Ndinakopeka ndi Mboni za Yehova
Ndinakopeka ndi Mboni za Yehova
Yosimbidwa ndi Tomás Orosco
Tsiku loyamba limene ndinapita ku msonkhano wa Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu, ndinaona kamnyamata kakang’ono kakukamba nkhani. Ngakhale kuti samafikira bwinobwino patebulo lokambira nkhani, iye anakamba nkhaniyo mwaluso ndipo zimenezi zinandichititsa chidwi kwambiri.
M’NYUMBA ya Ufumu yonseyo anthu anali duu, kumvetsera mnyamatayo. Ineyo ndinali nditazolowera kupatsidwa ulemu chifukwa poyamba ndinali mkulu wa gulu lina la asilikali a dziko la Bolivia limene linatumizidwa kukagwira ntchito zaboma ku United States. Ndinagwiraponso ntchito ngati mkulu wa asilikali ku Bolivia komanso ndinali mlangizi wa zankhondo wa pulezidenti. Koma ulemu umene mnyamatayu analandira, unandipangitsa kuunikanso zolinga zanga pamoyo.
Bambo anga anamwalira kunkhondo mu 1934. Nkhondoyi inali ya pakati pa dziko la Bolivia ndi Paraguay ndipo ankalimbirana dera la Chaco. Nkhondo itatha, ndinatumizidwa ku sukulu ya Akatolika yogonera komweko. Kwa zaka zambiri, ndinkachita nawo mwambo wa Misa tsiku lililonse, ndipo tinkaimba nyimbo, kumvetsera katekizimu, ndiponso kunena mapemphero oloweza. Ndinali mnyamata wothandizira wansembe komanso ndinkaimba nawo kwaya. Komabe, sindinkawerenga Baibulo ndipo ndinali ndisanalionepo.
Ndinkakonda kwambiri zikondwerero za kutchalitchi chifukwa kunkakhala kudya ndi kusangalala. Koma ansembe ndiponso anthu ena amene ankatiphunzitsa anali ankhanza kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti ndisamawakonde. Ndipo ndinaganiza zosiya kuchita nawo zinthu zachipembedzo.
Ndinakopeka ndi Ntchito ya Usilikali
Tsiku lina dzuwa likuswa mtengo, kutauni ya kwathu ku Tarija kunabwera asilikali awiri achinyamata atavala bwino kwambiri. Iwo anachokera ku La Paz, mzinda waukulu ku Bolivia, ndipo anali patchuthi. Iwo ankayenda monyadira ntchito yawo ndipo ankaoneka olemekezeka. Anavala yunifomu yobiriwira komanso chipewa chakhonde chokhala ndi kamzera konyezimira. Zimenezi zinandikopa kwambiri ndipo nthawi yomweyo ndinaganiza zolowa usilikali. Ndinkaona kuti anyamatawa akusangalala ndi ntchito yawo ndipo ayenera kuti achita zinthu zambiri zotamandika.
Kenako mu 1949, ndinapita kukayamba maphunziro pasukulu ina yophunzitsa usilikali ku Bolivia. Panthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 16. Mchimwene wanga anandiperekeza popita kusukuluko, ndipo nditafika, ine ndi anyamata ena tinakhala pamzere wokaonana ndi msilikali wina waudindo. Mchimwene wanga anandidziwikitsa kwa msilikaliyo
ndipo anamuuza kuti ndine munthu wodalirika. Anamupemphanso kuti azindisamalira. Iye atachoka, msilikaliyo anandilonjera mwachisilikali. Anandimenya ndipo nditagwa pansi anandiuza kuti, “Tiona ngati uli wodalirikadi.” Apa m’pamene ndinadziwira kuti ku usilikali kulibe chibwana ndipo sikufunika anthu amantha. Komabe ndinapirira, ndipo ndinaphunzira kudzichepetsa.M’kupita kwa nthawi ndinaphunzira kumenya nkhondo ndipo ndinkalemekezedwa kwambiri. Koma nditagwira ntchitoyi kwa zaka zambiri, ndinaona kuti ili ndi mavuto ake ngakhale kuti imaoneka yolemekezeka.
