GEORGIA | 1924-1990
Anthu Oyambirira Kuphunzira Choonadi
CHAKUMAYAMBIRIRO kwa zaka za m’ma 1920, Ophunzira Baibulo anayamba kulalikira anthu omwe ankafuna kuphunzira choonadi ku Georgia. M’chaka cha 1924 Ophunzira Baibulowa anatsegula ofesi ku Beirut, m’dziko la Lebanon, kuti iziyang’anira ntchito yolalikira ku Armenia, Georgia, Syria ndi Turkey.
Pa nthawi imeneyi mbewu zambiri za choonadi zinafesedwa ku Georgia, koma poyamba zotsatira zake sizinkaoneka bwinobwino. (Mat. 13:33) Patapita nthawi, uthenga wabwino unafalikira m’dzikoli ndipo unathandiza kuti anthu ambiri asinthe miyoyo yawo.
Ankafunitsitsa Kuona Chilungamo Chikuchitika
Pamene nkhondo yachiwiri yapadziko lonse inkayamba, Vaso Kveniashvili anali wachinyamata. Popeza dziko la Georgia linali pansi pa ulamuliro wa Soviet Union, bambo ake anauzidwa kuti apite kukamenya nawo nkhondo. Pa nthawiyi
n’kuti mayi ake atamwalira. Popeza Vaso anali woyamba kubadwa, udindo wonse wosamalira abale ake unakhala m’manja mwake, moti anayamba kuba kuti azipeza ndalama.Ndiyeno Vaso analowa m’gulu la zigawenga ndipo ankachita zinthu zambiri zoipa. Iye anati, “Ndinkaona kuti boma komanso anthu wamba amachita zinthu zambiri zopanda chilungamo kuposa zigawenga.” Koma kenako, Vaso anayamba kuona kuti palibe amene angakwanitse kuchita zinthu zachilungamo. Iye anati: “Ndinkafunitsitsa kuona chilungamo chikuchitika.”
Chifukwa cha khalidwe lake loipa, Vaso anamangidwa ndipo anatumizidwa kundende ya ku Siberia. Ali kumeneko, anakumana ndi munthu wina wa Mboni za Yehova, yemwe anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chake. Vaso anati, “Apa m’pamene ndinapeza zimene ndinkafuna. Ngakhale kuti tinalibe mabuku, ndinapindula kwambiri ndi zimene
m’baleyo ankandiphunzitsa ndipo ndinazindikira kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungabweretse chilungamo.”Atatuluka m’ndende mu 1964, Vaso anabwerera kwawo ku Georgia ndipo anayamba kufufuza a Mboni za Yehova. Iye anapitirizabe kulemberana makalata ndi m’bale yemwe anali naye limodzi kundende uja. Koma n’zomvetsa chisoni kuti m’baleyo anamwalira ndipo Vaso sanakumanenso ndi wa Mboni aliyense. Panapita zaka pafupifupi 20 kuti akumanenso ndi a Mboni za Yehova. Tifotokoza zambiri za m’bale ameneyu kutsogoloku.
Mavuto Amene Anakumana Nawo Anamuthandiza Kupeza Madalitso
Mayi wina wa ku Georgia, dzina lake Valentina Miminoshvili, anamangidwa n’kuikidwa m’ndende ina ya chipani cha Nazi. Zimene zinachitikazi zinachititsa kuti apeze madalitso aakulu chifukwa ali kundendeko anakumana ndi a Mboni za Yehova. Chimene chinamuchititsa chidwi kwambiri chinali choti a Mboniwo anali ndi chikhulupiriro cholimba. Iye
anasangalala kwambiri ndi zimene ankaphunzira kuchokera m’Baibulo.Nkhondo itatha, Valentina anabwerera kwawo ku Georgia ndipo anayamba kuuza ena zimene anaphunzira kundende kuja. Koma zimene ankachitazi zinachititsa kuti apolisi amumange ndipo anaweruzidwa kuti akakhale kundende ya ku Russia kwa zaka 10. Ali kumeneko anakumananso ndi a Mboni za Yehova moti patapita nthawi anabatizidwa.
Atatuluka kundendeyi mu 1967, anapita kuchigawo chakumadzulo kwa Georgia ndipo ali kumeneko anapitirizabe kulalikira, koma ankachita zimenezi mosamala. Valentina sankadziwa kuti zimene ankachitazi zithandiza kuti pemphero la munthu wina liyankhidwe.
