi. Mika ananeneratu kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu ndiponso kuti “wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira.” (11. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yesu ndi mwana wapadera kwambiri wa Yehova?
11 Yesu ndi mwana wapadera kwambiri wa Yehova ndipo pali zifukwa zomveka zimene amamuonera choncho. Iye amatchedwa “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” chifukwa ndi amene Mulungu anayambirira kumulenga. * (Akolose 1:15) Palinso chinthu china chimene chimachititsa kuti mwana ameneyu akhale wapadera. Iye ndi “Mwana wake wobadwa yekha.” (Yohane 3:16) Zimenezi zikutanthauza kuti ndi Yesu yekha amene analengedwa ndi Mulungu mwiniwake osagwiritsira ntchito winawake. Pamene polenga zinthu zina zonse Mulungu anagwiritsira ntchito Yesu. (Akolose 1:16) Yesu amatchedwanso “Mawu.” (Yohane 1:14) Izi zikusonyeza kuti iye ankalankhula m’malo mwa Mulungu, kupereka mauthenga ndi malangizo ochokera kwa Mulungu kupita kwa ana ena a Mulunguyo, omwe ndi angelo ndi anthu.
12. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu si wofanana ndi Mulungu?
12 Koma kodi Mwana woyambayu ndi wofanana ndi Mulungu ngati mmene ena amanenera? Zimenezi si zimene Baibulo limanena. Monga mmene taonera m’ndime yapitayi, Mwana ameneyu anachita kulengedwa. Izi zikusonyeza kuti iye poyamba kunalibe, pomwe Yehova Mulungu wakhala alipo kuyambira kalekale. (Salimo 90:2) Mwana woyamba kubadwayu sanayambe waganizapo zofuna kukhala wofanana ndi Atate ake. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti Atate ndi wamkulu kuposa Mwanayo. (Werengani Yohane 14:28; 1 Akorinto 11:3) Yehova yekha ndi amene ali “Mulungu Wamphamvuyonse.” (Genesis 17:1) Choncho alibe wofanana naye. *
13. Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamanena kuti Yesu ndi “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo”?
13 Yehova ndi Mwana wake woyamba kubadwayu anakhala limodzi mogwirizana kwa zaka mabiliyoni ambiri zinthu zakumwamba ndiponso dziko lapansi zisanalengedwe. Iwo ayenera kuti ankakondana kwambiri. (Yohane 3:35; 14:31) Mwana wokondedwa ameneyu ankatengera zochita za Atate ake. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Mwanayo ndi “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo.” (Akolose 1:15) Mwana wa Mulungu ameneyu anatengera makhalidwe ndi zochita za Atate ake mofanana ndi mmene mwana aliyense amatengera zochita za bambo ake.
14. Kodi zinatheka bwanji kuti Mwana wa Yehova abadwe ngati munthu?
14 Mwana wa Yehova ameneyu analolera kuchoka kumwamba n’kudzabadwa padziko lapansi ngati munthu. Koma mwina mukudabwa kuti, ‘Kodi zinatheka bwanji kuti Yesu, yemwe analipo kale kumwamba ngati mngelo adzabadwe ngati munthu?’ Kuti zimenezi zitheke, Yehova anachita chozizwitsa. Iye anasamutsa moyo wa Mwana wake woyamba kubadwa kuchokera kumwamba n’kuuika m’mimba mwa namwali wachiyuda, dzina lake Mariya. Panalibe mwamuna amene anagona naye. Zimenezi zinachititsa kuti Mariya abereke mwana wangwiro ndipo anam’patsa dzina lakuti Yesu.—Luka 1:30-35.
KODI YESU ANALI MUNTHU WOTANI?
15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kudziwa Yesu kungatithandize kumudziwa bwino Mulungu?
