NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MFUNDO ZA M’BAIBULO N’ZOTHANDIZABE MASIKU ANO?
Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Kukhulupirika M’banja
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa.”—Aheberi 13:4.
UBWINO WOKHALA OKHULUPIRIKA M’BANJA: Anthu ena amati kukhala wokhulupirika m’banja ndi kwachikale. Koma limeneli ndi bodza lankunkhuniza. Pa nthawi imene Baibulo linkalembedwa, mwamuna kapena mkazi akachita zosakhulupirika, mnzakeyo ankakhumudwa kwambiri. Zimenezi n’zimenenso zimachitika masiku ano.—Miyambo 6:34, 35.
Jessie, yemwe ndi mwamuna wapabanja komanso ali ndi ana, anati: “Kukhala wokhulupirika m’banja kwathandiza kuti ine ndi mkazi wanga tizikondana kwambiri ndiponso kuti tizikhala mosangalala. Tonse timayesetsa kupewa kuchita zinthu zomwe zingachititse kuti tizikayikirana.” Kusakhulupirika m’banja kumapangitsa kuti anthu asamakhulupirirane, zomwe zingachititse kuti banja lithe n’kuzunzitsa ana.
Ligaya * anachita zinthu zomwe zikanawonongetsa banja lake. Iye anati: “Ndinayamba kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa. Zimenezi zinachititsa kuti ndizipita kumabala ndi kumadansi usiku n’kumachita chiwerewere.” Kodi khalidwe lakeli linamuthandiza kuti azisangalala? Ayi ndithu. Iye anali munthu wosasangalala ndipo ankangokhalira kukangana ndi mwamuna wake. Ligaya anati: “Nditaona kuti banja langa silikuyenda bwino chifukwa cha khalidwe langa, ndinakumbukira zomwe makolo anga ankandiuza. Ankakonda kunena kuti: ‘Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.’”—1 Akorinto 15:33.
Ligaya ananenanso kuti: “Zinthu zisanafike poipa ndinaganiza zosiya khalidwe langa loipa ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo n’kumatsatira zomwe ndinkaphunzirazo.” Zimenezi zinapulumutsa banja lake ndipo mwamuna wake anayamba kumukonda ndi kumulemekeza. Ligaya anati: “Baibulo linandithandiza kwambiri. Ndimaona kuti ndinachita bwino kwambiri kusintha komanso kusiya kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa.”
^ ndime 6 Mayina ena asinthidwa.