Kodi Mumaonetsa Mzimu Wotani?
“Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale nanu chifukwa cha mzimu umene mumaonetsa.”—FILIM. 25.
1. Kodi Paulo ankakonda kuuza Akhristu anzake kuti chiyani?
M’MAKALATA opita kwa Akhristu anzake, Paulo ankakonda kuwauza kuti Mulungu ndiponso Khristu akhale nawo chifukwa cha mzimu umene Akhristuwo ankaonetsa. Mwachitsanzo, iye anauza Akhristu a ku Galatiya kuti: “Abale, kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, kukhale nanu chifukwa cha mzimu umene mumausonyeza. Ame.” (Agal. 6:18) Kodi iye ankatanthauza chiyani ponena kuti “mzimu umene mumausonyeza”?
2, 3. (a) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani nthawi zina ponena mawu akuti “mzimu”? (b) Kodi tingachite bwino kudzifunsa mafunso ati okhudza mzimu umene timasonyeza?
2 Paulo anagwiritsa ntchito mawu oti “mzimu” potanthauza maganizo kapena mtima wa munthu. Iye ankanena za zimene zimachititsa munthu kulankhula kapena kuchita zinthu m’njira inayake. Munthu wina akhoza kukhala ndi mtima wodekha, woganizira ena, wofatsa, wopatsa kapena wokhululuka. Baibulo limatilimbikitsa kukhala ndi “mzimu wabata ndi wofatsa.” (1 Pet. 3:4; Miy. 17:27) Koma munthu wina akhoza kukhala ndi mtima wapachala, wonyoza, wokonda chuma kapena wosamva za ena. Ndiye pali ena amene amakhala ndi mtima woipa, wosamvera ngakhalenso wopanduka.
3 Choncho pamene Paulo ankanena mawu ngati akuti ‘Ambuye akhale nanu chifukwa cha mzimu umene mumaonetsa,’ ankalimbikitsa abale ake kusonyeza mzimu wogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndiponso makhalidwe a Khristu. (2 Tim. 4:22; werengani Akolose 3:9-12.) Nafenso tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimaonetsa mzimu wotani? Kodi ndingatani kuti ndikhale ndi mzimu umene umasangalatsa Mulungu? Kodi ndingathandize bwanji kuti mu mpingo mukhale mzimu wabwino?’ Mwachitsanzo, m’munda wa mpendadzuwa, duwa lililonse limachititsa kuti munda wonsewo uzioneka wokongola. Kodi ifeyo tili ngati maluwa amene amakongoletsa mpingo? Tiyeni tiziyesetsa kutero. Tsopano tiona zimene tingachite kuti tikhale ndi mzimu wosangalatsa Mulungu.
PEWANI MZIMU WA DZIKO
4. Kodi “mzimu wa dziko” n’chiyani?
4 Malemba amati: “Sitinalandire mzimu wa dziko, koma mzimu wochokera kwa Mulungu.” (1 Akor. 2:12) Kodi “mzimu wa dziko” n’chiyani? Lemba la Aefeso 2:2 lingatithandize kuudziwa. Lembali limati: “Munali kuyenda m’zimenezo mogwirizana ndi nthawi za m’dzikoli, momveranso wolamulira wa mpweya umene umalamulira zochita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe kameneka, tsopano kakugwira ntchito mwa ana a kusamvera.” ‘Mpweyawu’ ndi mzimu wa dziko, kapena kuti maganizo ake, ndipo uli paliponse ngati mpweya weniweni. Anthu amasonyeza mzimuwu pokhala ndi mtima wosafuna kuuzidwa zochita kapena wofuna kumenyera ufulu wawo nthawi zonse. M’dziko la Satanali, anthu oterewa ndi “ana a kusamvera.”