15 Zimene Yesu analankhula komanso kuchita ali padziko lapansi pano zimatithandiza kumudziwa bwino. Kumudziwa bwino Yesu kungatithandizenso kumudziwa bwino Yehova. Kodi n’chifukwa chiyani tikutero? Kumbukirani kuti Yesu amasonyeza ndendende makhalidwe a Yehova, yemwe ndi Atate ake. N’chifukwa chake Yesu anauza wophunzira wake wina kuti: Yohane 14:9) Mabuku 4 a m’Baibulo omwe amadziwika kuti Mauthenga Abwino amatifotokozera zambiri za moyo wa Yesu Khristu, monga zimene ankachita ndiponso khalidwe lake. Mabuku amenewa ndi Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane.
“Amene waona ine waonanso Atate.” (16. Kodi uthenga umene Yesu ankalalikira kwenikweni unali wokhudza chiyani, nanga zimene ankaphunzitsa anazitenga kuti?
16 Anthu ambiri ankamudziwa Yesu ngati “Mphunzitsi.” (Yohane 1:38; 13:13) Kodi ankaphunzitsa zotani? Kwenikweni zimene ankaphunzitsa zinali “uthenga wabwino wa ufumu.” (Mateyu 4:23) Ufumu umenewu ndi Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma lakumwamba limene lidzalamulire dziko lonse lapansi ndipo udzabweretsa madalitso amene sadzatha kwa anthu omvera. Koma kodi uthenga womwe Yesu ankalalikirawu unali wochokera kwa ndani? Yesu anafotokoza yekha kuti: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma,” yemwe ndi Yehova. (Yohane 7:16) Yesu ankadziwa kuti Atate ake akufuna zoti anthu amve uthenga wabwino wa Ufumu. M’mutu 8, tidzaphunzira zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu ndiponso zimene udzachite.
17. Kodi Yesu ankaphunzitsa kuti, nanga n’chifukwa chiyani ankagwira ntchito imeneyi mwakhama kwambiri?
17 Kodi Yesu ankaphunzitsa kuti? Ankaphunzitsa kulikonse kumene kunkapezeka anthu monga m’mizinda, m’midzi, m’misika ndi kunyumba za anthu. Yesu sankadikira kuti anthu abwere kumene iyeyo anali kuti ayambe kuwaphunzitsa koma ankapita kumene kunali anthuwo. (Maliko 6:56; Luka 19:5, 6) Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ankadzipereka kwambiri choncho pogwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa? Chifukwa ndi zomwe Mulungu ankafuna kuti achite. Nthawi zonse Yesu ankachita zimene Atate ake amafuna. (Yohane 8:28, 29) Koma panalinso chifukwa china chimene chinkamuchititsa kuti azigwira ntchito yolalikira. Ankamvera chisoni anthu ambirimbiri amene ankabwera kuti adzamuone. (Werengani Mateyu 9:35, 36.) Anthu amenewa sankasamalidwa ndi atsogoleri awo achipembedzo, omwe ankayenera kuwaphunzitsa mfundo zolondola zonena za Mulungu komanso zolinga zake. Yesu ankadziwa kuti anthuwo ankafunikira kwambiri kumva uthenga wa Ufumu.
18. Kodi ndi makhalidwe ati a Yesu omwe amakuchititsani chidwi kwambiri?
18 Yesu anali munthu wachikondi komanso woganizira ena. N’chifukwa chake anthu ena ankamuona kuti ndi wochezeka komanso wachifundo. Ngakhale ana ankacheza naye momasuka. (Maliko 10:13-16) Yesu sankachita zinthu mokondera, moti ankadana ndi katangale ndiponso zinthu zopanda chilungamo. (Mateyu 21:12, 13) Pa nthawi imeneyo anthu ambiri sankalemekeza azimayi moti ankawapondereza. Koma Yesu ankawalemekeza kwambiri. (Yohane 4:9, 27) Yesu anali wodzichepetsa kwambiri moti nthawi ina anasambitsa mapazi a ophunzira ake, ntchito imene nthawi zambiri inkagwiridwa ndi wantchito wamba.
