Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUSINTHA ZOMWE MUNAZOLOWERA?

3 Musafulumire Kugwa Ulesi

3 Musafulumire Kugwa Ulesi

Katswiri wina ananena kuti munthu amayamba kuzolowera zinthu zatsopano pambuyo pa masiku 21. Komabe, ofufuza ena anapeza kuti anthu ena angayambe kuzolowera zinthu zatsopano mwamsanga poyerekezera ndi ena. Koma kodi zimenezi ziyenera kukugwetsani ulesi?

Taganizirani izi: Tiyerekeze kuti mukufuna kuzolowera kumachita masewera olimbitsa thupi katatu pa mlungu.

  • Mlungu woyamba mwakwanitsa masiku onse atatu.

  • Mlungu wachiwiri mwaphonya tsiku limodzi.

  • Mlungu wachitatu mwakwanitsa masiku onse atatu.

  • Mlungu wachinayi mwaphonya masiku awiri.

  • Mlungu wa 5 mwakwanitsa masiku onse kenako mukupitiriza osaphonyanso.

Mungaone kuti zakutengerani milungu 5 kuti muzolowere zomwe munkafuna mutamachita. Nthawiyi ingaoneke ngati ndi yaitali ndithu koma zikatheka mungasangalale podziwa kuti mwazolowera kuchita zinthu zatsopano zomwe munkafuna.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pakuti wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.”Miyambo 24:16.

Mfundo ya m’Baibuloyi ikusonyeza kuti si bwino kugwa ulesi mwamsanga. Zimenezitu n’zoona chifukwa chofunika si nthawi zimene timalephera koma nthawi zimene timachita bwino.

Chofunika si nthawi zimene tinalephera koma nthawi zimene tinachita bwino

ZIMENE MUNGACHITE

  • Musafulumire kudziona ngati wokanika chifukwa choti mwayambiranso kuchita zomwe mukufuna kusiya. Nthawi zina muzilakwitsa ndithu koma musafooke mpaka mutakwanitsa cholinga chanu.

  • Muziganizira kwambiri nthawi imene munakwanitsa kuchita zabwino. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kusintha mmene mumayankhulira ndi ana anu dzifunseni kuti: ‘Ndi liti pamene ndinkafuna kukalipira ana anga koma ndinadziletsa?’ N’chiyani chinandithandiza? Nanga ndingatani kuti ndichitenso zabwino zomwe ndinachitazo? Mafunsowa angakuthandizeni kuti mupitirize kuchita zabwino.

Kodi mukufuna kudziwa mmene mfundo za m’Baibulo zingakuthandizireninso pa mbali zina, monga zimene mungachite mukakhala ndi nkhawa, kuti banja lanu likhale losangalala, komanso kuti muzisangalaladi? Funsani a Mboni za Yehova kapena pitani pawebusaiti ya jw.org/ny.