Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Halowini N’chiyani?

Kodi Halowini N’chiyani?

Ku United States komanso ku Canada, mwambo wa Halowini ndi wotchuka kwambiri ndipo umachitika chaka chilichonse pa 31 October. Koma zimene zimachitika pa mwambowu zimachitikanso m’madera ena padziko lonse ngakhale kuti umadziwika ndi dzina lina. Pa nthawi ya mwambowu anthu amakhala ndi maholide ndipo amachita zinthu zosonyeza kuti akulankhulana ndi akudziko la mizimu kuphatikizapo mizimu ya anthu akufa, afiti, ziwanda ndi mizukwa.—Onani bokosi lakuti  “Zikondwerero Zofanana ndi Mwambo wa Halowini.”

ANTHU ena samakhulupirira mizimu koma amachita nawo mwambo umenewu kuti angopeza mpata wosangalala. Koma ena amaona kuti mwambo umenewu siwabwino pa zifukwa zotsatirazi:

  1. Buku lina linanena kuti “Mwambo wa Halowini umakhudzana kwambiri ndi kulankhulana ndi mizimu imene imaopseza anthu.” (Onani bokosi lakuti  “Mmene Halowini Inayambira.”) Zikondwerero zambiri zofanana ndi Halowini zinayamba ndi anthu osalambira Mulungu ndipo zimakhudzana kwambiri ndi kulambira anthu akufa. Masiku anonso, anthu akamachita  zikondwerero zimenezi amaganiza kuti akulankhulana ndi mizimu ya akufa.—Encyclopedia of American Folklore.

  2. Ngakhale kuti mwambo wa Halowini umaoneka kuti ndi wa ku America kokha, mayiko ambiri ayamba kuchita mwambo umenewu. Koma anthu ambiri sadziwa mmene mwambowu unayambira. Sadziwanso zimene zizindikiro, zokongoletsera komanso miyambo imene imachitika pa mwambowu zimatanthauza. Ndipo miyambo imene imachitika pa mwambowu imakhudzana ndi za mizimu.—Onani bokosi lakuti  “Kodi Zimaimira Chiyani?”

  3. Anthu ambiri okhulupirira za ufiti, omwe amatsatirabe miyambo ya Aselote, amatchulabe mwambo wa Halowini ndi dzina lake loyambirira lakuti Samhain. Iwo amaona kuti tsikuli ndi lapadera kwambiri pachaka chonse. Nyuzipepala ina, yotchedwa USA Today, inalemba zimene munthu wina, yemwe ankati ndi mfiti ananena. Munthuyo anati: “Akhristu sadziwa kuti akamachita nawo zikondwerero zimenezi, amakhala akuthandiza afiti kuchita mwambo umenewu. . . . Zimenezi zimatisangalatsa kwambiri.”

  4.   Zikondwerero zimenezi sizigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Baibulo limatichenjeza kuti: “Pakati panu pasapezeke munthu . . . wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa.”—Deuteronomo 18:10, 11; onaninso Levitiko 19:31; Agalatiya 5:19-21.

Malinga ndi zimene takambiranazi, tsopano mwadziwa mmene mwambo wa Halowini ndi zikondwerero zina, zofanana ndi mwambowu, zinayambira. Zimenezi zingakuthandizeni kupewa kuchita nawo zikondwerero zimenezi.

“Akhristu sadziwa kuti akamachita nawo zikondwerero zimenezi, amakhala akuthandiza afiti kuchita mwambo umenewu. . . . Zimenezi zimatisangalatsa kwambiri.”—Mawu amenewa analembedwa m’nyuzipepala ina, yotchedwa USA Today, omwe munthu wina, yemwe ankati ndi mfiti ananena

^ ndime 37 Mawu akuti “Halo” ankatanthauza “oyera.” Tsiku la Oyera Mtima ndi tsiku limene ankakumbukira oyera mtima amene anamwalira. Madzulo a tsiku limeneli ndi amene anayamba kutchedwa kuti Halowini.