Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI | BRETT SCHENCK

“Sindimakayikiranso Zoti Mulungu Analenga Zamoyo”

“Sindimakayikiranso Zoti Mulungu Analenga Zamoyo”

Brett Schenck ankagwira ntchito yosamalira zachilengedwe ku United States koma pano anapuma pantchito. Ntchito yake inali yofufuza mmene nyama ndi zomera zimadalirana. Koma n’chiyani chinam’pangitsa kuti azikhulupirira kuti Mulungu ndi amene analenga zamoyo zonse? Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe za chikhulupiriro chake komanso za ntchito yake.

Tiuzeni za moyo wanu.

Ndinakulira ku New Paris, mumzinda wa Ohio ku America. Bambo anga ankagwira ntchito yokonza makina osiyanasiyana. Ndili mwana bambo ankakonda kundiuza zambiri zokhudza masamu ndi sayansi. Ndinkachita chidwi ndi zinyama komanso zomera zomwe zinkapezeka m’madzi komanso m’madamu omwe anali kufupi ndi kwathu. Ndiye nditapita ku yunivesite ya Purdue, ndinayamba kuphunzira sayansi ya mmene zamoyo zimadalirana kuti zikhale ndi moyo.

Kodi munkapita kutchalitchi?

Eya ndinkapita. Bambo anga ankandilimbikitsa kuti ndizipita ku tchalitchi cha Lutheran. Ndinaphunzira Chigiriki cha anthu wamba, chimene anagwiritsa ntchito polemba Baibulo. Chifukwa cha zimenezi ndinkalemekeza kwambiri Baibulo.

Kodi munkakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha?

Ee, ndinkakhulupirira zimenezo chifukwa ndi zimene ankaphunzitsa ku tchalitchi kwathu. Komanso n’zimene anzanga onse ankakhulupirira. Koma ndinkakhulupiriranso kuti kuli Mulungu. Ndinkaganiza kuti ziphunzitso ziwirizi n’zogwirizana. Komabe ngakhale kuti ndinkalemekeza kwambiri Baibulo, sindinkaganiza kuti analilemba ndi Mulungu.

Munayamba bwanji kukhulupirira Baibulo?

Tsiku lina kunyumba kwanga kunabwera anthu awiri a Mboni za Yehova. Mayina awo ndi Steve ndi Sandy, ndipo anandipeza ndili ndi mkazi wanga Debbie. Anationetsa umboni wochokera m’Baibulo wosonyeza kuti zimene limanena pa nkhani zasayansi ndi zolondola. Mwachitsanzo, anatisonyeza zimene Baibulo limanena kuti: “Pali Winawake amene amakhala pamwamba pa dziko lapansi lozungulira.” (Yesaya 40:22) Limanenanso kuti: “Iye . . . anakoloweka dziko lapansi m’malere.” (Yobu 26:7) Pa nthawi imeneyi ndinkagwiritsa ntchito zithunzi zojambulidwa mlengalenga kuti ndizidziwa zambiri zokhudza nyama ndi  zomera. Choncho ndinamvetsa mosavuta zimene ndinawerenga m’Baibulozi ndipo zinandigwira mtima kwambiri. Mawu a m’Baibulowa analembedwa kalekale, asayansi asanatulukire kuti dzikoli ndilozungulira komanso kuti lili m’malere. Ine ndi mkazi wanga titayamba kuphunzira Baibulo ndi Steve komanso Sandy, ndinaphunzira maulosi a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa, ndinapeza malangizo othandiza komanso ndinamvetsa mfundo zina zomwe sindinkazimvetsa poyamba. Zimenezi zinandithandiza kuti ndizikukhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu.

Munayamba liti kukhulupirira kuti zinthu zonse zinachita kulengedwa?

Tsiku lina Steve anandionetsa zimene Baibulo limanena kuti: “Yehova Mulungu anaumba munthu kuchokera kufumbi lapansi.” (Genesis 2:7) Zimenezi zinandithandiza kudziwa kuti Baibulo limafotokoza zimene Mulungu anachita kuti munthu akhale ndi moyo. Zimenezi zinandichititsa kudzifunsa kuti: Kodi zimene Baibulo limanena zimagwirizana ndi sayansi? Steve anandilimbikitsa kuti ndifufuze ndipo ndinafufuzadi.

Ndiye mutafufuza munapeza zotani?

