NKHANI YA PACHIKUTO
Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala?
“Ndikadzakhala pa banja n’kukhala ndi ana, ndidzasangalala kwambiri.”
“Ndikadzakhala ndi nyumba yangayanga, ndidzasangalala kwambiri.”
“Nditapeza ntchito imeneyi, ndingasangalale kwambiri.”
“Ndidzasangalala ndikadza . . . ”
KODI inunso munakhalapo ndi maganizo amenewa? Ndiye mutapeza zimene munkafunazo, munakhala wosangalala kwa nthawi yaitali bwanji? N’zoona kuti munthu ukapeza zomwe umalakalaka, umasangalala. Komabe chisangalalo chimenechi sichikhala cha nthawi yaitali. Zili choncho chifukwa chisangalalo chenicheni sichichokera pa zimene munthu wakwanitsa kuchita kapena zomwe ali nazo. Chisangalalo chenicheni tingachiyerekeze ndi kukhala ndi thanzi labwino. Kuti munthu akhale ndi thanzi labwino pamafunika zambiri. Choncho kuti munthu akhaledi wosangalala, pamafunikanso zambiri.
Anthufe ndife osiyanasiyana. Zimene zingapangitse kuti inuyo mukhale wosangalala, wina sizingamusangalatse. Komanso zinthu zimene timakonda zimasintha tikamakula. Komabe pali umboni wosonyeza kuti pali zinthu zina zomwe nthawi zonse zimathandiza munthu kukhala wosangalala. Mwachitsanzo, munthu amene amakhala wokhutira ndi zomwe ali nazo, amapewa mtima wakaduka, amakonda anthu komanso sakhumudwa kwambiri akakumana ndi mavuto amakhala wosangalala nthawi zonse. Tiyeni tione chifukwa chake zili choncho.
1. MUZIKHUTIRA NDI ZIMENE MULI NAZO
“Mfumu Solomo ya ku Isiraeli, yomwe inkadziwa kwambiri zochita za anthu, inanena kuti: ‘Ndalama zimateteza.’ Komatu Solomo ananenanso kuti: “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza. Zimenezinso n’zachabechabe.” (Mlaliki 5:10; 7:12) Kodi Solomo ankatanthauza chiyani? Anthufe timafunika ndalama kuti tipeze zinthu zofunika. Komabe tiyenera kupewa mtima wadyera chifukwa umapangitsa kuti tisamakhutire ndi zomwe tili nazo. Solomo anayesapo kuti aone ngati ndalama zambiri komanso kukhala moyo wawofuwofu kungapangitse munthu kukhala wosangalala. Iye anati: “Chilichonse chimene maso anga anali kupempha sindinali kuwamana. Mtima wanga sindinaumane chosangalatsa cha mtundu uliwonse.”—Mlaliki 1:13; 2:10.
Solomo anali munthu wolemera kwambiri. Iye anali ndi ndalama zambiri, nyumba zikuluzikulu, minda yamaluwa yokongola, madamu komanso antchito ambiri. Ankapeza chilichonse chimene akufuna. Koma kodi zinthu zonsezi zinamuthandiza kukhaladi wosangalala? N’zoona kuti ankasangalala, komabe chisangalalo chake chinali chakanthawi. Iye anati: “Ndinaona kuti zonse zinali zachabechabe. . . . Padziko lapansi pano panalibe chaphindu chilichonse.” (Mlaliki 2:11, 17, 18) Apatu Solomo anasonyeza kuti moyo womangokhalira kufuna kupeza zofuna zako, umachititsa kuti usamakhutire ndi zomwe uli nazo komanso kuti uzikhala wosasangalala. *
Kodi zimene akatswiri apeza masiku ano zikugwirizana ndi zomwe Solomo ananenazi? Inde. Mwachitsanzo, nkhani yomwe inatuluka m’magazini ina inati: “Munthu akakhala ndi zinthu zofunika pa moyo, zomwe ndi chakudya, malo ogona komanso zovala, akhoza kukhala wosangalala. Koma anthu ambiri amaganiza kuti munthu atakhala ndi zinthu zambiri kuwonjezera pamenepa akhoza kukhala wosangalala kwambiri. Koma zimenezi si zoona.” (Journal of Happiness Studies) Kafukufuku amasonyeza kuti munthu amene amangokhalira kufunafuna chuma, amakhala wosasangalala makamaka ngati zimenezi zikumulepheretsa kuchita zinthu zauzimu komanso ngati zikumupangitsa kukhala wosaona mtima.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.”—Aheberi 13:5.