Ndinapatsidwa Udindo Wapamwamba
Nditangoyamba kumene ntchito ya usilikali, ndinkaphunzirira mu sitima ya nkhondo ya pamadzi yotchedwa General Belgrano, yomwe inkanyamula asilikali oposa 1,000. Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse isanayambe, sitimayi inali ya dziko la United States ndipo inkadziwika ndi dzina lakuti USS Phoenix. Sitimayi inapulumuka, asilikali a ku Japan ataphulitsa bomba ku Pearl Harbor, mumzinda wa Hawaii, m’chaka cha 1941.
Patapita nthawi, ndinakhala m’maudindo osiyanasiyana mpaka kufika pa wachiwiri kwa msilikali amene ankayang’anira sitima yankhondo yapamadzi, yomwe inkalondera malire a dziko la Bolivia ndi mayiko ena. Sitimayi inkayenda mu mtsinje wa Amazon komanso m’nyanja ya Titicaca.
Kenako mu May 1980, ine ndi asilikali ena tinasankhidwa ndi boma la Bolivia kukagwira ntchito ku Washington, D.C., lomwe ndi likulu la dziko la United States. Gulu lililonse la asilikali, apamadzi, apamtunda ndiponso a mumlengalenga, linali ndi mtsogoleri wake. Popeza kuti ndinali nditagwira ntchito ya usilikali kwa zaka zambiri kuposa anzangawo, ndinasankhidwa kuti ndikhale mkulu woyang’anira magulu onsewo. Ndinakhala m’dziko la United States kwa zaka ziwiri ndipo kenako anandisankha kuti ndikhale mlangizi wa pulezidenti wa ku Bolivia pankhani za nkhondo.
Monga mkulu wa asilikali, ndinkafunikira kupita kutchalitchi Lamlungu lililonse. Koma ansembe ndiponso asilikali amene ankapempheretsa ankalimbikitsa nkhondo komanso moyo wogalukira ndipo zimenezi zinkandikhumudwitsa kwambiri. Ndinkadziwa ndithu kuti tchalitchi sichiyenera kulimbikitsa nkhondo. Koma zimene ankachita
akuluakulu achipembedzo sizinandichititse kusiya kupemphera, m’malomwake ndinayamba kufufuza choonadi chonena za Mulungu. Ndinali ndisanawerengepo Baibulo, koma tsopano ndinayamba kuliwerenga mwapatalipatali.Ku Nyumba ya Ufumu Kunkachitika Zinthu Zadongosolo
Mosayembekezereka, mkazi wanga Manuela anayamba kuphunzira Baibulo ndi m’mishonale wa Mboni za Yehova, dzina lake Janet. Kenako Manuela anayamba kupita ku misonkhano yawo ku Nyumba ya Ufumu. Nthawi zambiri ndinkamuperekeza pa galimoto koma ineyo sindinkafuna kuchita nawo misonkhanoyo chifukwa ndinkaganiza kuti imakhala yaphokoso.
Tsiku lina Manuela anandifunsa ngati ndingalole kuti mwamuna wa Janet, Ian, abwere kudzacheza nane. Poyamba sindinkafuna kuti abwere koma kenako ndinavomera. Ndinkaona kuti ndikudziwa zambiri zokhudza chipembedzo ndipo ndikhoza kumutsutsa chilichonse cholakwika chimene anganene. Iye atabwera, chimene chinandichititsa chidwi kwambiri ndi khalidwe lake, osati zimene ananena. Ian ankadziwa zambiri zokhudza Baibulo koma ankandilemekeza komanso ankasonyeza kuti ndi wokoma mtima. Ndipo ankayesetsa kuti asandichititse manyazi.