Yehova Anayankha Mapemphero Ake
Mu 1962, Mlongo Antonina Gudadze, anasamuka ku Siberia n’kupita ku Georgia. Anachita zimenezi chifukwa mwamuna wake, yemwe anali wosakhulupirira, ankafuna kubwerera kwawo. Kwawo kwa mlongoyu kunali ku Siberia ndipo n’kumene anaphunzira Baibulo ndi a Mboni omwe anatumizidwa kundende ya kumeneko. Atafika m’chigawo chakumadzulo kwa dziko la Georgia, anakakhala mumzinda wa Khashuri koma sanakumane ndi wa Mboni aliyense.
Mlongo Antonina ananena kuti Yehova anayankha mapemphero ake. Iye anati: “Tsiku lina ndinalandira katundu wochokera kwa mayi anga ku Siberia. Pakati pa katunduyo panabisidwa mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Kwa zaka 6 ndinakhala ndikulandira mabuku kudzera m’njira imeneyi. Ndikalandira mabukuwo, ndinkathokoza Yehova chifukwa cha zimene ankandichitira ndiponso chifukwa cha malangizo olimbikitsa komanso othandiza amene ankandipatsa.”
Vuto lina linali lakuti Antonina anali yekha wa Mboni mumzindawo. Iye anati: “Ndinkapempha Yehova kuti andithandize kukumananso ndi abale komanso alongo. Tsiku lina, azimayi awiri analowa musitolo yomwe ndinkagwira ntchito
ngati kalaliki. Anandifunsa kuti, ‘Kodi ndinu a Antonina?’ Nditangoona mmene nkhope zawo zinkaonekera, sindinakayikire kuti anali Akhristu anzanga. Kenako ndinawakumbatira moti tonse tinayamba kulira.”Mmodzi mwa alongo awiriwa anali Mlongo Valentina Miminoshvili. Mlongo Antonina atamva zoti misonkhano inkachitikira m’chigawo chakumadzulo kwa dziko la Georgia, anasangalala kwambiri. Mlongoyu anayamba kupita kumisonkhano kamodzi pamwezi ngakhale kuti misonkhanoyo inkachitikira kutali kwambiri, pamtunda wa makilomita 300 kuchokera kwawo.
Anthu Ambiri a M’chigawo Chakumadzulo kwa Dziko la Georgia Anayamba Kuphunzira Choonadi
M’zaka za m’ma 1960, a Mboni za Yehova anayamba kuzunzidwa m’madera ena omwe anali pansi pa ulamuliro wa Soviet Union ndipo ankathawira m’madera omwe zinthu zinali bwinoko. Mmodzi mwa anthu amene anathawawo anali M’bale Vladimir Gladyuk, yemwe anali wakhama komanso wodzipereka. Mu 1969, m’baleyu anasamuka ku Ukraine n’kupita mumzinda wa Zugdidi, womwe uli m’chigawo chakumadzulo kwa dziko la Georgia.
Poyamba, anthu amene anasamukira ku Georgia ankachita misonkhano yawo m’chinenero cha ku Russia. M’kupita kwa
nthawi, anthu ambiri a ku Georgia anayamba kufika pamisonkhano. Zimenezi zinachititsa kuti akonze zoti misonkhano iyambe kuchitikira m’Chijojiya. Ntchito yophunzitsa anthu Baibulo inkayenda bwino kwambiri moti mu August 1970, anthu 12 a m’dziko la Georgia anabatizidwa.Chakumayambiriro kwa chaka cha 1972, M’bale Vladimir ndi banja lake anasamukira mumzinda wa Sokhumi, womwe uli m’mbali mwa nyanja ya Black Sea. M’bale Vladimir anati: “Tinkaona kuti Yehova watidalitsa kwambiri moti tinkafuna kumuthokoza chifukwa cha zimene anatichitira. Mpingo wa kumene tinasamukirako unakula mofulumira kwambiri.” Pa nthawi imeneyi, m’dera la Sokhumi munachitika Chikumbutso choyamba ndipo pamwambowu panasonkhana anthu 45.
