Mungasangalale ndi Madalitso Osatha Ochokera kwa Mulungu Wachikondi
Kodi mumalakalaka mutakhala m’dziko lopanda nkhondo, chiwawa ndi chidani?
Kodi mumafunitsitsa mutaona matenda, kuvutika ndi imfa zitatheratu?
Kodi mumalakalaka mutakhala moyo popanda kudandaula ndiponso kuda nkhawa?
Kodi mumafuna mutakhala pamalo amene sangawonongedwe ndi ngozi za m’chilengedwe?
Mulungu wathu wachikondi yemwenso ndi Mlengi wa dziko lathu lokongolali, walonjeza kuti adzadalitsa mtundu wa anthu powapatsa moyo wamtendere komanso wachimwemwe kwamuyaya. Amenewa si maloto.
Mukamawerenga nkhani zotsatirazi tikukupemphani kuti muganizire mafunso awa:
Kodi Mlengi wathu amatikonda?
Kodi Mulungu akutiuza uthenga wotani?
Kodi aneneri a Mulungu ananena zotani zokhudza madalitso amene Mulungu analonjeza?
Kodi tingatani kuti tizikhala osangalala panopa ndiponso kuti tidzasangalale ndi madalitso osatha m’tsogolo?
Tiyeni tiyambe ndi kuona zimene Mlengi wathu amatichitira posonyeza kuti amakonda anthu