5. Kodi Aisiraeli ena anasonyeza mzimu wotani?
5 Anthu anayamba kalekale kukhala ndi maganizo amenewa. M’nthawi ya Mose, Kora anaukira anthu amene ankayang’anira Aisiraeli. Iye ankatsutsa kwambiri Aroni ndi ana ake, omwe anali ansembe. Mwina Kora ankadziwa zinthu zimene iwo ankalakwitsa. Mwinanso ankaona kuti Mose amangopereka maudindo kwa azibale ake. Kaya Kora ankachita izi pa zifukwa zotani, mfundo ndi yakuti, sankaona zinthu mmene Mulungu ankazionera. Iye anachitira mwano anthu amene Yehova anasankha. Ananena kuti: “Tatopa nanu tsopano! . . . N’chifukwa chiyani inu mukudzikweza pa mpingo?” (Num. 16:3) Datani ndi Abiramu anatsutsanso Mose. Iwo ananena kuti iye ‘akukhala ngati mfumu yomawalamula.’ Mose atawaitana, iwo anayankha mokula mtima kuti: “Ife sitibwerako kumeneko!” (Num. 16:12-14) Yehova sanasangalale ndi mzimu umene anasonyeza. Iye anapha opanduka onsewo.—Num. 16:28-35.
6. Kodi anthu ena m’nthawi ya atumwi anasonyeza bwanji kuti anali ndi mzimu woipa? Kodi mwina ankachita zimenezi chifukwa chiyani?
6 M’nthawi ya atumwi, panalinso anthu ena amene ankatsutsa oyang’anira mu mpingo ndiponso “kunyalanyaza ulamuliro.” (Yuda 8) Zikuoneka kuti anthuwa sankakhutira ndi maudindo awo ndipo ankayesa kukopa ena kuti aukire oyang’anira mu mpingo. Koma oyang’anirawa anali osankhidwa ndi Mulungu ndipo ankayesetsa kukwaniritsa udindo wawo.—Werengani 3 Yohane 9, 10.
7. Kodi tiyenera kupewa mzimu uti mu mpingo?
7 Mzimu umenewu ndi wosafunika mu mpingo wachikhristu. Choncho tiyenera kusamala kuti tisayambe kukhala nawo. M’nthawi ya Mose komanso ya mtumwi Yohane, oyang’anira anali opanda ungwiro. Ndi mmene zililinso mu mpingo masiku ano. Akulu angalakwitse zinthu zina zimene zingatikhumudwitse. Ngati zimenezi zitachitika, kungakhale kulakwa kusonyeza mzimu wa dziko wonena kuti, “Chilungamo chichitike basi!” kapena wonena kuti, “Asangomusiya m’bale ameneyu!” Yehova akhoza kungoyang’ana zinthu zina n’kuzisiya. Nafenso tingachite bwino kutengera chitsanzo chake. Anthu ena amene achita tchimo lalikulu amakana kukumana ndi akulu amene apemphedwa kuwathandiza. Iwo amachita zimenezi chifukwa chodziwa zinthu zina zimene akuluwo analakwitsa. Anthu oterowo ali ngati wodwala amene akukana mankhwala othandiza chifukwa chakuti sakusangalala ndi dokotala.
8. Kodi ndi malemba ati amene angatithandize kulemekeza oyang’anira mu mpingo?
Chiv. 1:16, 20) Popeza Yesu ndi Mutu wa mpingo, amadziwa chilichonse chokhudza akulu mu mpingo. Ngati pali mkulu wina amene ayenera kudzudzulidwa, Yesu amene ali ndi maso “ngati lawi la moto” adzaonetsetsa kuti zimenezi zichitike m’nthawi ndiponso njira yoyenera. (Chiv. 1:14) Pamene tikudikira Yesu, chofunika kuchita ndi kulemekeza anthu amene aikidwa ndi mzimu woyera. Paja Paulo analemba kuti: “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvera ndi kuwagonjera kuti agwire ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuvulazani.”—Aheb. 13:17.
8 Tikhoza kupewa mzimu umenewu tikamakumbukira kuti Baibulo limasonyeza kuti Yesu ali ndi “nyenyezi 7” m’dzanja lake lamanja. “Nyenyezi” zimenezi kwenikweni zimaimira oyang’anira odzozedwa koma zingaimirenso oyang’anira onse m’mipingo. Yesu angatsogolere “nyenyezi” za m’dzanja lake m’njira iliyonse imene akufuna. (9. (a) Kodi Mkhristu ayenera kusamala ndi chiyani akapatsidwa uphungu? (b) Kodi ndi bwino kuchita chiyani tikapatsidwa uphungu?
