Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti “palibe amene amathira vinyo watsopano m’matumba achikopa akale”?

M’nthawi za m’Baibulo, anthu ankakonda kusunga vinyo m’matumba achikopa. (Yoswa 9:13) Zikopazi zinkakhala za nyama zoweta, monga mbuzi zazing’ono ndi zazikulu zomwe. Kuti apange thumba lachikopa, iwo ankapha nyama n’kuidula mutu ndi miyendo ndipo kenako ankaisenda mwaluso kuti asaiboole pamimba. Akamaliza kusendako, ankafufuta chikopacho. Kenako ankasoka mabowo onse n’kungosiya khosi lokha kapena mwendo umodzi kuti pakhale kamwa la thumbalo. Akafuna kutseka pakamwapo, ankalowetsapo chinthu chinachake kapena kumangapo ndi chingwe.

Chikopacho chikakhalitsa chinkauma, moti chinkasiya kutanuka. Choncho matumba achikopa akale sanali abwino kusungiramo vinyo watsopano chifukwa vinyoyo amakhala akuwirabe kapena kuti kupesa. Motero ngati chikopa chili chakale chingalephere kutanuka ndipo chingathe kung’ambika mosavuta. Koma zimenezi sizingachitike ngati chikopa chili chatsopano, chifukwa chimakhala chofewa motero chingathe kutanuka mosavuta vinyo watsopanoyo akamawira. Poganizira zimenezi, Yesu anafotokoza zinthu zomwe anthu ambiri m’nthawi yake ankazidziwa. Ponena zimene zingachitike ngati munthu ataika vinyo watsopano m’matumba achikopa akale, iye anati: “Vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba achikopawo, ndipo amatayika ndipo matumba achikopawo amawonongeka. Koma vinyo watsopano ayenera kuikidwa m’matumba achikopa atsopano.”​—Luka 5:37, 38.

Kodi anthu amene anatchulidwa kuti “zigawenga” pamene Aroma ankamanga Paulo anali ndani?

Buku la Machitidwe limafotokoza kuti nthawi ina kukachisi wa ku Yerusalemu kunachitika chipwirikiti ndipo mtsogoleri wa asilikali achiroma anamanga Paulo pomuganizira kuti anali mtsogoleri wa gulu lina la “zigawenga 4,000,” lomwe linaukira boma. (Machitidwe 21:30-38) Kodi anthu oukira bomawa anali ndani?

Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “zigawenga” anachokera ku mawu a Chilatini (sicarii) omwe amatanthauza kuti “anthu ogwiritsira ntchito sica,” kapena kuti lupanga. Wolemba mbiri wina wa m’nthawi ya atumwi, dzina lake Flavius Josephus anafotokoza kuti anthu amenewa anali kagulu ka Ayuda okondetsa kwambiri dziko lawo ndipo ankadana ndi Aroma kwadzaoneni, moti ankakonza chiwembu n’kumapha Aromawo.

Josephus anati anthu amenewa “ankapha anthu m’kati mwa mzinda ngakhale masana dzuwa likuswa mtengo; ndipo ankakonda kuchita zimenezi pazikondwerero. Iwo ankalowerera m’chigulu cha anthu atabisa malupanga afupiafupi m’zovala zawo, ndipo ankabaya adani awo ndi malupangawo.” Adaniwo akafa, zigawengazi zinkanamizira kukhumudwa kwambiri ndi imfayo kuti zisadziwidwe. Josephus anatchulaponso kuti zigawengazi zinathandiza kwambiri panthawi imene Ayuda anaukira Roma mu 66 mpaka 70 C.E. Motero m’pomveka kuti mtsogoleri wa asirikali achiroma ankafunitsitsa kumanga Paulo poganiza kuti anali mtsogoleri wa gulu limeneli.

[Chithunzi patsamba 15]

Thumba Lachikopa Lakale

[Chithunzi patsamba 15]

Chithunzi Chojambula Pamanja cha Chigawenga