NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ANTHU OMWE ANAMWALIRA ADZAKHALANSO NDI MOYO?
Imfa Ndi Yopweteka Kwambiri
Anthu ambiri safuna kukamba nkhani yokhudza imfa chifukwa imfa ndi chinthu chowawa kwambiri. Komabe, zoona n’zoti nthawi ina ifeyo, kapena anthu amene timawakonda, tidzamwalira.
Munthu amene tinkamukonda kwambiri akamwalira, anthufe timadandaula ngakhale zitakhala kuti zinali zodziwikiratu kuti munthuyo amwalira. Nthawi zina munthu amafa mwadzidzidzi, pomwe nthawi zina amadwala kwa nthawi yaitali. Kaya munthu wamwalira mwadzidzidzi kapena ayi, imfa imakhala yowawa kwambiri.
Antonio, yemwe bambo ake anamwalira pa ngozi ya pamsewu, ananena kuti: “Zinali ngati munthu wina wakhoma nyumba yathu n’kutenga makiyi ndipo sitingathenso kulowa m’nyumbayo. Imfa ikachitika, umangokumbukira za imfayo basi ndipo zimakhala zovuta kuzivomereza. Koma zimakhala kuti zachitika basi.”
Mayi wina wazaka 47, dzina lake Dorothy amene mwamuna wake anamwalira, ankafuna kudziwa mayankho okhudza imfa. Iye anali mphunzitsi wa Sande Sukulu ndipo ankadziwa kuti imfa si mapeto a zonse. Koma anali ndi mafunso ambiri okhudza imfa. Anafunsa m’busa wawo wa Anglican funso lakuti, “Kodi chimamuchitikira n’chiyani munthu akamwalira?” Koma m’busayo anamuyankha kuti, “Palibe angadziwe, tingodikira mwina tidzadziwa yankho lake m’tsogolo.”
Kodi tikufunikadi tingodikira kuti tidzadziwe mayankho okhudza imfa m’tsogolo? Kodi n’zosatheka kudziwa zolondola pa nkhaniyi panopa?