Kodi Mwasandulika?
“Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.”—AROMA 12:2.
1, 2. Kodi timakhudzidwa bwanji ndi kumene tinakulira komanso kumene tikukhala?
TONSEFE timachita zinthu malinga ndi kumene tinakulira komanso kumene tikukhala. Ndipo timasiyana pa nkhani ya zovala, chakudya komanso makhalidwe. Izi zingachitike chifukwa timatengera anthu amene timakhala nawo ndiponso chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wathu.
2 Koma timasiyananso pa zinthu zofunika kwambiri kuposa zovala ndi zakudya. Mwachitsanzo, malinga ndi mmene tinakulira, pali zinthu zina zimene timaona kuti ndi zoyenera pomwe zina timaona kuti ndi zolakwika. Timachitanso zinthu zina potsatira chikumbumtima chathu. Baibulo limanena kuti nthawi zambiri ‘anthu a mitundu amene alibe chilamulo amachita mwachibadwa zinthu za m’chilamulo.’ (Aroma 2:14) Kodi izi zikutanthauza kuti ngati Mulungu sanapereke lamulo loletsa zinthu zina ndiye kuti tikhoza kutsatira zimene ifeyo kapena anthu ena a m’dera lathu amaona kuti n’zoyenera?
3. Kodi Akhristu sayenera kungotsatira maganizo awo kapena a anthu ena pa zifukwa ziwiri ziti?
3 Akhristu oona sayenera kungotsatira maganizo awo kapena a anthu ena. Tikutero pa zifukwa ziwiri. Choyamba, Baibulo limatiuza kuti: “Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu, koma mapeto ake ndi imfa.” (Miy. 16:25) Popeza si ife angwiro, patokha sitingasankhe bwinobwino zinthu zimene zingatithandize pa moyo wathu. (Miy. 28:26; Yer. 10:23) Chachiwiri, Baibulo limasonyeza kuti dziko lonse lili m’manja mwa Satana. Choncho maganizo ndiponso mfundo zimene anthu ambiri amayendera m’dzikoli zimachokera kwa Satanayo, yemwe ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akor. 4:4; 1 Yoh. 5:19) Ndiyetu ngati tikufuna kuti Yehova atidalitse tiyenera kutsatira malangizo a pa Aroma 12:2.—Werengani.
4. Kodi m’nkhani ino tipeza mayankho a mafunso ati?
4 Pa lemba la Aroma 12:2 pali mfundo zofunika kwambiri zimene tiyenera kuziganizira. Mwachitsanzo, tikhoza kudzifunsa kuti, (1) N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kusandulika’? (2) Kodi kusandulika n’kutani? ndiponso (3) Kodi tingatani kuti tisandulike? Tiyeni tipeze mayankho a mafunso amenewa.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUSANDULIKA?
5. Kodi mawu a pa Aroma 12:2 anali othandiza kwambiri kwa ndani?
5 Uthenga wa m’kalata imene Paulo analembera Aroma, unali wopita kwa Akhristu anzake odzozedwa osati anthu osakhulupirira. (Aroma 1:7) Iye anawauza kuti asandulike n’kusiya ‘kutengera nzeru za pa nthawiyo.’ Paulo analemba kalatayi cha m’ma 56 C.E., ndipo pa nthawiyo anthu ankatengera makhalidwe, maganizo ndiponso nzeru za Aroma. Komanso zikuoneka kuti Akhristu ena anali kutengerabe zinthu zimenezi. Kodi zinthuzi zinakhudza bwanji abale ndi alongo pa nthawiyo?
6, 7. Kodi ndi zinthu ziti zimene zikanabweretsa mavuto kwa Akhristu a ku Roma?
