Mlengi Wathu Wachikondi Amatisamalira
1. MLENGI WATHU AMAWALITSA DZUWA
Kodi moyo ukanakhala bwanji padzikoli zikanakhala kuti kulibe dzuwa? Mphamvu ya dzuwa imathandiza kuti mitengo itulutse masamba, maluwa, zipatso ndi njere. Imathandizanso kuti mizu ya mitengo izitha kutenga madzi kuchokera munthaka n’kuwapititsa m’masamba ndipo kenako madziwo akapita mumpweya amakhala nthunzi.
2. MLENGI WATHU AMAVUMBITSA MVULA
Mvula ndi mphatso yamtengo wapatali imene Mulungu amatipatsa ndipo imathandiza kuti dziko lapansi lizitulutsa chakudya chimene anthufe timadya. Mulungu amatipatsa mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zathu zimakhala zambiri, amadzadza mitima yathu ndi chakudya komanso chimwemwe.
3. MLENGI WATHU AMATIPATSA CHAKUDYA NDI ZOVALA
Abambo ambiri amadera nkhawa za mmene angapezere banja lawo chakudya chokwanira ndiponso zovala. Taonani zimene Malemba amanena: “Onetsetsani mbalame zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga chakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?”—Mateyu 6:25, 26.
“Phunzirani pa mmene maluwa akutchire amakulira. . . . Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale [Mfumu] Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa. Tsopano ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, . . . kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo?”—Mateyu 6:28-30.
Popeza kuti Mulungu amatha kutipatsa chakudya ndi zovala, n’zosakayikitsa kuti angatithandizenso kupeza zinthu zina zofunikira pa moyo. Tikamafunitsitsa kuchita zimene Mulungu amafuna, iye angadalitse khama lathu ndipo tingalime n’kupeza chakudya kapena angatithandize kupeza ntchito kuti tizigula zinthu zomwe tikufunikira.—Mateyu 6:32, 33.
Zoonadi, tili ndi zifukwa zabwino zotichititsa kukonda Mulungu tikaganizira zomwe analenga monga dzuwa, mvula, mbalame komanso maluwa. Nkhani yotsatirayi itithandiza kudziwa mmene Mlengi wathu wathandizira anthu kudziwa malonjezo ake.