Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Chithunzichi Chalakwika Pati?

Werengani Machitidwe 9:36-41. Tchulani zinthu zitatu zimene zalakwika pachithunzichi. Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo malizitsani zithunzizi pozikongoletsa ndi chekeni.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi Tabita ankadziwikanso ndi dzina lina liti, ndipo mayina awiri onsewa amatanthauza chiyani?

ZOKUTHANDIZANI: Onani mawu am’munsi palemba la Machitidwe 9:36 mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika.

Kodi Tabita anali munthu wotani? Fotokozani.

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Machitidwe 9:36, 39.

Kodi mawu amene Yesu ananena pa Luka 6:38, anakwaniritsidwa bwanji kwa Tabita? Kodi mungatengere bwanji chitsanzo chake?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Aefeso 4:28; Yakobo 2:14-17.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Aliyense aganizire za munthu winawake amene angafune kumupatsa mphatso. Kenako konzani kamphatso kenakake koti mukapatse munthuyo. Mwachitsanzo, mungam’patse kakhadi kokhala ndi vesi la m’Baibulo.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 7 PETULO

MAFUNSO

A. N’chifukwa chiyani Petulo anayamba kumira?

B. Kodi mawu awa ndi oona kapena abodza? Petulo anali wosakwatira.

C. Atsogoleri achipembedzo atauza atumwi kuti asiye kulalikira, Petulo ndi atumwi ena anayankha kuti: “Ife tiyenera . . . “

[Tchati]

4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.

Kulengedwa Anakhala ndi moyo Baibulo

kwa Adamu zaka za pakati pa linamalizidwa

1 C.E ndi 100 C.E. kulembedwa

[Mapu]

Anakhala ku Betsaida ndi ku Kaperenao

GALILEYA

Kaperenao

Betsaida

Nyanja ya Galileya

PETULO

ANALI NDANI?

Anali msodzi wakhama amene anali mmodzi wa anthu oyambirira kukhala ophunzira a Yesu. Yesu anasankha Petulo kuti akhale mmodzi wa atumwi 12. Mabuku anayi a Mauthenga Abwino analemba zambiri zokhudza Petulo kuposa za mtumwi wina aliyense. Yehova anamugwiritsa ntchito kwambiri kulalikira ndiponso ‘kulimbikitsa abale ake.’—Luka 22:32; Maliko 3:13-19.

MAYANKHO

A. Ankakayikira.—Mateyu 14:28-31.

B. Abodza.—Maliko 1:29-31; Yohane 1:42; 1 Akorinto 9:5.

C. “. . . kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”—Machitidwe 5:18, 27-29.

Anthu ndi Mayiko

4. Dzina langa ndine Antonia. Ndili ndi zaka 8 ndipo ndimakhala m’dziko Chile, ku South America. Kodi ku Chile kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 69,500; 96,500 kapena 106,500?

5. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ineyo ndimakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Chile.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba  23

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Petulo sanapemphere ataimirira; anagwada.

2. Azimayi (amasiye) anasonyeza Petulo zovala zimene Tabita anasoka, osati miphika.

3. Petulo anali yekha popemphera m’chipindamo, osati ndi anthu ena.

4. 69,500.

5. B.