Mlungu wotsatira ndinaganiza zopita ku Nyumba ya Ufumu kumene ndinaona kamnyamata kakang’ono kakukamba nkhani, monga ndinafotokozera poyamba paja. Nditaona mmene anawerengera ndiponso kufotokoza malemba kuchokera m’buku la Yesaya, ndinazindikira kuti ndapeza chipembedzo choona. Ndili mwana ndinkafuna kudzakhala msilikali wolemekezeka, koma nditaona mnyamatayu ndinamusirira kwambiri ndipo ndinkafuna kuti nanenso ndizitha kuphunzitsa anthu Baibulo. Zimenezi zinachititsa kuti ndisinthe kwambiri n’kuyamba kutsatira zimene ndinkaphunzira.
M’kupita kwa nthawi, ndinayambanso kuchita chidwi ndi mmene a Mboni ankasungira nthawi pamisonkhano yawo. Iwo ankandipatsanso moni mosangalala ndipo ankachita zinthu zosonyeza kuti andilandira ndi mtima wonse. Ndinkachitanso chidwi ndi kavalidwe komanso ukhondo wawo. Chimene ndinkakondanso kwambiri ndi chakuti misonkhano yawo inkachitika mwadongosolo. Mwachitsanzo, nkhani imene yasonyezedwa pa ndandanda ndi imene inkakambidwadi pa tsikulo. Ndinkaona kuti iwo akuchita zinthu mwadongosolo osati chifukwa choopsezedwa ndi winawake koma chifukwa cha chikondi.
Nditangopezeka pa misonkhano kamodzi kokha, ndinavomera kuti Ian azindiphunzitsa Baibulo. Tinkaphunzira buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. * Ndimakumbukirabe mutu wachitatu wa m’buku limeneli womwe uli ndi chithunzi chosonyeza bishopu akudalitsa asilikali omwe ankakonzekera kupita kunkhondo. Sindinakaikire zimene bukuli limafotokoza chifukwa ndi zinthu zimene ndinaona ndi maso anga zikuchitika. Ku Nyumba ya Ufumu ndinalandirako buku lakuti Kukambitsirana za m’Malemba. Nditawerenga m’bukuli kuti Baibulo limaletsa Akhristu kumenya nawo nkhondo, ndinaona kuti ndiyenera kusintha. Ndinaganiza kuti ndisadzapitenso ku tchalitchi cha Katolika ndipo ndinayamba kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova nthawi zonse. Ndinaganizanso zosiya usilikali.
Ndinayamba Kulimbikira Kuti Ndibatizidwe
Patapita milungu ingapo, ndinamva kuti anthu a mu mpingowo adzapita kukakonza kubwalo la masewera kuti adzachitireko msonkhano. Ndinkafunitsitsa kudzapita kumsonkhanowo ndipo ndinapita kukagwira nawo ntchitoyo. Ndinasangalala kwambiri kugwira ntchitoyi komanso kucheza ndi anthu osiyanasiyana. Ndikusesa, mnyamata wina anabwera n’kundifunsa ngati ndinali mkulu wa asilikali.
Ndinamuyankha kuti, “Inde.”
Kenako iye ananena modabwa kwambiri kuti, “Sindinaonepo mkulu wa asilikali akusesa.” Iye sanakhulupirire kuona msilikali waudindo waukulu akutolatola zinyalala ndiponso kusesa. Munthuyu m’mbuyomo anali dalaivala wanga ndipo tsopano atakhala wa Mboni za Yehova.
Kugwirizana Chifukwa cha Chikondi
Ku usilikali, umapatsidwa ulemu chifukwa cha udindo umene uli nawo, ndipo zimenezi zinakhazikika m’maganizo mwanga. Mwachitsanzo, ndimakumbukira kuti ndinafunsapo ngati anthu ena a Mboni za Yehova ali apamwamba kuposa ena potengera udindo wawo kapena ntchito imene amagwira. Ineyo ndinkaona kuti kulemekezedwa komanso kukhala ndi udindo waukulu n’zofunika kwambiri, koma maganizo amenewa anadzasintha pasanapite nthawi yaitali.
