Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ANTHU OMWE ANAMWALIRA ADZAKHALANSO NDI MOYO?

Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo

Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo

Betaniya inali tauni yomwe inali pamtunda wamakilomita atatu kuchokera ku Yerusalemu. (Yohane 11:18) Kutatsala milungu ingapo kuti Yesu aphedwe, kuderali kunachitika nkhani yomvetsa chisoni. Lazaro, yemwe anali mnzake wapamtima wa Yesu anadwala kwambiri ndipo kenako anamwalira.

Yesu atamva nkhaniyi, anauza ophunzira ake kuti Lazaro akugona ndipo akufuna apite kukamudzutsa. (Yohane 11:11) Koma ophunzirawo sanamvetse zimene ankatanthauza, choncho Yesu anawauza momveka bwino kuti: “Lazaro wamwalira.”—Yohane 11:14.

Patatha masiku 4 kuchokera pamene Lazaro anaikidwa m’manda, Yesu anafika ku Betaniya n’cholinga choti akapepese Marita yemwe anali mlongo wake wa Lazaro. Marita anauza Yesu kuti: “Mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.” (Yohane 11:17, 21) Koma Yesu anamuyankha kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo. Aliyense wokhulupirira mwa ine, ngakhale amwalire, adzakhalanso ndi moyo.”—Yohane 11:25.

“Lazaro, tuluka!”

Pofuna kusonyeza kuti zimene ankanenazi zinali zoona, Yesu anapita pamanda pamene Lazaro anaikidwa n’kunena kuti: “Lazaro, tuluka!” (Yohane 11:43) Anthu onse amene anali pamalowa anadabwa kwambiri ataona kuti Lazaro wadzukadi.

Pa nthawiyi, n’kuti Yesu ataukitsapo kale anthu awiri. Mmodzi mwa anthu amenewa anali kamtsikana, komwe kanali mwana wa Yairo. Yesu asanaukitse mtsikanayu, ananenanso kuti mwanayo akugona.—Luka 8:52.

Onani kuti ponena za imfa ya Lazaro komanso mwana wamkazi wa Yairo, Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. M’pake kuti Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa choti munthu akagona tulo tofa nato samva ululu uliwonse ndipo izi n’zofanana ndi zimene zimachitika munthu akafa. (Mlaliki 9:5; onani bokosi lakuti  “Imfa Ili Ngati Tulo Tofa Nato.”) Ophunzira oyambirira  a Yesu ankadziwa bwino zimene zimachitikira munthu akamwalira. Buku lina linanena kuti, ‘ophunzira a Yesu ankaona kuti kwa anthu amene amwalira ndi chikhulupiriro, imfa ili ngati tulo ndipo manda ali ngati malo amene amakapumako, osamvanso ululu.’ *Encyclopedia of Religion and Ethics.

N’zolimbikitsa kudziwa kuti anthu amene anamwalira akugona m’manda ndipo sakuvutika. Choncho imfa si chinthu chosamvetsetseka ndipo sitiyenera kuiopa.

“MUNTHU AKAFA, KODI ANGAKHALENSO NDI MOYO?”

Ngakhale kuti anthufe timasangalala kugona tulo tabwino, palibe amene amafuna kumangogona osadzukanso mpaka kalekale. Ndiyeno kodi anthu amene anamwalira adzaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo ngati mmene zinakhalira ndi Lazaro ndiponso mwana wamkazi wa Yairo?

Yobu anafunanso funso la ngati lomweli atadwala kwambiri. Iye anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?”—Yobu 14:14.

Polankhula ndi Mulungu Wamphamvuyonse, Yobu anayankha funso lakeli ponena kuti: “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:15) Yobu ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova amalakalaka tsiku limene adzaukitse mtumiki wakeyu. Kodi apa Yobu ankangoganiza za zinthu zosatheka? Ayi ndithu.

Zimene Yesu anachita poukitsa anthu, ndi umboni wosonyeza kuti Mulungu anamupatsa mphamvu yogonjetsa imfa. Ndipotu Baibulo limati Yesu ali ndi “makiyi a imfa ndi a Manda.” (Chivumbulutso 1:18) Choncho tingati Yesu adzatsegula manda kuti akufa atulukemo, ngati mmene anachitira polamula kuti chimwala chimene chinaikidwa pamanda a Lazaro, chichotsedwe.

M’Baibulo muli mavesi ambirimbiri amene amanena zoti akufa adzaukitsidwa. Mwachitsanzo mngelo anauza Danieli kuti: “Udzapuma. Koma udzauka kuti ulandire gawo lako pa mapeto a masikuwo.” (Danieli 12:13) Komanso polankhula ndi Asaduki, omwe anali atsogoleri achipembedzo achiyuda ndipo sankakhulupirira zoti akufa adzauka, Yesu anati: “Mukulakwitsa chifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.” (Mateyu 22:23, 29) Nayenso mtumwi Paulo anati: “Ine ndili ndi chiyembekezo mwa Mulungu, . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15.

KODI AKUFA ADZAUKITSIDWA LITI?

Koma kodi anthu olungama ndi osalungama amene anamwalira adzaukitsidwa liti? Kumbukirani kuti mngelo anauza Danieli kuti adzauka “pa mapeto a masikuwo.” Komanso Marita ankakhulupirira kuti mchimwene wake Lazaro, “adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.”—Yohane 11:24.

Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa ‘tsiku lomaliza’ ndi Ufumu wa Khristu. Paulo analemba kuti: “Pakuti [Khristu] ayenera kulamulira monga mfumu kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.” (1 Akorinto 15:25, 26) Ichitu n’chifukwa chake tiyenera kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere komanso kuti chifuniro chake chichitike padziko lapansi pano. *

Mulungu akufunitsitsa kudzaukitsa akufa ndipo Yobu ankadziwa bwino zimenezi. Tsiku limeneli likadzafika, imfa idzawonongedwa ndipo palibenso amene azidzadabwa kuti, ‘Kodi anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo?’

^ ndime 8 Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “manda” amatanthauza “malo ogona.”

^ ndime 18 Kuti mudziwe zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu, werengani mutu 8 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.