6 Masiku ano, munthu akapita ku Rome amatha kuona mabwinja a akachisi, manda, zipilala, mabwalo a masewera ndi zinthu zina. Zina mwa zinthuzi zinamangidwa nthawi ya atumwi ndipo zimatithandiza kudziwa mmene zinthu zinalili kalelo pa nkhani ya chipembedzo komanso moyo wa tsiku ndi tsiku. Tikawerenganso mabuku a mbiri yakale timamva zimene zinkachitika kumeneko. Mwachitsanzo, timamva kuti kunkakhala masewera achiwawa, mipikisano ya magaleta ndiponso zisudzo zosiyanasiyana. Zina mwa zisudzozi zinali zochititsa manyazi. Kunkachitikanso malonda osiyanasiyana moti anthu anali ndi mwayi wopeza ndalama zambiri.—Aroma 6:21; 1 Pet. 4:3, 4.
7 Ngakhale kuti Aroma anali ndi akachisi komanso milungu yambirimbiri, iwo sankakonda kwenikweni milunguyo. Kwa iwo chofunika kwambiri pa nkhani ya chipembedzo chinali miyambo yokhudza kubadwa kwa mwana, ukwati ndiponso maliro. Ndiye mutha kuona kuti zimenezi zikanabweretsa mavuto kwa Akhristu a ku Roma. Ambiri asanakhale Akhristu ankachita zimenezi ndipo anafunika kusandulika kuti akhale Akhristu oona. Koma kuti asandulike, ankayenera kupitiriza kusintha zinthu ngakhale atabatizidwa.
8. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingabweretse mavuto kwa Akhristu masiku ano?
8 Masiku anonso, pali zinthu zambiri m’dzikoli zimene zingabweretse mavuto kwa Akhristu. Tikutero chifukwa chakuti mzimu wa dzikoli umasokoneza anthu m’njira zosiyanasiyana. (Werengani Aefeso 2:2, 3; 1 Yohane 2:16.) N’zosavuta kutengera makhalidwe, maganizo ndiponso mtima wa anthu amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku. Choncho m’pofunikadi kutsatira malangizo a m’Malemba akuti ‘tisandulike’ ndipo tisiye ‘kutengera nzeru za nthawi ino.’ Kodi tingachite bwanji zimenezi?
ZINTHU ZIMENE TIYENERA KUSINTHA KUTI TISANDULIKE
9. Kodi anthu ambiri anasintha zinthu ziti asanabatizidwe?
9 Munthu akamaphunzira mfundo za m’Baibulo n’kumazigwiritsa ntchito amayamba kukonda kwambiri Mulungu. Ndiyeno amasintha zinthu zambiri pa moyo wake mogwirizana ndi zimene waphunzirazo. Amasiya kuchita zinthu zokhudza chipembedzo chonyenga komanso amasiya makhalidwe ake oipa n’kuyamba kutsanzira Khristu. (Aef. 4:22-24) Timasangalala kuona anthu ambirimbiri akuchita zimenezi chaka chilichonse n’kukhala oyenerera kubatizidwa posonyeza kuti anadzipereka kwa Yehova Mulungu. Tikudziwa kuti zimenezi zimasangalatsanso mtima wa Yehova. (Miy. 27:11) Komabe, tiyeni tione ngati pali zinanso zimene munthu ayenera kusintha.
10. Kodi kusandulika kumasiyana bwanji ndi kungosintha zina ndi zina?
10 Kusandulika kumafuna zambiri osati kungosintha zinthu zina ndi zina. Mwachitsanzo, kampani yopanga sopo ikhoza kusintha zinthu zina ndi zina kuti sopoyo akhale wabwino kwambiri. Mwina akhoza kungowonjezera kenakake kapena kusintha paketi yake, koma sopoyo amakhalabe yemweyo. Ponena za mawu akuti ‘kusandulika’ buku lina lomasulira mawu a m’Baibulo limati: “Lemba la Aroma 12:2 likusiyanitsa kutengera zinthu za m’nthawi ino ndi kusinthiratu maganizo ndiponso mtima chifukwa chothandizidwa ndi mphamvu ya Mzimu Woyera.” Choncho kuti munthu asandulike, pamafunika zambiri osati kungosiya makhalidwe kapena malankhulidwe oipa. Anthu ena amene sadziwa mfundo za m’Baibulo, amayesetsa kupewa zinthu zoipazi. Ndiyeno kodi chimafunika n’chiyani kuti Mkhristu asandulike?