“Ndinamvetsera ndi Mtima Komanso Moyo Wanga Wonse”
Panopa Mlongo Babutsa Jejelava ali ndi zaka zoposa 90. Mlongoyu ndi mmodzi mwa anthu amene anali oyambirira kuphunzira choonadi mumzinda wa Sokhumi, chakumayambiriro kwa chaka cha 1973. Iye anati: “Tsiku lina
ndinakumana ndi azimayi 4 omwe ankakambirana nkhani inayake. Azimayi awiri anali masisitere ndipo enawo, monga mmene ndinamvera pambuyo pake, anali a Mboni za Yehova.” Mlongo mmodzi anali mkazi wa Vladimir Gladyuk, yemwe dzina lake ndi Lyuba ndipo winayo anali Mlongo Itta Sudarenko, yemwe anali mpainiya wakhama kwambiri wochokera ku Ukraine.A Babutsa ananena kuti zimene azimayiwa ankakambirana zinawafika pamtima kwambiri. Iwo anati: “Ndinamvetsera ndi mtima komanso moyo wanga wonse.” Atamva zoti Mulungu ali ndi dzina, anapita pomwepo ndipo anapempha kuti amuonetse dzinalo kuchokera m’Baibulo. Mlongoyu anafunsa mafunso ambirimbiri moti zimenezi zinachititsa kuti akhale pamalopo kwa maola atatu.
Mlongo Babutsa ankafunitsitsa kudzaonananso ndi azimayi a Mboniwo moti anafunsa kuti, “Kodi muzipita n’kundisiya pompano?”
Alongowo anayankha kuti: “Ayi, sitikusiyani. Tibweranso Loweruka kuti tidzakambirane zambiri.”
Tsikulo litafika, a Babutsa anasangalala kwambiri chifukwa alongowo anabweradi ndipo nthawi yomweyo anayamba kuphunzira Baibulo. Atatsala pang’ono kumaliza phunzirolo, a Babutsa anauza alongowo kuti asasiye kubwera kudzawaphunzitsa Baibulo. Pansi pamtima ankangoti: ‘Ndachita mwayi kukumana ndi anthu amenewa ndipo sindilola kuti ndisiyane nawo.’
Kuti asasiyane ndi alongowa, a Babutsa anapanga pulani. Iwo anati: “Ndinkadziwa kuti a Lyuba ndi okwatiwa, choncho ndinafunsa a Itta ngati nawonso anali pa banja. A Itta atayankha kuti sali pa banja ndinawauza kuti, ‘Ndiyetu mubwere muzidzakhala ndi ine! M’chipinda changa muli mabedi awiri ndipo pakati pa mabediwo pali nyali. Tikhoza kugwiritsa ntchito nyali imeneyo n’kumaphunzira Baibulo ngakhale usiku.’” Mlongo Itta anavomera moti anayamba kukhala kunyumba kwa a Babutsa.
Pokumbukira zimene zinkachitika nthawi imeneyo, Mlongo Babutsa anati: “Nthawi zina sindinkagona chifukwa choganizira zimene ndinkaphunzira. Funso likabwera m’maganizo mwanga, ndinkadzutsa Mlongo Itta n’kumuuza kuti: ‘A Itta, tatengani Baibulo lanu! Ndili ndi funso.’ Mlongo Itta ankadzuka kwinaku akutikita m’maso chifukwa cha tulo, ndipo ankandiyankha kuti: ‘Chabwino, funso lako ndi lotani?’ Ndikafunsa ankatsegula Baibulo n’kundionetsa yankho lake.” Patangotha masiku atatu, Mlongo Itta atasamukira kumeneku, a Babutsa anayamba kulalikira uthenga wabwino.
A Babutsa anali ndi mnzawo wapamtima, dzina lake Natela Chargeishvili. Mlongo Babutsa anati: “Ndinkaganiza kuti mnzangayo sangamvetsere choonadi cha m’Baibulo chifukwa kwawo kunali kochita bwino. Koma ndinkalakwitsa kwambiri. Kungoyambira tsiku loyamba limene ndinamulalikira, zinkaoneka kuti mfundo za m’Baibulo zinkamufika pamtima kwambiri.” Pasanapite nthawi, a Babutsa ndi a Natela anayamba kulalikira kwa anzawo, ogwira nawo ntchito komanso anthu omwe ankakhala nawo pafupi.