9 Munthu akapatsidwa uphungu ndi akulu kapena kuchotseredwa maudindo ena, ayenera kusamala kwambiri kuti asasonyeze mzimu Sal. 11:5; 1 Tim. 3:8-10) Izi zitachitika, m’baleyu ankauza ena kuti sakugwirizana ndi chiweruzochi. Iye ankalemba makalata ambiri ku ofesi ya nthambi oneneza akuluwo. Ankalimbikitsanso ena kuchita zimenezi. Koma si nzeru kusokoneza mtendere mu mpingo poyesa kusonyeza ena kuti sitinalakwe. Ndi bwino kuona uphungu ngati mwayi wotithandiza kuzindikira mavuto athu ndiyeno n’kutsatira uphunguwo popanda kulankhulalankhula.—Werengani Maliro 3:28, 29.
woipa. M’bale wina wachinyamata analangizidwa ndi akulu kuti asiye kuchita masewera achiwawa pakompyuta. N’zomvetsa chisoni kuti iye sanamvere ndipo anayenera kuchotsedwa monga mtumiki wothandiza. Zinatero chifukwa chakuti mogwirizana ndi Malemba, sanalinso woyenerera. (10. (a) Kodi tingaphunzire chiyani pa lemba la Yakobo 3:16-18? (b) Kodi kuchita zinthu mogwirizana ndi “nzeru yochokera kumwamba” kungatithandize bwanji?
10 Lemba la Yakobo 3:16-18 limasonyeza zoyenera ndiponso zosayenera mu mpingo. Lembali limati: “Pamene pali nsanje ndi mtima wokonda mikangano, palinso chisokonezo ndi zoipa zamtundu uliwonse. Koma nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere, yololera, yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, ndiponso yopanda chinyengo. Komanso, chilungamo ndicho chipatso cha mbewu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.” Tikamachita zinthu mogwirizana ndi “nzeru yochokera kumwamba,” timatsanzira makhalidwe a Mulungu. Zimenezi zingatithandize kulimbikitsa mzimu wabwino mu mpingo.
SONYEZANI MZIMU WAULEMU MU MPINGO
11. (a) Kodi kukhala ndi mzimu wabwino kungatithandize kupewa chiyani? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Davide?
11 Tizikumbukira kuti Yehova wapatsa akulu udindo ‘woweta mpingo wa Mulungu.’ (Mac. 20:28; 1 Pet. 5:2) Kaya ndife akulu kapena ayi, tiyenera kulemekeza dongosolo limene Mulungu wakhazikitsa. Kukhala ndi mzimu wabwino kungatithandize kuti tisamaganizire kwambiri za udindo. Sauli ankaona kuti Davide alanda ufumu wake, choncho “anayamba kuyang’ana Davide ndi diso loipa.” (1 Sam. 18:9) Sauli anayamba kukhala ndi mzimu woipa mpaka kufika pofuna kupha Davide. Tiyeni tipewe mtima wofunitsitsa udindo ngati Sauli koma titengere chitsanzo cha Davide. Ngakhale kuti Davide anachitiridwa zinthu zambiri zopanda chilungamo, iye ankalemekezabe mfumu yoikidwa ndi Mulungu.—Werengani 1 Samueli 26:23.
12. N’chiyani chingalimbikitse mgwirizano mu mpingo?
12 Kusiyana maganizo kungachititse anthu kuyambana mu mpingo. Izi zikhoza kuchitika ngakhale pakati pa oyang’anira. Koma malangizo a m’Baibulo angatithandize. Malemba amati: “Posonyezana ulemu, khalani patsogolo” komanso kuti, “Musadziyese anzeru.” (Aroma 12:10, 16) M’malo mongoti kakaka pa maganizo athu, tizikumbukira kuti pamakhala njira zingapo zophera khoswe. Tikamayesa kuona zinthu mmene anzathu akuzionera, tikhoza kulimbikitsa mgwirizano mu mpingo.—Afil. 4:5.
13. Kodi tiyenera kukhala ndi mtima wotani tikapereka maganizo athu pa nkhani inayake? Kodi ndi chitsanzo chiti cha m’Baibulo chimene chingatithandize?