11. Kodi Paulo ananena kuti munthu ayenera kuchita chiyani kuti asandulike?
11 Paulo analemba kuti: “Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.” Choncho kuti munthu asandulike ayenera kusintha mmene amaganizira. Kumayambiriro kwa kalata imene analembera Aroma, Paulo ananena za anthu amene anali ndi ‘maganizo oipa.’ Anthu amenewa ankachita “zosalungama zonse, kuipa konse, kusirira konse kwa nsanje, ndi uchimo wonse. Mtima wawo unadzala kaduka, umbanda, ndewu, chinyengo” ndi zinthu zina zoipa. (Aroma 1:28-31) N’chifukwa chake Paulo analimbikitsa anthu amene anakulira m’dera limeneli n’kuyamba kutumikira Mulungu kuti ‘asandulike ndi kusintha maganizo awo.’
“Kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu.”—Aef. 4:31
12. (a) Kodi anthu ambiri amaganiza bwanji masiku ano? (b) Kodi maganizo amenewa angabweretse mavuto otani kwa Akhristu?
12 Anthu ambiri m’dzikoli alinso ndi ‘maganizo oipa.’ Mwina iwo amaganiza kuti n’zachikale zoti anthu ena aziuza anzawo mfundo zoti aziyendera. Aphunzitsi ndi makolo ambiri amaganiza kuti ana ayenera kukhala ndi ufulu wochita zimene akufuna. Iwo amaona kuti palibe mfundo zimene anthu onse ayenera kuyendera. Ngakhale anthu ambiri amene ali m’zipembedzo amaona kuti ali ndi ufulu wochita chilichonse chimene akuona kuti n’chabwino osaganizira zimene Mulungu amafuna. (Sal. 14:1) Maganizo amenewa akhoza kusokoneza mmene Akhristu ena amaonera zinthu m’gulu la Yehova. Mwachitsanzo, mwina sangafune kuyendera dongosolo la mpingo ndipo angayambe kudandaula ndi chilichonse chimene sakusangalala nacho. Kapena sangagwirizane ndi malangizo ochokera m’Baibulo pa nkhani ya zosangalatsa, kugwiritsa ntchito Intaneti kapena maphunziro a ku yunivesite.
13. N’chifukwa chiyani tiyenera kudzifufuza moona mtima?
13 Choncho kuti tisatengere maganizo a m’dzikoli, tiyenera kufufuza moona mtima maganizo athu, zolinga zathu ndiponso zimene timaona kuti n’zofunika. Anthu ena angaone ngati tikuchita bwino ndipo mwina angatiuze zimenezi. Koma munthu aliyense amadziwa yekha ngati akulola kuti zimene waphunzira m’Baibulo zizisintha mtima wake.—Werengani Yakobo 1:23-25.
KODI MUNTHU ANGASANDULIKE BWANJI?
14. N’chiyani chingatithandize kusintha?
14 Kuti tisandulike tiyenera kusintha zimene zili mumtima. Kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi? Tiyenera kuphunzira Baibulo kuti tidziwe zimene Yehova amafuna kuti tizichita. Ndiyeno zimene timachita tikamaphunzira Baibulo, zimasonyeza zimene zili mumtima mwathu. Zimasonyezanso zimene tiyenera kusintha kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi ‘chifuniro cha Mulungu changwiro.’—Aroma 12:2; Aheb. 4:12.
15. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamaumbidwa ndi Yehova?
15 Werengani Yesaya 64:8. Zimene Yesaya ananena zingatithandize kuzindikira mfundo zina zofunika pa nkhaniyi. Kodi Yehova amatiumba bwanji? Sikuti amatisintha kuti tizioneka okongola kwambiri. M’malomwake, amatiphunzitsa kuti tikhale ndi mtima wabwino. Ngati titalola kuti Yehova atiumbe, tidzakhala ndi mtima umene ungatithandize kupewa maganizo oipa a m’dzikoli. Kuti timvetse nkhaniyi tiyeni tikambirane zimene woumba mbiya weniweni amachita.
