Kodi Zipembedzo Mungazikhulupirire pa Nkhani ya Nkhondo?
Alberto anakhala akugwira ntchito ya usilikali kwa zaka pafupifupi 10. Iye anati: “Tisanapite ku nkhondo, wansembe ankatidalitsa ndi mawu akuti, ‘Mulungu akhale nanu.’ Koma ndinkadzifunsa kuti, ‘Ndikupita kukapha anthu, si paja Baibulo limati “usaphe”?’”
Ray anali msilikali wapanyanja ndipo anamenya nawo nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Tsiku lina iye anafunsa wansembe kuti: “Tisanapite ku nkhondo, mumadzatipempherera kuti tikapambane. Kodi anthu amene tikukamenyana nawowo samachitanso zomwezi?” Wansembeyo anangomuyankha kuti palibe amene angamvetse zochita za Mulungu.
Ngati mukuona kuti yankho limene wansembeyu anapereka ndilosamveka, dziwani kuti si inu nokha amene mukuona choncho.
KODI BAIBULO LIMATI CHIYANI PA NKHANI YA NKHONDO?
Yesu ananena kuti limodzi mwa malamulo awiri ofunika kwambiri ndi lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Maliko 12:31) Yesu sananene kuti tizingokonda mnzathu amene timakhala naye m’dziko limodzi kapena wa mtundu wathu wokha. Iye anauza ophunzira ake kuti: ‘Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana.’ (Yohane 13:34, 35) Ophunzira a Yesu afunika kukondana kwambiri moti khalidwe limeneli liyenera kukhala chizindikiro chawo. M’malo mopha anzawo, iwo ayenere kulolera kufa chifukwa chofuna kupulumutsa moyo wa Akhristu anzawo.
Akhristu oyambirira ankayesetsa kukondana potsatira zimene Yesu ananena. Buku lina linanena kuti: “Atsogoleri a chipembedzo akale, monga Tertullian ndi Origen, ananena kuti Akhristu ankakhulupirira kuti sayenera kupha munthu. Mfundo imeneyi inkawachititsa kuti asamalowe nawo m’gulu la asilikali achiroma.”—The Encyclopedia of Religion.
KODI A MBONI ZA YEHOVA AMATANI PA NKHANIYI?
Chifukwa chakuti a Mboni za Yehova amapezeka pafupifupi dziko lililonse, nthawi zina zingachitike kuti dziko lawo lingayambe nkhondo ndi dziko lina. Koma iwo amayesetsa kupewa kumenya nawo nkhondo chifukwa chokonda abale awo.
Kodi atsogoleri achipembedzo aphunzitsadi anthu kuti azikondana?
Mwachitsanzo, a Mboni za Yehova sanamenye nawo nkhondo yapachiweniweni imene inachitika ku Rwanda mu 1994, pakati pa Ahutu ndi Atutsi. Anthu a Mboni a mitundu iwiriyi ankatha kutetezana pa nthawi yankhondoyi ngakhale kuti akanatha kuphedwa chifukwa cha zimenezi. Nthawi ina asilikali achihutu a gulu la Interahamwe anagwira a Mboni awiri a mtundu wa chihutu chifukwa choti ankabisa Akhristu anzawo achitutsi. Asilikaliwo anauza a Mboni awiriwo kuti: “Tikuphani chifukwa choti mwathandiza Atutsi kuti athawe.” N’zomvetsa chisoni kuti asilikaliwo anaphadi a Mboniwo.—Yohane 15:13
Kodi mukuganiza kuti zimene a Mboni za Yehova amachitazi n’zogwirizana ndi mawu a Yesu akuti tizilolera kufera ena chifukwa cha chikondi?