13 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti si bwino kufotokoza maganizo athu ngati taona kuti pali zinthu zina zofunika kusintha mu mpingo? Ayi. M’nthawi ya atumwi, anthu anatsutsana za nkhani inayake. Ndiyeno abale “anasankha Paulo ndi Baranaba, pamodzi ndi ena mwa iwo, kuti apite kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu, kuti akawauze za kutsutsanako.” (Mac. 15:2) N’zosachita kufunsa kuti aliyense anali ndi maganizo ake a mmene angathetsere nkhaniyi. Pokambirana, aliyense anafotokoza maganizo ake ndipo mzimu unawathandiza kusankha chimodzi. Izi zitachitika, abalewo sanapitirize kuumirira maganizo awo. Kalata yofotokoza zimene anasankha itafika ku mipingo, anthu “anakondwera chifukwa cha mawu olimbikitsawo” ndipo mipingo “inapitiriza kulimba m’chikhulupiriro.” (Mac. 15:31; 16:4, 5) Nafenso tiyenera kutengera chitsanzo chimenechi. Ngati tauza akulu nkhani inayake, tiyenera kuisiya m’manja mwawo ndipo tisamakayikire kuti adzaiganizira ndi kuisamalira moyenera.
SONYEZANI MZIMU WOKHULULUKIRA ANZANU
14. Kodi tingasonyeze bwanji mzimu wabwino pochita zinthu ndi anzathu?
14 Pochita zinthu ndi anzathu, timakhala ndi mwayi wosonyeza mzimu wabwino. Mwachitsanzo, anthu ena akatilakwira, tingachite bwino kusonyeza mzimu wokhululuka. Baibulo limatiuza kuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.” (Akol. 3:13) Mawu akuti “ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira” amasonyeza kuti pangakhale zifukwa zomveka zoti tikhumudwe ndi zochita za ena. Koma tikamakhumudwa msanga, tikhoza kusokoneza mtendere mu mpingo. M’malomwake, tiziyesetsa kutengera chitsanzo cha Yehova chokhululuka ndi mtima wonse n’kumapitiriza kutumikira Mulungu.
15. (a) Kodi tingaphunzire chiyani kwa Yobu pa nkhani ya kukhululuka? (b) Kodi kupemphera kungatithandize bwanji kusonyeza mzimu wabwino?
15 Yobu ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya kukhululuka. Anthu atatu amene anabwera kudzamutonthoza anamukhumudwitsa pomulankhula mawu opweteka. Koma Yobu anawakhululukira. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? ‘Iye anawapempherera.’ (Yobu 16:2; 42:10) Kupempherera anthu ena kungatithandize kuti tiziwaona moyenera. Kupempherera Akhristu anzathu kumatithandiza kukhala ndi maganizo a Khristu. (Yoh. 13:34, 35) Tiyenera kupempheranso kuti Mulungu atipatse mzimu woyera. (Luka 11:13) Mzimu wa Mulungu ungatithandize kukhala ndi makhalidwe abwino pochita zinthu ndi anzathu.—Werengani Agalatiya 5:22, 23.
THANDIZANI KUTI M’GULU LA MULUNGU MUKHALE MZIMU WABWINO
16, 17. Kodi inuyo mukufunitsitsa kusonyeza mzimu wotani?
16 Zinthu zimayenda bwino kwambiri ngati aliyense mu mpingo amayesetsa kuthandiza kuti mukhale mzimu wabwino. Pamene takambirana nkhaniyi, mwina tikuona kuti pali zinazake zimene tiyenera kusintha n’cholinga choti tizisonyeza mzimu wabwino. Ngati ndi choncho, tiyeni tilole Mawu a Mulungu kuti atithandize kusintha. (Aheb. 4:12) Paulo ankafuna kwambiri kukhala chitsanzo chabwino mu mpingo. Iye anati: “Sindikudziwa kanthu kalikonse konditsutsa mumtima mwanga. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti basi ndine wolungama, koma Yehova ndiye amandifufuza.”—1 Akor. 4:4.
17 Tonsefe tikhoza kuthandiza mpingo kukhala ndi mzimu wabwino. Tingatero pochita zinthu mogwirizana ndi nzeru yochokera kumwamba. Tizipewanso kuganizira kwambiri za udindo ndiponso kuumirira maganizo athu. Kuti tizigwirizana ndi Akhristu anzathu, tiyenera kukhala ndi mzimu wokhululukira ena ndiponso kuwaona moyenera. (Afil. 4:8) Tikamachita zonsezi, Yehova ndi Yesu adzasangalala kwambiri ndi ‘mzimu umene timaonetsa.’—Filim. 25.