Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Mongolia

Dziko la Mongolia

ZAKA za m’ma 1100, msilikali wina wolimba mtima dzina lake Genghis Khan anagonjetsa madera ena amene anadzakhala ufumu wa Mongol. Ufumuwu unali waukulu koma panopa kachigawo kochepa chabe ka pakati pa Russia ndi China n’kamene kamatchedwa Mongolia. Dziko limeneli ndi la anthu ochepa kwambiri.

M’dzikoli muli zidikha, mapiri ataliatali ndiponso mitsinje. Chakum’mwera kuli chipululu chotchedwa Gobi ndipo kumeneko anthu anapeza mafupa a zinyama zikuluzikulu zakalekale. Malo ambiri m’dzikoli ndi okwera ndipo kumakhala kopanda mitambo masiku oposa 250 pa chaka. N’chifukwa chake anthu a kumeneko amanena kuti ndi “Dziko la Kumwamba kwa Buluu.”

Kambuku

Nyengo imasintha kwambiri m’dzikoli. M’miyezi ina kumatentha kufika madigiri seshasi 40 pomwe m’miyezi ina kumazizira kufika -40. Moyo wa anthu pafupifupi 1 miliyoni m’dzikoli ndi wongoyendayenda. Akadzuka m’mawa, amayamba ndi kukama mkaka wa mbuzi, ng’ombe, ngamila ndi mahatchi. Amakonda kudya nyama ndi zinthu zopangidwa kuchokera ku mkaka. Nyama imene amaikonda kwambiri ndi ya nkhosa.

Ayanika makeke opangidwa kuchokera ku mkaka

Anthu ake amalandira bwino alendo. Amakhala m’matenti koma satseka pakhomo kuti munthu aliyense wodutsa alowe n’kupuma komanso kudya zimene angafune. Alendo amakonda kuwaphikira tiyi wamkaka wothira kamchere pang’ono.

Anthu ambiri kumeneku ndi Abuda. Kulinso anthu ena a Chisilamu, Chishama ndi Chikhristu koma ena alibe chipembedzo. M’dzikoli muli a Mboni za Yehova oposa 350 amene amaphunzitsa Baibulo anthu oposa 770.

Ngamila za malinunda awiri zimanyamula katundu ngakhale kutazizira kwambiri