Kodi Kugona Mokwanira N’kofunika Bwanji?
Kodi Kugona Mokwanira N’kofunika Bwanji?
● Kafukufuku wina amene anachitika posachedwapa anasonyeza kuti ku North America, anthu ambiri amagona maola 7 kapena 7.5 okha usiku uliwonse. * Kodi kugona mokwanira n’kofunika bwanji? Munthu akagona, nthawi ndi nthawi maso ake amayendayenda koma zikope zili zotseka. Zimenezi zimachitika usiku wonse pakatha mphindi 60 mpaka 90 zilizonse. Pa nthawi imeneyi, ubongo umakhala ukugwira ntchito kwambiri, ndipo akatswiri ochita kafukufuku akukhulupirira kuti umakhala ukudzikonzakonza. Akatswiri ena amanena kuti munthu akadukiza tulo pa nthawi imeneyi n’kusagonanso, thupi lonse limavutika. Ubongo sugwira ntchito bwino ndipo zimenezi zimachititsa kuti munthu asamagwirenso ntchito bwino, komanso munthuyo akhoza kudwala matenda osiyanasiyana.
Kumwa khofi kapena tiyi kukhoza kuchititsa kuti kwa kanthawi, munthu asamawodzere chifukwa chosagona mokwanira. Komabe, ngati sitinagone mokwanira, ubongo umatha kutichititsabe kuti tigone, ndipo zimenezi zimachititsa kuti tizigona kwa kanthawi kochepa kwambiri koma osadziwa. Nyuzipepala ina ya ku Canada inati: “Kaya munthu akuchita chiyani, ngati sanagone mokwanira, amagona mwadzidzidzi nthawi ndi nthawi, kwa masekondi 10 mpaka kupitirira mphindi imodzi nthawi iliyonse.” Ndiyeno tayerekezerani kuti mukuyendetsa galimoto pa liwiro la makilomita 50 pa ola ndipo mwagona mwadzidzidzi kwa masekondi 10. Pa nthawi imeneyi mungayende mtunda wautali kuposa utali wa bwalo la masewera a mpira, ndipo mukhoza kuchita ngozi. Kusagona mokwanira kungachepetsenso mphamvu ya thupi lanu yolimbana ndi matenda, chifukwa munthu akagona m’pamene thupi lake limapanga maselo amene amalimbana ndi tizilombo toyambitsa matenda. Tikagona m’pamenenso thupi lathu limapanga mankhwala amene amatithandiza kuti tizifuna kudya. Choncho kugona n’kofunika kwambiri kwa munthu mofanana ndi kuchita masewera olimbitsa thupi ndiponso kudya chakudya choyenerera.
Kodi mukulephera kugona mokwanira chifukwa chogwira ntchito kwa nthawi yaitali? Kapena kodi mumalephera kugona chifukwa cha kuda nkhawa ndi zinthu zimene zikuchitika pa moyo wanu panopa kapenanso chifukwa choopa kuti mudzavutika m’tsogolo? Pa nthawi ina, mfumu yanzeru Solomo inanena kuti: “Wotumikira munthu wina amagona tulo tokoma ngakhale adye zochepa kapena zambiri. Koma zambiri zimene munthu wolemera amakhala nazo zimamulepheretsa kugona.”—Mlaliki 5:12.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Onani nkhani za mu Galamukani! ya February 8, 2004 zonena za kugona tulo tosakwanira.