19. Kodi ndi chitsanzo chiti chimene chikusonyeza kuti Yesu ankakhudzidwa akaona anthu ena akuvutika?
19 Yesu ankakhudzidwa akaona anthu ena akuvutika. Umboni waukulu wosonyeza kuti zinkamukhudza ndi zimene anachita pochiritsa anthu odwala ndi mphamvu ya mzimu wa Mulungu. Mateyu 14:14) Mwachitsanzo, munthu wina wakhate anabwera kwa Yesu n’kunena kuti: “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.” Yesu anakhudzidwa kwambiri poganizira ululu umene munthuyo ankamva. Chifukwa chomumvera chisoni, Yesu anatambasula dzanja lake n’kumugwira, kenako anamuuza kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.” Atangochita zimenezi munthuyo anachira. (Maliko 1:40-42) Kodi mukuganiza kuti munthuyu anamva bwanji atamuchiritsa?
(ANALI WOKHULUPIRIKA MOYO WAKE WONSE
20, 21. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yokhala wokhulupirika kwa Mulungu?
20 Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yokhala wokhulupirika kwa Mulungu. Nthawi zonse anali wokhulupirika kwa Atate ake akumwamba ngakhale kuti ankatsutsidwa komanso kuzunzidwa. Yesu anatsutsa mwamphamvu mayesero onse a Satana. (Mateyu 4:1-11) Pa nthawi ina, ena mwa achibale ake sankamukhulupirira, moti mpaka ankamunena kuti “wachita misala.” (Maliko 3:21) Koma Yesu sanalole kuti zochita za achibale akewo zimusokoneze chifukwa mtima wake wonse unali potumikira Mulungu. Ngakhale kuti anthu ankamunyoza komanso kumuzunza, Yesu sankapsa mtima kapena kubwezera.—1 Petulo 2:21-23.
21 Yesu anakhalabe wokhulupirika ngakhale pamene adani ake ankamuzunza mpaka kumupha mwankhanza. (Werengani Afilipi 2:8.) Taganizirani zimene zinamuchitikira pa tsiku limene anaphedwa. Anamangidwa, anthu ankamunenera zinthu zabodza, oweruza achinyengo anamugamula kuti ndi wolakwa, anthu ambirimbiri ankamuseka ndiponso asilikali anamuzunza. Atakhomereredwa pamtengo, anapuma komaliza n’kunena kuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!” (Yohane 19:30) Koma patapita masiku atatu Yesu atamwalira, Atate ake akumwamba anamuukitsa ndipo anakhalanso mzimu ngati poyamba. (1 Petulo 3:18) Patapita milungu ingapo anabwerera kumwamba. Atafika kumwambako, “anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu” kuyembekezera kuti apatsidwe mphamvu zokhala mfumu.—Aheberi 10:12, 13.
22. Kodi kukhulupirika kwa Yesu mpaka imfa yake kuli ndi phindu lotani?
22 Kodi kukhulupirika kwa Yesu mpaka imfa yake kunali ndi phindu lililonse? Inde, chifukwa imfa yake inatipatsa mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi mogwirizana ndi zimene Yehova ankafuna poyamba. M’mutu wotsatira tikambirana mmene imfa ya Yesu inathandizira kuti zimenezi zikhale zotheka.
^ ndime 7 Onani Zakumapeto tsamba 197-199, pomwe tafotokoza mmene ulosi wa Danieli unakwaniritsidwira pa Yesu.
^ ndime 11 Yehova amatchedwa Atate chifukwa ndi Mlengi. (Yesaya 64:8) Yesu amatchulidwa kuti ndi Mwana wa Mulungu chifukwa analengedwa ndi Mulungu. N’chifukwa chakenso angelo komanso Adamu amatchulidwa kuti ndi ana a Mulungu.—Yobu 1:6; Luka 3:38.
^ ndime 12 Kuti muone umboni wina wotsimikizira kuti Yesu si wofanana ndi Mulungu, onani Zakumapeto tsamba 201-204.