Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mavuto Amene Timakumana Nawo Ndi Chilango Chochokera kwa Mulungu?

Kodi Mavuto Amene Timakumana Nawo Ndi Chilango Chochokera kwa Mulungu?

LUZIA AMAYENDA MOTSIMPHINA. Ali mwana, anadwala matenda a poliyo omwe amagwira mitsempha yotumiza mauthenga kuubongo. Ndiyeno ali ndi zaka 16, ankagwira ntchito kwa mayi wina ndipo mayiyo anamuuza kuti: “Kulumalakutu ndi chilango chochokera kwa Mulungu chifukwa sunkamvera mayi ako komanso unkawachitira mwano.” Luzia amakumbukirabe mmene anakhumudwira mayiyu atamuuza zimenezi.

DAMARIS ATAUZIDWA KUTI ALI NDI KHANSA YA MUUBONGO, bambo ake anamufunsa kuti: “Kodi wachita chiyani kuti Mulungu akudwalitse matenda amenewa? Uyenera kuti wachita tchimo lalikulu kwambiri ndipo Mulungu akukulanga.” Damaris anakhumudwa kwambiri atamva mawu amenewa.

Anthu anayamba kale kwambiri kukhulupirira kuti akamadwala ndiye kuti Mulungu akuwalanga pa zinazake zimene analakwitsa. Buku lina limanena kuti anthu ambiri m’nthawi ya Yesu, ankakhulupirira kuti “munthu ankadwala chifukwa cha tchimo limene wachita kapena limene achibale ake achita.” (Manners and Customs of Bible Lands) Ndipo m’zaka za m’ma 500 mpaka m’ma 1500 C.E., “anthu ena ankakhulupirira kuti Mulungu ankabweretsa miliri pofuna kulanga anthu ochimwa.” (Medieval Medicine and the Plague) Mwachitsanzo, anthu ambiri anafa ndi mliri womwe unachitika ku Europe m’zaka za m’ma 1300 C.E. Ndiye kodi tinganene kuti anthu amenewa analangidwa ndi Mulungu chifukwa choti ankachita zoipa? Kapena mliriwo unachitika chifukwa cha mabakiteriya oyambitsa matenda monga mmene akatswiri ofufuza zamankhwala akhala akunenera? Ena angafunse kuti, kodi Mulungu amadwalitsadi anthu powalanga chifukwa cha machimo amene achita? *

TAGANIZIRANI MFUNDO IYI: Ngati matenda komanso mavuto alidi chilango chochokera kwa Mulungu, n’chifukwa chiyani Yesu yemwe ndi mwana wa Mulungu ankachiritsa anthu? Kodi zimene anachitazi sizikanasonyeza kuti akutsutsana ndi chilango chimene Mulungu wapereka kwa anthuwo? (Mateyu 4:23, 24) Yesu sakanachita zinthu zotsutsana ndi Mulungu. Tikutero chifukwa iye anati: “Ndimachita zinthu zomukondweretsa nthawi zonse,” komanso anati, “Ndikuchita izi kutsatira lamulo limene Atatewo anandipatsa.”​—Yohane 8:29; 14:31.

Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu “sachita chosalungama.” (Deuteronomo 32:4) Mwachitsanzo, Mulungu sangachititse ngozi yandege n’kuphetsa anthu ambirimbiri chifukwa choti akufuna kulanga munthu winawake yemwe wamuchimwira. Mfundo yoti Mulungu amachita zinthu mwachilungamo inatchulidwanso ndi Abulahamu, yemwe anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu. Iye anafunsa Mulungu kuti: “Kodi zoona mungawononge olungama pamodzi ndi oipa?” Kenako anayankha kuti: “Simungachite zimenezo.” (Genesis 18:23, 25) Baibulo limanenanso kuti, “Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe” ndipo “sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.”​—Yobu 34:10-12.

BAIBULO LIMASONYEZA KUTI MULUNGU SACHITITSA MAVUTO AMENE TIMAKUMANA NAWO

Mavuto amene timakumana nawo si chilango chochokera kwa Mulungu chifukwa cha machimo amene tachita. Yesu anasonyeza bwino mfundo imeneyi pamene iye limodzi ndi ophunzira ake anaona munthu yemwe anabadwa ali wosaona. “Ophunzira ake anamufunsa kuti: ‘Rabi, anachimwa ndani kuti munthu uyu abadwe wakhungu chonchi? Ndi iyeyu kapena makolo ake?’ Yesu anayankha kuti: ‘Munthuyu kapena makolo ake, onsewa palibe amene anachimwa. Izi zinachitika kuti ntchito za Mulungu zionekere kudzera mwa iye.’”​—Yohane 9:1-3.

Zikuoneka kuti ophunzira a Yesuwa ankakhulupirira zinthu zolakwika zomwe zinali zofala pa nthawiyo. Iwo ayenera kuti anadabwa kwambiri atamva Yesu akuwauza kuti munthuyo sanabadwe wolumala chifukwa cha kulakwa kwa iyeyo kapena makolo ake. Yesu anachiritsa munthu wosaonayo ndipo kuchita zimenezi kunatsutsa maganizo olakwika akuti mavuto ndi chilango chochokera kwa Mulungu. (Yohane 9:6, 7) Anthu amene akudwala matenda aakulu masiku ano, angalimbikitsidwe kudziwa kuti Mulungu si amene akuchititsa mavuto amene akukumana nawo.

Kodi Yesu akanachiritsa anthu odwala zikanakhala kuti Mulungu akuwalanga chifukwa cha machimo awo?

Malemba awa amatitsimikizira mfundo imeneyi

  • “Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (YAKOBO 1:13) Zoonadi, “zinthu zoipa” zomwe zakhala zikuchitika kwa zaka zonsezi, kuphatikizapo matenda, imfa komanso zopweteka, zichotsedwa posachedwapa.

  • Yesu Khristu anachiritsa “onse amene sanali kumva bwino m’thupi.” (MATEYU 8:16) Popeza Yesu ankachiritsa odwala, anasonyeza zomwe Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu ukamadzalamulira padzikoli.

  • “Iye [Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”​—CHIVUMBULUTSO 21:3-5.

KODI N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAVUTIKA?

Ngati Mulungu si amene amachititsa mavutowa, n’chifukwa chiyani anthufe timavutika chonchi? Anthu akhala akudzifunsa funso limeneli kwa nthawi yaitali. Kodi pali winawake amene amachititsa mavutowa? Mafunso amenewa ayankhidwa m’nkhani yotsatira.

^ ndime 4 Ngakhale kuti kale Mulungu ankalanga anthu ena powagwetsera tsoka chifukwa cha machimo amene achita, Baibulo silisonyeza kuti Yehova amagwiritsabe ntchito njira imeneyi masiku ano.