Kodi ndingodzipha?
Zimene Achinyamata Amadzifunsa
Kodi ndingodzipha?
Chaka chilichonse achinyamata mamiliyoni ambiri amafuna kudzipha. Ndipo ambiri amadziphadi. N’chifukwa chake taona kuti m’pofunika kukambirana nkhani imeneyi.
“MUNDICHOTSERETU moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ayi.” Kodi ndani ananena mawuwa? Kodi anali munthu wosakhulupirira Mulungu? Kodi anali munthu amene anasiya kulambira Mulungu? Kapena kodi anali munthu amene anasiyidwa ndi Mulungu? Ayi, sichoncho. Ananena mawuwa ndi Yona *, yemwe anali munthu wodzipereka kwa Mulungu, koma panthawiyi anali atakhumudwa kwambiri. (Yona 4:3) Baibulo silinena kuti Yona anatsala pang’ono kudzipha. Komabe mawu akewa akusonyeza kuti ngakhale mtumiki wa Mulungu nthawi zina angasowe mtendere kwambiri.—Salmo 34:19.
Achinyamata ena amataya mtima kwambiri moti amaona kuti palibe chifukwa chokhalira ndi moyo. Angamve mmene anamvera Laura, * mtsikana wa zaka 16 amene ananena kuti: “Ndakhala ndikusowa mtendere kwanthawi yaitali. Nthawi zambiri ndimaganiza zodzipha.” Kodi mungatani ngati munthu wina wakuuzani kuti akufuna kudzipha kapena ngati inuyo mukufuna kudzipha? Choyamba tiyeni tione chifukwa chake anthu ena amafuna kudzipha.
Zimene Zimachititsa Kutaya Mtima
N’chifukwa chiyani munthu angafune kudzipha? Pangakhale zifukwa zambiri. Chifukwa choyamba n’chakuti tikukhala mu “nthawi yovuta” ndipo achinyamata ambiri amada nkhawa kwambiri ndi mavuto a pamoyo wawo. (2 Timoteyo ) Chifukwa chinanso n’chakuti kupanda ungwiro kumachititsa ena kumangoganiza kuti zinthu pamoyo wawo komanso m’dzikoli sizikuyenda bwino. ( 3:1Aroma 7:22-24) Nthawi zina ena amafuna kudzipha chifukwa chakuti anthu ena anawachitira nkhanza kapena zachipongwe. Koma nthawi zina limakhala vuto la matenda. M’dziko lina kafukufuku anasonyeza kuti pafupifupi anthu onse amene anadzipha anali ndi matenda okhudza maganizo. *
N’zoona kuti tonse timavutika. Baibulo limanena kuti: “Chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zopweteka mpaka pano.” (Aroma 8:22) Mawu amenewa akukhudzanso achinyamata. Ndipotu achinyamata ambiri angakhudzidwe kwambiri ndi zoipa monga:
▪ Imfa ya m’bale wawo, mnzawo, kapena chiweto chimene amachikonda kwambiri
▪ Mikangano ya m’banja
▪ Kulephera kusukulu
▪ Kutha kwa chibwenzi
▪ Kuchitiridwa nkhanza kapena chipongwe monga kumenyedwa kapena kugwiriridwa
Zoona zake n’zakuti nthawi ina achinyamata angavutike ndi zina mwa zimene tatchulazi. N’chifukwa chiyani ena amathana bwinobwino ndi mavuto amenewa pomwe ena zimawavuta? Akatswiri ena amanena kuti achinyamata amene amafika podzipha amakhala ataona kuti palibe aliyense amene angawathandize pa vuto lawolo. Iwo amaona kuti palibe chimene angachite kuti zinthu zikhale bwino, ndipo sakhala ndi chiyembekezo chilichonse choti zinthu zingasinthe. Dokotala wa matenda a maganizo dzina lake Kathleen McCoy anauza ofalitsa magazini ino kuti: “Sikuti achinyamata amenewa amafunadi kufa. Iwo amangofuna kuthetsa mavuto awowo.”
Kodi Pamakhaladi Palibe Mochitira?
Ngati mukudziwapo wachinyamata amene akufuna kudzipha pofuna kuthetsa mavuto ake, kodi mungam’thandize bwanji?
Ngati mnzanu akuda nkhawa kwambiri moti akufuna kudzipha, yesetsani kum’thandiza kuona kuti angathe kupeza thandizo. Uzani munthu wina wamkulu ndipo musaope zimene mnzanuyo angachite akadziwa. Musadandaule kuti mwina ubwenzi wanu ungasokonekere. Ngati muuza munthu wina mudzasonyeza kuti ndinu “bwenzi” lenileni limene ‘linabadwira kuti lithandize pooneka tsoka.’ (Miyambo 17:17) Mukatero mungathe kupulumutsa moyo wake.
