Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Ndinayamba Kulemekeza Akazi Komanso Kudzilemekeza

Ndinayamba Kulemekeza Akazi Komanso Kudzilemekeza
  • CHAKA CHOBADWA:1960

  • DZIKO:FRANCE

  • POYAMBA:NDINKAGWIRITSA NTCHITO MANKHWALA OSOKONEZA BONGO, SINDINKALEMEKEZA AKAZI

KALE LANGA:

Ndinabadwira m’tauni ya Mulhouse, yomwe ili kumpoto chakummawa, m’dziko la France. M’tauniyi munali anthu ambiri osauka ndipo munkakonda kuchitika zandewu. Ndimakumbukira kuti pa nthawi imene ndinali mwana, mabanja ambiri ankangokhalira kukangana ndi kumenyana. Achibale anga sankalemekeza akazi ndipo nthawi zambiri amuna ankasankha okha zochita osafunsa akazi awo. M’dera lomwe ndinkakhala anthu ambiri ankaona kuti ntchito ya azimayi n’kuphika komanso kusamalira abambo ndi ana moti nanenso ndinatengera maganizo amenewa.

Ndili mwana ndinakumana ndi mavuto ambiri. Mwachitsanzo, ndili ndi zaka 10 bambo anga anamwalira chifukwa cha mowa. Kenako patapita zaka 5 mchimwene wanga wina anadzipha. Chaka chomwecho ndinaonanso m’bale wanga wina akuphedwa pamkangano womwe unali pakati pa banja lathu ndi banja lina. Zimenezi zinandichititsa mantha kwambiri. Abale anga anandiphunzitsa mmene ndingagwiritsire ntchito mipeni ndi mfuti. Komanso anandiphunzitsa ndewu kuti ndizikhala wokonzeka ngati wina atandiputa. Choncho ndinasokonezeka maganizo kwambiri moti ndinayamba kudzijambulajambula thupi lonse komanso kumwa mowa.

Nditakwanitsa zaka 16, ndinayamba kumwa kwambiri mowa moti patsiku ndinkamwa mabotolo 10 kapena 15. Kenako ndinayambanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Kuti ndizipeza ndalama zogulira mowa ndi mankhwalawa, ndinkagulitsa zitsulo zakutha komanso ndinkaba. Pamene ndinkakwanitsa zaka 17, n’kuti nditamangidwapo maulendo angapo. Ndinaweruzidwapo maulendo 18 pa milandu ya kuba ndi kuchita ndewu. Pa maulendowa, katatu ndinaweruzidwa kuti ndikakhale kundende ndipo maulendo 15 kuti ndisachoke m’dera lathu.

Ndili ndi zaka za m’ma 20 ndinayamba kuchita zinthu zoipa kwambiri. Mwachitsanzo, ndinkasuta ndudu za chamba 20 patsiku kuphatikizaponso mankhwala ena oopsa kwambiri osokoneza bongo. Maulendo angapo ndinapulumuka lokumbakumba chifukwa chomwa kwambiri mankhwalawa. Kenako ndinayamba kuzembetsa mankhwala osokoneza bongo ndipo ndinkayenda ndi mfuti komanso mipeni. Tsiku lina ndinkafuna kuombera munthu koma mwamwayi chipolopolo chinakafikira pachitsulo cha lamba ndipo chinangonjanja n’kukagwera kwina. Nditakwanitsa zaka 24, mayi anga anamwalira ndipo imfa yawo inangondiwonjezera mkwiyo. Ndinkaoneka woopsa kwambiri moti ndikakumana ndi anthu mumsewu ankathawira mbali ina. Chifukwa chokonda ndewu nthawi zambiri mlungu uliwonse ukamatha ndinkapezeka kupolisi kapena kuchipatala kukasoketsa mabala.

Ndinakwatira ndili ndi zaka 28 ndipo makhalidwe angawa anachititsa kuti ndisamalemekeze mkazi wanga. Ndinkamunyoza ndiponso kumumenya kwambiri. Sitinkachita zinthu mogwirizana ngati banja. Ndinkaona kuti chofunika kwambiri ndi kungomupatsa ndolo ndi zibangili zomwe ndaba. Koma kenako ndinadabwa kwambiri mkazi wanga atayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Ataphunzira ulendo woyamba, anasiya kusuta fodya, anakana kulandira ndalama zakuba ndipo anandibwezeranso ndolo zomwe ndinkamupatsa. Zimenezi zinandipsetsa mtima kwambiri. Ndipo ndinayamba kumuletsa kuphunzira Baibulo komanso ndikamasuta fodya ndinkamupeperera utsi kunkhope. Nthawi zambiri ndinkanyoza mkazi wanga anthu oyandikana nawo nyumba akumva.