Ndinapeza zinthu zambiri. Mwachitsanzo, asayansi amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha amalephera kufotokoza momveka bwino mmene moyo wa zolengedwa zosiyanasiyana unayambira. Nyama iliyonse imayenera kukhala ndi ziwalo zofunika monga mtima, mapapu komanso maso kuti ikhale ndi moyo. Pogwiritsiranso ntchito makina oonera zinthu zing’onozing’ono, timatha kuona maselo amene anapangidwa mochititsa chidwi kwambiri. Koma funso ndi lakuti, kodi maselo amenewa amachokera kuti? Asayansi amene amati zamoyo zinachita kusintha amakhulupirira kuti zamoyo zokhazo zimene zili ndi mphamvu kwambiri komanso zimene zili ndi maselo ogometsawo, n’zimene zimapitirizabe kukhala ndi moyo. Komabe mfundo imeneyi siiyankha funsolo. Ndinapezanso kuti asayansi ambiri amadziwa kuti chiphunzitsochi sichiyankha funso limeneli. Katswiri wina woona za nyama zosungidwa ku malo osungira nyama anandiuza yekha kuti sakhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha. Kungoti sanganene zimenezi poyera chifukwa akhoza kuchotsedwa ntchito.

Kodi zimene munaphunzira kuyunivesite zinakuthandizani bwanji?

Monga ndanenera kale, ntchito yanga inali yoona mmene zamoyo zimadalirana kuti zikhale ndi moyo. Chamoyo chilichonse padziko lapansi chimadalira chinzake kuti chikhale ndi moyo. Mwachitsanzo, maluwa ndi njuchi zimadalirana. Maonekedwe, kununkhira komanso timadzi ta m’maluwa tinapangidwa kuti tizikopa njuchi. Njuchizo zikatera pa maluwapo zimasiyapo mungu. Zimayamwanso timadzi ta m’maluwawo ndi mungu wake n’kukaika pa maluwa ena zomwe zimathandiza kuti maluwawo apange njere.

‘Ndikaona mmene chilengedwe chimadzikonzera chokha, sindikayikira kuti zamoyo zonse zinalengedwa ndi Mulungu’

M’chilengedwe muli zinthu zambiri zimene zimadalirana. Mwachitsanzo, m’nkhalango mumapezeka nyama, zomera, mabakiteriya ndi tizilombo ting’onoting’ono tamitundu yosiyanasiyana. Nyama zonse zimadalira zomera kuti zizipeza zakudya komanso mpweya wabwino ndipo zomera zomwe zimapanga maluwa zimadalira nyama. Ngakhale kuti m’chilengedwe muli zamoyo zambiri, zomwe zina ndi zing’onozing’ono komanso zofooka, zikhoza kukhalabe ndi moyo kwa zaka zambiri. Mwachitsanzo, ngati zamoyo zina zitafa chifukwa cha mpweya woipa wochokera m’mafakitale, zamoyo zina zimayamba kupezeka makampaniwo akasiya kutulutsa mphweya woipawo. Ndiye ndimati ndikaona mmene chilengedwe chimadzikonzera chokha, sindikayikira kuti zamoyo zonse zinachita kulengedwa ndi Mulungu.

N’chiyani chinakupangitsani kuti mukhale wa Mboni za Yehova?

Ndimakhudzidwa kwambiri ndi mmene anthu akuwonongera chilengedwe. N’zoona kuti chilengedwe chimatha kudzikonzanso chokha koma chikhoza kuwonongekeratu ngati anthu atapitiriza kuchiwononga. Ndinaphunzira kuchokera m’Baibulo kuti Mulungu adzawononga “amene akuwononga dziko lapansi.” (Chivumbulutso 11:18) Mawu amenewo anandisangalatsa kwambiri. Pamene ndinkaphunzira Baibulo ndinazindikira kuti zonse zimene Baibulo limalonjeza zidzachitikadi.

Ndimasangalala kwambiri kuuza ena zimene ndimakhulupirira ndipo ndaphunzitsa Baibulo akatswiri ena asayansi. Nditakwanitsa zaka 55, ndinapuma pa ntchito n’cholinga choti ndizikhala ndi nthawi yambiri yothandiza anthu kumudziwa bwino Mlengi wa zamoyo zonse komanso kuti adziwe zinthu zabwino zimene akufuna kudzachitira anthu.