ZAKUMAPETO
Kuthetsa Kusamvana pa Nkhani za Bizinezi
Pa 1 Akorinto 6:1-8, mtumwi Paulo anafotokoza zimene Akhristu ayenera kuchita ngati asemphana maganizo. Vesi 1 likusonyeza kuti iye anakhumudwa chifukwa chakuti Akhristu ena a ku Korinto ‘ankalimba mtima kupita kukhoti kwa anthu osalungama.’ Paulo ananena kuti Akhristu sayenera kusumirana m’makhoti. Milandu yawo iyenera kukambidwa kumpingo. Ndipo anapereka zifukwa zimene Akhristu ayenera kuchitira zimenezi. Tiyeni tikambirane zina mwa zifukwazi ndiponso tiona zochitika zina zomwe sizinafotokozedwe m’malangizo amenewa.
Ngati tasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzathu pa nkhani za bizinezi, tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi malangizo a Yehova, osati nzeru zathu. (Miyambo 14:12) Yesu anasonyeza kuti ndi bwino kuthetsa kusamvana mofulumira nkhaniyo isanafike poipa. (Mateyu 5:23-26) Koma chomvetsa chisoni n’chakuti, Akhristu ena amakangana kwambiri mpaka kutengerana kukhoti. Pa mfundo imeneyi, Paulo anati: “Ndiye kuti mwalephereratu ngati mukutengerana kukhoti.” N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti kuchita zimenezi n’kulephera? Chifukwa chachikulu n’chakuti zimenezi zingaipitse mbiri ya mpingo ndiponso zinganyozetse dzina la Mulungu amene timalambira. N’chifukwa chake tiyenera kuganizira mozama funso la Paulo lakuti: “Bwanji osangolola kulakwiridwa?”—Vesi 7.
Paulo ananenanso kuti Mulungu wakhazikitsa dongosolo labwino mumpingo lothetsera milandu yambiri. Akulu ndi amuna achikhristu ndipo ndi anzeru chifukwa choti amadziwa choonadi cha m’Malemba. Paulo ananena kuti iwo angathe ‘kuweruza milandu pakati pa abale’ pa nkhani za “m’moyo uno.” (Vesi 3-5) Yesu anasonyeza kuti ngati pali kusemphana maganizo chifukwa cholakwirana zinthu zazikulu, monga kunenerana miseche ndi kuchita chinyengo, nkhanizo ziyenera kuthetsedwa pochita zinthu zitatu izi: Choyamba, anthu awiri amene alakwiranawo aziyesetsa kuthetsa nkhaniyo paokha. Zimenezi zikakanika, azipeza mboni imodzi kapena ziwiri. Ndiyeno zonsezi zikalephereka, azitengera nkhaniyo kwa akulu kumpingo.—Mateyu 18:15-17.
N’zoona kuti akulu achikhristu si maloya kapena alangizi a nkhani za bizinezi ndipo ntchito yawo sikupereka malangizo ngati mmene amachitira anthu amenewa. Iwo samaika malamulo oti atsatiridwe ngati abale asemphana pa nkhani za bizinezi. Koma amafuna kuthandiza anthu amene asemphana maganizowo kuti agwiritse ntchito Malemba ndi kuthetsa nkhaniyo mwamtendere. Koma ngati pali nkhani zikuluzikulu, akulu angathe kufunsa woyang’anira dera kapenanso ku ofesi ya Mboni za Yehova. Komabe, pali zochitika zina zimene Paulo sanafotokoze. Kodi zina mwa nkhani zimenezi n’ziti?
Pa zochitika zina, kupita kukhoti kuti muthetse nkhaniyo mwamtendere komanso popanda kudyerana masuku pamutu kungakhale njira imene malamulo amafuna kapena imene anthu anazolowera. Mwachitsanzo, mwina ndi kukhoti kokha kumene mungapeze chikalata chololeza kuthetsa banja ndiponso chilolezo chotenga ana banja likatha. Mwinanso n’kukhoti kokha kumene angakuuzeni kuchuluka kwa ndalama zimene mwamuna ayenera kumapereka kwa mkazi wake banja likatha. N’kuthekanso kuti n’kukhoti kokha kumene mungapeze chilolezo cholandira inshulansi, cholandira ndalama ngati kampani yagwa, ndiponso kungakhale kumene mungakasainitse mawilo. Nthawi zinanso m’bale angaone kuti n’koyenera kusumira anthu amene anamusumira kukhoti kuti adziteteze pa mlandu. *
Ngati Akhristu atengerana kukhoti pa nkhani ngati zimenezi popanda kukangana, sanachite zosemphana ndi malangizo amene Paulo anapereka. * Komabe, chinthu chofunikira kwambiri kwa Mkhristu chizikhala kuyeretsa dzina la Yehova ndiponso kukhala mwamtendere ndi mogwirizana mumpingo. Chizindikiro chachikulu cha otsatira Khristu ndi chikondi, ndipo “chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.”—1 Akorinto 13:4, 5; Yohane 13:34, 35.
^ ndime 2 Nthawi zinanso Mkhristu angapalamule mlandu waukulu kwa Mkhristu mnzake monga kugwirira, kumenya munthu, kupha, kapena kuba zinthu zochuluka. Zimenezi zikachitika, sikulakwa kuti Mkhristu akanene kupolisi, ngakhale kuti kuchita zimenezi kungachititse kuti wolakwayo aimbidwe mlandu kukhoti.
^ ndime 3 Kuti mumve zambiri, onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 1997, patsamba 17 mpaka 22, ndi ya October 15, 1991, patsamba 25 mpaka 28.