Tsiku lina usiku ndinayatsa nyumba yathu chifukwa choledzera kwambiri. Koma mkazi wanga anandipulumutsa, n’kupulumutsanso mwana wathu wazaka 5. Mowa utandithera m’mutu, ndinadziimba mlandu kwambiri. Ndinkangoona kuti Mulungu sangandikhululukire, moti ndinakumbukira zomwe wansembe wina ananena kuti anthu oipa akamwalira amapita kumoto. Nayenso dokotala woona za maganizo amene ankandithandiza anandiuza kuti: “Inutu nde kaya! Zoti mudzasintha iwalani.”

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Nyumba yathu itapsa, tinasamuka n’kumakakhala kwa apongozi anga. Tsiku lina a Mboni za Yehova omwe ankaphunzira ndi mkazi wanga atabwera kudzamuona, ndinawafunsa kuti: “Kodi Mulungu angandikhululukire machimo anga onse?” Iwo anandisonyeza lemba la 1 Akorinto 6:9-11. Lembali limatchula makhalidwe amene Mulungu amadana nawo, koma limanenanso kuti: “Ena mwa inu munali otero.” Ndi mawu amenewa, ndinaona kuti n’zotheka kusintha. Kenako anandionetsa lemba la 1 Yohane 4:8 pofuna kunditsimikizira kuti Mulungu amandikonda. Zimenezi zinandilimbikitsa kwambiri moti ndinawapempha kuti aziphunzira nane Baibulo kawiri pa mlungu. Ndinayamba kupita ku misonkhano yawo yachikhristu ndiponso nthawi zonse ndinkapemphera kwa Yehova.

Mwezi usanathe, ndinasiya kumwa mowa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Komatu kusiya zimenezi kunalinso ndi mavuto ake. Mwachitsanzo, ndinkalota zinthu zoopsa, mutu unkandipweteka komanso minofu inkakungana. Ngakhale zinali choncho, ndinkaonabe kuti Yehova akundigwira dzanja n’kumandilimbikitsa. Ndinkamva ngati mmene Paulo ankamvera. Paulo anafotokoza mmene Mulungu ankamuthandizira. Iye anati: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Patapita nthawi ndinasiyanso kusuta fodya.—2 Akorinto 7:1.

Baibulo linandithandiza kwambiri kusintha khalidwe langa. Linathandizanso kuti ndisinthe mmene ndinkachitira zinthu ndi mkazi wanga. Ndinayamba kumulemekeza kwambiri ndipo ndikafuna kuti andipatse zinazake, ndinkamupempha mwaulemu ndi kumuthokoza. Ndinayambanso kukonda kwambiri mwana wathu. Kenako nditaphunzira Baibulo kwa chaka chimodzi, nanenso ndinadzipereka kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Ndimakhulupirira kuti mfundo za m’Baibulo n’zomwe zinapulumutsa moyo wanga. Ngakhale abale anga omwe si a Mboni amavomereza kuti ndikanakhala kuti sindinaphunzire Baibulo, bwenzi nditafa ndi mankhwala osokoneza bongo kapenanso ndikanaphedwa pandewu.

Mfundo za m’Baibulo zinandithandiza kwambiri kuti ndisinthe khalidwe langa. Ndinaphunzira zimene ndingachite kuti ndikhale mwamuna komanso bambo wabwino. (Aefeso 5:25; 6:4) Zimenezi zinachititsa kuti tiyambe kuchitira zinthu limodzi monga banja. Ndinasiya kuona kuti ntchito ya mkazi wanga ndi kuphika basi. Komanso ndimamuthandiza kuti akwaniritse bwino ntchito yake youza anthu uthenga wabwino nthawi zonse. Mkazi wanga nayenso amandithandiza kuti ndikwaniritse bwino udindo wanga monga mkulu mumpingo.

Yehova wandichitira zinthu zambiri zosonyeza kuti amandikonda komanso amandichitira chifundo. Choncho ndimafunitsitsa kuuza ena za makhalidwe abwino a Yehova, makamaka anthu amene amaonedwa kuti sangasinthe chifukwa nanenso anthu ena ankandiona choncho. Ndimadziwa kuti Baibulo likhoza kuthandiza munthu aliyense kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso moyo wosangalala. Baibulo landithandiza kuti ndizikonda anthu onse ndiponso kuwalemekeza, kaya akhale amuna kapena akazi. Landithandizanso kuti ndizidzilemekeza.