2. MUSAMACHITE KADUKA
Mawu akuti kaduka amatanthauza “kuwawidwa mtima komanso kuipidwa chifukwa cha zinthu zabwino zimene munthu wina ali nazo n’kumalakalaka zinthuzo zitakhala zako.” Khalidwe la kaduka tingaliyerekeze ndi chotupa chomwe chimakula ndipo chimapangitsa munthu kukhala wosasangalala mwinanso kufa kumene. Kodi khalidweli limayamba bwanji? Nanga tingadziwe bwanji ngati tili nalo? Ndipo kodi tingalithetse bwanji?
Buku lina linanena kuti nthawi zambiri munthu amachitira kaduka anthu ofanana nawo pa zinthu zina. Zinthu zake zingakhale monga zaka, zimene akudziwa komanso zimene amachita. Mwachitsanzo, munthu amene amagulitsa malonda sangachitire kaduka katswiri wa mafilimu. Koma akhoza kuchitira kaduka wamalonda mnzake, yemwe zinthu zikumuyendera bwino.
Zoterezi n’zimenenso zinachitika ku Perisiya. Akuluakulu a boma sankachitira kaduka mfumu. Koma ankachitira kaduka Danieli, yemwe anali mkulu mnzawo wa boma. Ankamuchitira kaduka chifukwa choti zinthu zinkamuyendera bwino kuposa iwowo. Anthuwa anakwiya kwambiri ndi Danieli moti mpaka anakonza chiwembu choti aphedwe. Koma chiwembu chawocho chinalephereka. (Danieli 6:1-24) Buku lija linanenanso kuti: “Munthu wakaduka amalakalaka kuti munthu amene akumuchitira kadukayo akumane ndi mavuto. N’chifukwa chake anthu ambiri amene anazunzidwa kapena kuphedwa anali oti ankachitiridwa kaduka.” *
Kaduka angapangitse kuti munthu asamasangalale ndi zinthu zabwino pa moyo
Kodi mungadziwe bwanji ngati muli ndi kaduka? Dzifunseni kuti: ‘Kodi munthu wina zinthu zikakhala kuti zikumuyendera, ndimasangalala kapena ndimakhumudwa? M’bale wanga, munthu wa m’kalasi mwathu kapena munthu wa kuntchito kwathu zikakhala kuti sizikumuyendera, kodi ndimadandaula kapena ndimasangalala?’ Ngati pa funso loyambalo mwayankha kuti “ndimakhumudwa” ndipo lachiwirilo mwayankha kuti “ndimasangalala,” n’kutheka kuti muli ndi kaduka. (Genesis 26:12-14) Buku lina linafotokoza kuipa kwa khalidwe la kaduka. Linati: “Kaduka angapangitse kuti munthu asamasangalale ndi zinthu zabwino pa moyo komanso kuti asamayamikire zabwino zomwe ali nazo. . . . Zimenezi zingapangitse kuti munthu azikhala wosasangalala.”—Encyclopedia of Social Psychology.
Kodi tingathetse bwanji khalidwe la kaduka? Tiyenera kukhala odzichepetsa. Kudzichepetsa kumatithandiza kuti tiziona makhalidwe abwino a anthu ena komanso kuti tiziyamikira zomwe amachita. Baibulo limati: “Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.”—Afilipi 2:3.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.”—Agalatiya 5:26.
3. MUZIKONDA ANTHU
Buku lija linanenanso kuti: “Munthu akamagwirizana ndi anthu amakhala wosangalala kwambiri. Amaposa munthu yemwe ali pa ntchito yabwino, ali ndi ndalama zambiri kapenanso ali ndi thanzi labwino koma sagwirizana ndi anthu.” Mwachidule tingati, kuti munthu akhale wosangalala amafunika kuti azikonda anthu komanso azikondedwa. Munthu wina amene analemba nawo Baibulo anati: “Ngati . . . ndilibe chikondi, sindili kanthu.”—1 Akorinto 13:2.
