Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi nkhani yakuti “Dzina Lanu Liyeretsedwe” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya June 2020, inamveketsa bwanji zimene timakhulupirira pa nkhani yokhudza dzina la Yehova ndi ulamuliro wake?
Munkhaniyo tinaphunzira kuti pali nkhani imodzi yokha yofunika kwambiri yomwe imakhudza anthu ndi angelo. Nkhani yake ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova. Nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova, kapena kuti kufuna kudziwa ngati Mulungu amalamulira bwino kapena ayi, ndi mbali ya nkhani yaikuluyi. Mofanana ndi zimenezi, nkhani yakuti anthu angakhale okhulupirika kwa Mulungu kapena ayi, ndi mbali inanso ya nkhani yaikuluyi.
N’chifukwa chiyani panopa timafotokoza kwambiri kuti nkhani yaikulu ndi yokhudza dzina la Yehova komanso kuyeretsedwa kwake? Tiyeni tikambirane zifukwa zitatu.
Choyamba, Satana anaipitsa dzina la Yehova, kapena kuti mbiri yake, m’munda wa Edeni. Funso limene Satana anafunsa Hava mochenjera linasonyeza ngati kuti Yehova anali Mulungu woumira, yemwe anapatsa Adamu ndi Hava malamulo opanda chilungamo. Kenako Satana mwachindunji anatsutsa zimene Yehova ananena ndipo pochita zimenezo anasonyeza kuti Mulungu ndi wabodza. Pamenepa iye ananyoza dzina la Yehova. Choncho anakhala “Mdyerekezi,” dzina limene limatanthauza “woneneza.” (Yoh. 8:44) Chifukwa chakuti Hava anakhulupirira bodza la Satanali, sanamvere Mulungu zomwe zinasonyeza kuti sanafune kuti Mulunguyo akhale wolamulira wake. (Gen. 3:1-6) Mpaka pano, Satana amanyozabe dzina la Mulungu n’kumafalitsa zabodza zokhudza iye. Kwa anthu amene amakhulupirira mabodzawa nthawi zambiri zimakhala zowavuta kumvera Yehova. Choncho kwa anthu a Mulungu, kunyoza dzina loyera la Yehova n’kupanda chilungamo koipitsitsa. Chimenechi ndi chifukwa chachikulu chomwe chikuchititsa mavuto ndi zoipa zonse padzikoli.
Chachiwiri, kuti athandize zolengedwa zake zonse, Yehova ndi wofunitsitsa kuti ayeretse dzina lake. Chimenechi ndi chinthu chofunika kwambiri kwa Yehova. Choncho iye amanena kuti: “Ndidzayeretsa dzina langa lalikulu.” (Ezek. 36:23) Ndipo Yesu anasonyeza bwino chinthu chofunika kwambiri chomwe atumiki okhulupirika onse a Yehova ayenera kutchula m’mapemphero awo pomwe anati: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mat. 6:9) Mobwerezabwereza, Baibulo limasonyeza kufunika kolemekeza dzina la Yehova. Taganizirani zitsanzo zochepa izi: “M’patseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.” (1 Mbiri 16:29; Sal. 96:8) “Imbani nyimbo zotamanda dzina lake.” (Sal. 66:2) “Ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale.” (Sal. 86:12) Nthawi ina imene Yehova analankhula kuchokera kumwamba, kunali kukachisi ku Yerusalemu, komwe Yesu anati: “Atate lemekezani dzina lanu.” Poyankha Yehova anati: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”—Yoh. 12:28. a
Chachitatu, nthawi zonse cholinga chachikulu cha Yehova chizidzakhala chogwirizana ndi dzina lake, kapena kuti mbiri yake. Taganizirani izi: N’chiyani chidzachitike pambuyo pa mayesero omaliza omwe adzachitike Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu
ukadzatha? Kodi anthu komanso angelo adzapitirizabe kugawikana pa nkhani yaikulu yokhudza kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova? Kuti tipeze yankho tiyeni tiganizirenso mbali ziwiri za nkhani yaikuluyi, zomwe ndi kukhulupirika kwa anthu komanso ulamuliro wa Yehova. Kodi anthu omwe anasonyeza kuti ndi okhulupirika adzapitiriza kuyesedwa kuti asonyezenso kuti ndi okhulupirika? Ayi. Iwo adzakhala angwiro komanso atayesedwa kale mokwanira ndipo adzalandira moyo wosatha. Kodi anthu komanso angelo adzapitiriza kukayikira kapenanso kugawikana pa nkhani yakuti Yehova ndi wolamulira wabwino? Ayi. Pofika pa nthawiyo, onse kumwamba ndi padziko lapansi adzagwirizana komanso kuvomereza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Koma nanga bwanji nkhani yokhudza dzina la Yehova?Pofika pa nthawiyo, dzina la Yehova lidzakhala litayeretsedweratu. Komabe lidzapitiriza kukhala lofunika kwambiri kwa atumiki ake onse okhulupirika kumwamba ndi padziko lapansi. Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo azidzaona Yehova akupitiriza kuchita zinthu zodabwitsa. Taganizirani izi: Chifukwa chakuti modzichepetsa Yesu adzabwezera ulamuliro kwa Yehova, Mulungu ‘adzakhala zinthu zonse kwa aliyense.’ (1 Akor. 15:28) Pambuyo pa zimenezi, anthu padziko lapansi adzasangalala ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Ndipo Yehova adzakwaniritsa cholinga chake chomwe wakhala nacho kwa nthawi yaitali chakuti onse kumwamba ndi padziko lapansi akhale banja lalikulu logwirizana.—Aef. 1:10.
Kodi zonsezi zidzakhudza bwanji banja la Yehova kumwamba ndi padzikoli? Mosakayikira, tidzakhala ofunitsitsa kupitiriza kutamanda dzina lokongola la Yehova. Wolemba masalimo Davide anauziridwa kulemba kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu . . . Lidalitsike dzina lake laulemerero mpaka kalekale.” (Sal. 72:18, 19) Tidzapitiriza kupeza zifukwa zatsopano zotichititsa kulemekeza Yehova mpaka kalekale.
Dzina la Yehova limaimira chilichonse chokhudza iye. Choncho limatikumbutsa makamaka zokhudza chikondi chake. (1 Yoh. 4:8) Nthawi zonse tizidzakumbukira kuti chikondi chinamuchititsa kuti atilenge, apereke nsembe ya dipo komanso kuti asonyeze kuti ulamuliro wake ndi wolungama ndiponso wachikondi. Komabe tidzapitiriza kuona Yehova akusonyeza chikondi kwa zolengedwa zake. Tizidzafunitsitsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Atate wathu komanso kuimba nyimbo zotamanda dzina lake mpaka kalekale.—Sal. 73:28.
a Baibulo limasonyezanso kuti Yehova amachita zinthu “chifukwa cha dzina lake.” Mwachitsanzo, iye amatsogolera anthu ake, kuwathandiza, kuwapulumutsa, kuwakhululukira komanso kuwasunga amoyo. Iye amachita zonsezi chifukwa cha dzina lake lalikulu, lakuti Yehova.—Sal. 23:3; 31:3; 79:9; 106:8; 143:11.