Bwanji ngati inuyo mukufuna kudzipha? Dr. McCoy tam’tchula kale uja anati: “Pezani thandizo. Ndibwino kuuza winawake mmene mukumvera. Mungauze kholo, m’bale wanu, mnzanu, mphunzitsi wanu, mtumiki wa mumpingo wanu kapena munthu aliyense amene angakumvetsetseni komanso kukuthandizani. Mukatero mudzathandiza anthu odalirika kuti amve maganizo anu.”
Simungagwe m’vuto chifukwa choti mwauza anthu ena, m’malo mwake angakuthandizeni. Lingalirani chitsanzo cha m’Baibulo. Panthawi ina munthu wolungama Yobu anati: “Mtima wanga ulema nawo moyo wanga.” Koma kenako anati: “Ndidzadzilolera [kapena kuti kuuza ena za] kudandaula kwanga, ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.” (Yobu 10:1) Yobu anali ndi nkhawa ndipo ankafuna kuuza ena vuto lake. Inunso mungapepukidweko ngati mutauza mnzanu wokhwima maganizo za vuto lanu.
Akhristu ali ndi mwayi chifukwa pali enanso amene angawauze vuto lawo. Iwo angathe kuuza akulu mumpingo. (Yakobe 5:14, 15) N’zoona kuti kuuza munthu wina sikungathetseretu vuto lanulo. Koma kungakuthandizeni kuona mavuto anuwo m’njira yoyenera. Zimene mnzanuyo angakuuzeni, zingakuthandizeninso kupeza njira zothetsera vuto lanulo.
Zinthu Zimasintha
Ngati mukuda nkhawa kumbukirani mfundo iyi: Kaya vuto lanu likhale lalikulu bwanji, Salmo 6:6) Davide ananenanso mawu akuti: “Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera.”—Salmo 30:11.
m’kupita kwanthawi zinthu zidzasintha. Wamasalmo Davide anakumana ndi mavuto osaneneka ndipo m’pemphero lake anati: “Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.” (Davide anadzionera yekha kuti mavuto amabwera ndipo amatha. N’zoona kuti panopo mavuto ena angaoneke othetsa nzeru kwambiri. Koma upezeni mtima. Zinthu zingasinthe n’kukhalanso bwinobwino. Nthawi zina vutolo mungalithetse kapena kulipirira m’njira imene simumaiganizira n’komwe. Mfundo ndi yakuti, mavuto anu sangakhale chimodzimodzi mpaka kalekale.—2 Akorinto 4:17.
Pemphero Limathandiza
Kupemphera n’kofunika kwambiri kuposa kulankhulana ndi munthu wina aliyense. Mungapemphere ngati Davide amene anati: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha.”—Salmo 139:23, 24.
Sikuti pemphero ndi njira yongothetsera mavuto. Kumakhala kulankhula ndi Atate wathu wakumwamba amene amafuna kuti ‘tizimutsanulira mitima yathu.’ (Salmo 62:8) Taganizirani mfundo zotsatirazi zokhudza Mulungu:
▪ Iye amadziwa zimene zikupangitsa mavuto athu.—Salmo 103:14.
▪ Iye amakudziwani bwino kuposa mmene mumadzidziwira.—1 Yohane 3:20.
▪ “Amasamala za inu.”—1 Petulo 5:7.
▪ M’dziko latsopano, Mulungu “adzapukuta msozi uliwonse m’maso” mwanu.—Chivumbulutso 21:4.
Ngati Matenda Ndiwo Akuchititsa Munthu Kufuna Kudzipha
Monga tanena kale, nthawi zambiri matenda enaake ndi amene amachititsa anthu kufuna kudzipha. Ngati ndi mmene zilili ndi inu, funani thandizo. Yesu ananena kuti anthu odwala ndi amene amafuna wochiritsa. (Mateyo 9:12) Chosangalatsa n’chakuti munthu angathe kulandira thandizo pamatenda ambiri amene angadwale. Ndipo zimenezi zingakuthandizeni kuti mupezeko bwino.
Baibulo limalonjeza kuti m’dziko latsopano la Mulungu, “wokhalamo sadzanena, ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Panopo yesetsani kuchita zimene mungathe kuti mupirire mavuto pamoyo wanu. Munthu wina ku Germany dzina lake Heidi anachita zimenezi. Iye anati: “Nthawi zina ndinkada nkhawa kwambiri moti ndinkangofuna kudzipha basi. Koma panopo ndili bwinobwino. Ndikuthokoza kwambiri mwayi wa pemphero komanso chithandizo chimene ndikulandira.” Nanunso mungatero. *
M’magazini yotsatira, pamutu wakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” tidzakambirana zimene mungachite ngati m’bale wanu wadzipha
Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr2711.com.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Mawu oterewa ananenedwanso ndi Rebeka, Mose, Eliya ndi Yobu.—Genesis 25:22; 27:46; Numeri 11:15; 1 Mafumu 19:4; Yobu 3:21; 14:13.
^ ndime 5 Mayina m’nkhani ino asinthidwa.
^ ndime 7 Komabe dziwani kuti achinyamata ambiri amene ali ndi matenda okhudza maganizo sadzipha.