Ngakhale munthu amene poyamba sankakondedwa komanso sanaphunzire kukonda anthu, akhoza kuyamba kuchita zimenezi. Mwachitsanzo mtsikana wina, dzina lake Vanessa, bambo ake anali ankhanza komanso chidakwa. Vanessa ali ndi zaka 14, anachoka panyumba ndipo ankangokhala m’nyumba za anthu. Kenako anayamba kukhala pamalo ena osalongosoka ndipo pa nthawiyi anapempha Mulungu kuti amuthandize. Patapita nthawi anayamba kukhala ndi banja lina lomwe linkatsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.” (1 Akorinto 13:4) Apa Mulungu anayankha pemphero lake. Kukhala kunyumba imeneyi komanso kuphunzira Baibulo, kunathandiza Vanessa kuti ayambe kukhala wosangalala. Kunamuthandizanso kuti aiwale nkhanza zomwe bambo ake ankamuchitira komanso kuti ayambe kukhoza kusukulu. Iye anati: “Poyamba ndinkangolephera koma ndinayamba kukhoza bwino kwambiri.”
Vanessa amakumbukirabe nkhanza zomwe wakumana nazo pa moyo wake. Komabe pano iye anakwatiwa ndipo ali ndi ana awiri aakazi. Banja lake ndi losangalala kwambiri.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”—Akolose 3:14.
4. MUSAMAKHUMUDWE KWAMBIRI MUKAKUMANA NDI MAVUTO
Aliyense amakumana ndi mavuto. Ndipotu Baibulo limati pali “nthawi yolira” komanso “nthawi yolira mofuula.” (Mlaliki 3:4) Choncho mukakumana ndi mavuto, muziyesetsa kuti musangokhala wokhumudwa. Izi zingakuthandizeni kuti muthe kupirira. Taganizirani chitsanzo cha Carol komanso Mildred.
Carol ali ndi vuto la msana, matenda a shuga, amavutika kugona komanso ali ndi vuto la maso lomwe linachititsa kuti diso lake lakumanzere lichite khungu. Komabe iye anati: “Ndimayesetsa kuti ndisamangokhala wokhumudwa. Ndimadziwa kuti ndili pa mavuto. Komabe ndimapewa kumangoganizira za mavuto anga. Ndipo ndimathokoza Mulungu chifukwa cha zinthu zomwe ndimakwanitsa kuchita, makamaka pothandiza ena.”
Nayenso Mildred ali ndi matenda osiyanasiyana monga nyamakazi, khansa ya m’mawere komanso matenda a shuga. Iye anati: “Ndimayesetsa kukonda anthu komanso kulimbikitsa omwe akudwala ndipo zimenezi zimandithandiza kwambiri. Ndimaonanso kuti kulimbikitsa ena kumachititsa kuti ndisamadandaule kwambiri za mavuto anga.”
Ngakhale kuti Carol ndi Mildred amafunitsitsa kupeza thandizo labwino la kuchipatala, sikuti amangoganizira za matenda awo. M’malomwake amaganizira kwambiri za zimene angachite kuti azikhalabe osangalala komanso mmene angathandizire anthu ena. Zimenezi zawathandiza kuti akhale ndi mtendere wa mumtima. Komanso anthu ambiri amawakonda ndipo amatengera chitsanzo chawo cha kupirira.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Wodala [kapena kuti wosangalala] ndi munthu wopirira mayesero, chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira mphoto ya moyo.”—Yakobo 1:12.
Malangizo a m’Baibulo ali “ngati mtengo wa moyo” ndipo amene amawatsatira amakhala “odala” kapena kuti osangalala. (Miyambo 3:13-18) Tikukupemphani kuti nanunso muzitsatira malangizo a m’Baibulo kuti muone umboni wosonyeza kuti zimenezi n’zoona. Baibulo limati Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe” ndipo iye amafuna kuti nanunso mukhale wosangalala.—1 Timoteyo 1:11.
^ ndime 11 Nkhani yonena za zimene Solomo anachita ikupezeka pa Mlaliki 2:1-11.
^ ndime 17 Chitsanzo cha anthu oterewa ndi Yesu Khristu. Lemba la Maliko 15:10 limati, “ansembe aakulu anamupereka chifukwa cha kaduka” kuti aphedwe.