Mu 1989, ndinamva kuti munthu wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova wochokera ku New York akubwera ku Bolivia ndipo akabwera adzakamba nkhani pabwalo la masewera lomwe tinakakonza lija. Ndinkayembekezera kuti iye adzapatsidwa ulemu waukulu. Ndinkaganiza kuti munthu waudindo waukulu chonchi akafika alandiridwa ngati pulezidenti.
Koma msonkhano utayamba, panalibe chilichonse chosonyeza kuti pafika munthu aliyense waudindo waukulu moti ndinayamba kuganiza kuti sanabwere. Pafupi ndi pamene ine ndi mkazi wanga Manuela tinakhala panali banja lina lachikulire. Manuela anaona kuti mkaziyo ali ndi nyimbo ya Chingelezi, choncho panthawi yopuma, Manuela anayamba kucheza naye. Atatha kucheza, banjalo linachoka pamene tinakhala.
Kenako ine ndi mkazi wanga tinadabwa kuona mwamuna wa mayiyo akupita pa pulatifomu kukakamba nkhani yaikulu pa msonkhanowo. Nditaona zimenezi, maganizo anga onse a ku usilikali okhudza udindo, ulemu ndiponso mphamvu anasintha. Panthawi ina ndinauza mkazi wanga kuti, “Sindimadziwa kuti m’bale amene tinayandikana naye pa mipando yachabechabe uja ndi wa m’Bungwe Lolamulira.”
Panopa ndimasangalala ndikakumbukira kuti Ian ankandithandiza mobwerezabwereza kuti ndimvetse mawu a Yesu a pa Mateyo 23:8 akuti: “Nonsenu ndinu abale.”
Kulalikira kwa Nthawi Yoyamba
Nditasiya ntchito ya usilikali, Ian anandipempha kuti ndipite naye kukalalikira kunyumba ndi nyumba. (Machitidwe 20:20) Dera limene tinapita kukalikira ndinkaliopa chifukwa kunali nyumba za asilikali zokhazokha. Ndipo nditagogoda pa nyumba yoyamba mkulu wa asilikali yemwe sindinkafuna nditakumana naye ndi amene anatsegula chitseko. Ndinachita mantha kwambiri, makamaka pamene iye anaona kuti ndili ndi chikwama komanso Baibulo. Anandifunsa mwamwano kuti, “Zimene ukuchitazi ndiye chiyani?”
Mwamsanga ndinapemphera chamumtima, ndipo ndinalimba mtima n’kuyamba kulankhula naye modekha. Mkuluyu anamvetsera zimene ndinkamuuza ndipo analandira mabuku ofotokoza za m’Baibulo amene ndinam’patsa. Zimenezi zinandilimbikitsa kuti ndidzipereke kutumikira Yehova. Ndipo pa January 3, 1990, ndinabatizidwa posonyeza kudzipereka kwanga.
M’kupita kwa nthawi, mkazi wanga, mwana wathu wamwamuna ndiponso wamkazi anabatizidwanso. Panopa ndili ndi mwayi wotumikira mumpingo wathu ngati mkulu komanso ndikuchita utumiki wa nthawi zonse wolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Koma mwayi waukulu umene ndili nawo ndi kudziwa Yehova ndiponso kudziwidwa ndi iye. Udindo uliwonse ku usilikali sungafanane ndi zimenezi. Ndipo ndaona kuti chikondi n’chimene chimafunika kuti zinthu zizichitika mwadongosolo, osati nkhanza ndiponso kusamva za ena. Yehova ndi Mulungu wadongosolo, koma chofunika kwambiri n’chakuti iye ndi Mulungu wachikondi.—1 Akorinto 14:33, 40; 1 Yohane 4:8.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 21 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, koma tsopano anasiya kulisindikiza.
[Chithunzi patsamba 13]
Ndili ndi mchimwene wanga Renato, mu 1950
[Chithunzi patsamba 13]
Ndikucheza ndi asilikali a ku China ndiponso mayiko ena pa mwambo winawake