^ ndime 33 Kuti mumve zambiri pankhani ya mmene mungathetsere nkhawa, werengani nkhani yakuti “Kuthandiza Achinyamata Amene Akuvutika Maganizo,” mu Galamukani ya September 8, 2001, komanso yakuti “Kumvetsetsa Matenda a Maganizo,” mu Galamukani ya January 8, 2004.
ZOTI MUGANIZIRE
▪ Anthu amanena kuti kudzipha sikuthetsa mavuto, m’malomwake kumangokhala kusiyira ena mavutowo. Kodi zimenezi n’zoona?
▪ Kodi mungauze ndani ngati muli ndi nkhawa yadzaoneni?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 29]
MAWU KWA MAKOLO
M’mayiko ochuluka achinyamata ambiri akudzipha. Mwachitsanzo, ku United States pa zinthu zimene zimachititsa imfa za achinyamata a zaka 15 mpaka 25, kudzipha kuli pa nambala 3. Achinyamata a zaka 10 mpaka 14 amene amadzipha achuluka mowirikiza kawiri, kuyerekezera ndi zaka 20 zapitazo. Kwenikweni achinyamata amene ali pangozi yodzipha ndi amene ali ndi matenda a maganizo, amene m’bale wawo anadzipha komanso amene anayesapo kudzipha. Zizindikiro zina zosonyeza kuti wachinyamata akufuna kudzipha ndi izi:
▪ Kusiya kucheza ndi anthu am’banja lake kapena anzake
▪ Kusintha kadyedwe ndi nthawi yogona
▪ Kusiya kuchita zinthu zimene amakonda kuchita
▪ Kusintha kwambiri zochita zake
▪ Kuledzera ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo
▪ Kugawa katundu wake amene amam’konda kwambiri
▪ Kulankhulalankhula za imfa kapena nkhani zokhudza imfa
Dr. Kathleen McCoy anauza olemba magazini ino kuti makolo ambiri amakhala akulakwitsa kwambiri akamanyalanyaza zizindikirozi. Iye anati: “Palibe amene amafuna kuvomereza kuti mwana wake angakhale ndi vuto lofuna kudzipha, choncho makolo ena savomereza n’komwe zimenezi zikachitika. Iwo amangoti, ‘Ndi mmene zimakhalira munthu akafika msinkhu umenewu,’ kapena amati, ‘Asiya zimenezi,’ kapenanso amati, ‘Uyu n’kukhala kwake basi.’ Komatu maganizo amenewa ndi oopsa. Zinthu zimenezi sizofunika kuzinyalanyaza ngakhale pang’ono.”
Musachite manyazi kum’pezera thandizo mwana wanu amene wataya mtima kapena ngati ali ndi matenda osokonezeka maganizo. Ngati mukuona kuti mwana wanu akufuna kudzipha mufunseni bwinobwino. Si zoona kuti kukambirana nkhani yodzipha kumalimbikitsa munthuyo kudziphadi. Achinyamata ambiri amasintha maganizo akakambirana ndi makolo awo nkhaniyi. Ngati mwana wanuyo wavomera kuti akufuna kudzipha m’funseni bwinobwino kuti mudziwe ngati waganizira kale njira yodziphera. Akafotokoza mwatsatanetsatane mmene akufuna kudziphera, mudziwe kuti m’pofunika kuchitapo kanthu msanga. *
Musaganize kuti vuto lakelo lingathe lokha. Ndipo ngati lacheperapo musaganize kuti basi zili bwino. Akatswiri ena amanena kuti iyi ndiyo nthawi yoopsa kwambiri. N’chifukwa chiyani amatero? Dr. McCoy anati: “Wachinyamata amene wavutika maganizo kwambiri sangakhale ndi mphamvu zodziphera. Komano vutolo likachepa, amakhala ndi mphamvu moti angathe kudziphadi.”
Inde n’zachisoni kwambiri kuti achinyamata ena amafika poganiza zongodzipha chifukwa chovutika maganizo. Motero ndibwinodi kukhala maso kuona zizindikiro zoti munthu akufuna kudzipha ndiponso kuchitapo kanthu. Potero, makolo komanso akuluakulu ena angathe ‘kulankhula molimbikitsa kwa achinyamata amtima wachisoni’ komanso angakhale malo awo obisalapo.—1 Atesalonika 5:14.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 55 Akatswiri amachenjezanso kuti m’posavuta kuti achinyamata adziphe ngati m’nyumba mwawo muli mankhwala oopsa kapena mfuti. Pankhani ya mfuti, bungwe lina linati: “Ngakhale kuti anthu ambiri amati mfuti zawo ‘n’zodzitetezera,’ ambiri mwa anthu amene amafa ndi mfuti amachita kudzipha. Ndipo nthawi zambiri mfutiyo sikhala yawo.”—American Foundation for Suicide Prevention
[Chithunzi patsamba 28]
Kupemphera n’kofunika kwambiri kuposa kulankhulana ndi munthu wina aliyense