MAVUTO A M’DZIKOLI
2 | Muzisamala Ndalama
CHIFUKWA CHAKE ZILI ZOFUNIKA
Tsiku lililonse, anthu ambiri amavutika kuti apeze zinthu zofunika pa moyo. N’zomvetsa chisoni kuti mavuto a m’dzikoli angawachititse kuti azivutika kwambiri. Chifukwa chiyani?
-
Kukakhala mavuto, zinthu monga zakudya komanso nyumba zimakhala zodula kwambiri.
-
Mavuto akachuluka, anthu ambiri amachotsedwa ntchito kapenanso malipiro amachepetsedwa.
-
Kukachitika ngozi zam’chilengedwe, mabizinesi amasokonekera komanso nyumba ndi katundu wina amawonongeka, ndipo zimenezi zimachititsa kuti anthu akhale pa umphawi.
Zimene Muyenera Kudziwa
-
Mukamagwiritsa ntchito bwino ndalama, sizingadzakuvuteni mukadzakumana ndi mavuto.
-
Kupeza ndalama zambiri, kusunga ndalama komanso kukhala ndi katundu wambiri, nthawi zina n’kosadalirika chifukwa zimatha mphamvu.
-
Pali zinthu zina zimene ndalama sizingagule monga kukhala wosangalala komanso kukhala ndi banja logwirizana.
Zimene Mungachite Panopa
Baibulo limanena kuti: “Pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.”—1 Timoteyo 6:8.
Kukhala wokhutira kumaphatikizapo kudziikira malire pa zimene tikufuna, n’kumakhala wokhutira ndi zimene timafunikiradi tsiku ndi tsiku. Zimenezi n’zofunika kwambiri makamaka tikakhala kuti tikukumana ndi mavuto azachuma.
Kuti mukhale okhutira mumafunika kusintha zimene mumachita pa moyo wanu. Mukamafuna kukhala moyo wapamwamba woposa ndalama zimene mumapeza, mavuto anu azachuma sangathe.