16, 17. (a) Fotokozani zimene munthu amachita akafuna kuumba mbiya. (b) Kodi Mawu a Mulungu amatithandiza bwanji?
16 Munthu akafuna kuumba mbiya yabwino, amasankha dongo labwino kwambiri. Kenako amachita zinthu ziwiri. Choyamba, amalithira madzi kuti achotse zinyalala ndi zinthu zina zosafunika. Chachiwiri, dongolo likauma amalithiranso madzi pang’ono kuti lifewe n’kuyamba kuumba chinthu chimene akufuna.
17 Apa tikuona kuti woumba amagwiritsa ntchito madzi pochotsa zinthu zosafunika komanso kuti afewetse dongolo n’cholinga choti aumbe chinthu chimene akufuna. Kodi Mawu a Mulungu amafanana bwanji ndi madzi pa moyo wathu? Choyamba, amatithandiza kuchotsa maganizo oipa amene tinali nawo tisanadziwe Mulungu. Chachiwiri, amatithandiza kusintha kuti tikhale munthu wamtengo wapatali kwa Mulungu. (Aef. 5:26) N’chifukwa chake timalimbikitsidwa mobwerezabwereza kuti tiziwerenga Baibulo tsiku lililonse ndiponso kusonkhana nthawi zonse kuti tiziphunzira Mawu a Mulungu. Tikamachita zimenezi timakhala tikulola kuti Yehova azitiumba.—Sal. 1:2; Mac. 17:11; Aheb. 10:24, 25.
18. (a) Kodi kuganizira zimene taphunzira kungathandize bwanji kuti Mawu a Mulungu atisinthe? (b) Kodi tingachite bwino kudzifunsa mafunso ati?
18 Kuwonjezera pa kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo nthawi zonse, tiyenera kuchita zinthu zinanso kuti Mawu a Mulungu atisinthe. Anthu ambiri amawerenga Baibulo nthawi ndi nthawi mpaka kufika polizolowera kwambiri. Mwina munakumanapo ndi anthu ngati amenewa mu utumiki. Ena anafika poloweza nkhani zina za m’Baibulo. * Komabe siziwathandiza kusintha moyo wawo. Kodi vuto limakhala chiyani? Kuti Mawu a Mulungu asinthe munthu, mawuwo ayenera kumufika pamtima. Choncho tiyenera kupeza nthawi yoganizira zimene tikuphunzira. Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakhulupiriradi kuti zimene ndikuphunzira ndi zoona? Kodi ndimaona mmene ndingagwiritsire ntchito zimene ndaphunzira kapena ndimangoona kuti ndi zokaphunzitsa ena? Kodi ndikamaphunzira ndimaona kuti Yehova akulankhula ndi ineyo?’ Kuganizira mafunso ngati amenewa kungatithandize kuti tizikonda kwambiri Yehova. Ndiyeno Mawu ake akatifika pamtima tidzasintha moyo wathu.—Miy. 4:23; Luka 6:45.
19, 20. Kodi tiyenera kutsatira malangizo ati a m’Baibulo kuti tidalitsidwe?
19 Kuwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse ndiponso kuganizira zimene tawerengazo kungatithandize kuti tidziwe zinthu molondola. Tikatero, tidzapitiriza ‘kuvula umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, n’kuvala umunthu watsopano umene Mulungu amapereka.’ (Akol. 3:9, 10) Tikamamvetsa bwino Mawu a Mulungu komanso mawuwo akatifika pamtima, zinthu zimatiyendera bwino chifukwa umunthu watsopano umene timavala umatiteteza ku misampha ya Satana.
20 Mtumwi Petulo ananena kuti: ‘Monga ana omvera, lekani kukhala motsatira zilakolako zimene munali nazo kale koma khalani oyera m’makhalidwe anu onse.’ (1 Pet. 1:14, 15) Nkhani yotsatira ikusonyeza kuti tikamayesetsa kuchotsa maganizo akale n’kusandulika, tidzadalitsidwa kwambiri.
^ ndime 18 Onani chitsanzo chimene chili mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 1994, tsamba 10, ndime 7.