Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | YOSEFE

“Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”

“Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”

YOSEFE anali ataima m’munda wake womwe unali pafupi ndi nyumba yawo. Pa nthawiyi n’kuti kunja kuli kachisisira. N’kutheka kuti ankayang’ana madamu amadzi komanso zipatso za mitengo ya kanjedza ndi zipatso zina, zomwe zinali zitakhwima. Akaponya maso chakutsogolo, ankaona nyumba yachifumu ya Farao. Mwina pa nthawiyi ankamvanso kaphokoso kuchokera m’nyumba mwake. Ankamva mwana wake woyamba Manase, akusewera ndi mng’ono wake Efuraimu, yemwe pa nthawiyi anali wakhanda. N’kutheka kuti Yosefe ankaganiza kuti mkazi wake ayenera kuti akuseka poona Manase akusewera ndi mng’ono wakeyo. Ndiyeno yerekezerani kuti mukuona Yosefe akumwetulira podziwa kuti Yehova akumudalitsa.

Yosefe anapatsa mwana wake woyamba dzina lakuti Manase lomwe limatanthauza, “woiwalitsa mavuto.” (Genesis 41:51) Pa nthawiyi n’kuti Yehova atadalitsa kwambiri Yosefe. Izi zinachititsa kuti aiwaleko bambo ake, aiwale kwawo komanso kuti aiwale zimene azichimwene ake anamuchitira. Azichimwene akewo ankadana naye ndipo ankafuna kumupha. Koma kenako anamugulitsa kwa amalonda omwe ankapita ku Iguputo. Atafika ku Iguputo, anali kapolo wa Potifara ndipo kenako anamangidwa n’kuikidwa m’ndende. Moyo wakundendeko unali wowawa kwambiri chifukwa nthawi zambiri akaidi ankawamanga m’matangadza. Koma kenako zinthu zinasintha pa moyo wa Yosefe ndipo anali wachiwiri kwa Farao, mfumu ya Iguputo. *

Kwa zaka 7, Yosefe anaona mawu a Yehova akukwaniritsidwa. Pa zaka 7 zimenezo, m’dziko la Iguputo munali chakudya chamwanaalirenji ndipo Yosefe ankayang’anira ntchito yosunga chakudya m’nkhokwe kuti adzachigwiritse ntchito pa nthawi yanjala. Pa nthawiyi anakwatira mkazi wotchedwa Asenati, n’kubereka naye ana awiri aja. Komabe sikuti Yosefe anaiwaliratu kwawo. Ankakumbukirabe mng’ono wake Benjamini komanso bambo ake, a Yakobo, omwe ankawakonda kwambiri. Ankawadera nkhawa ndipo ankafunitsitsa atadziwa mmene alili. Ankafunanso kudziwa ngati azichimwene ake anasintha makhalidwe awo oipa. Komanso ankalakalaka banja lawo litadzakhalanso limodzi mosangalala.

Kodi nanunso banja lanu siligwirizana chifukwa chodana, nsanje komanso kusakhulupirika? Ngati ndi choncho, nkhani ya Yosefe ingakuthandizeni kwambiri. Kodi tingatsatire bwanji chikhulupiriro chake poona zimene anachitira azichimwene ake?

“PITANI KWA YOSEFE”

Popeza Yosefe anali ndi udindo waukulu, anali munthu wotanganidwa kwambiri. Mogwirizana ndi maloto omwe Yehova analotetsa Farao, zitatha zaka 7 za chakudya chambiri, kunabwera zaka zina 7 zanjala. Pasanapite nthawi, anthu a m’madera oyandikana ndi dziko la Iguputo anayamba kuvutika ndi njala. Koma Baibulo limati: “Dziko lonse la Iguputo linali ndi chakudya.” (Genesis 41:54) Anthu a ku Iguputo sanavutike ndi njala chifukwa choti Yehova anathandiza Yosefe kudziwa tanthauzo la maloto a Farao. Komanso chifukwa choti Yosefe anawauza pulani yabwino yoti asungiretu chakudya.

Yehova anamugwiritsa ntchito Yosefe chifukwa anali wodzichepetsa

Anthu a ku Iguputo ankamulemekeza kwambiri Yosefe chifukwa ankamuona kuti ndi munthu wanzeru. Koma Yosefe ankafuna kuti anthuwo azilemekeza Yehova, chifukwa ndiye anachititsa zonsezi. Ifenso ngati tili ndi luso linalake, tizitumikira Mulungu modzichepetsa. Tikatero, Mulungu angatigwiritse ntchito kuposa mmene timaganizira.

Komabe patapita nthawi, anthu a ku Iguputo anayamba kusowa chakudya. Choncho ankapita kwa Farao kukadandaula. Faraoyo ankawauza kuti: “Pitani kwa Yosefe! Zilizonse zimene akuuzeni, chitani zomwezo.” Choncho Yosefe anatsegula nkhokwe zija n’kumawagulitsa anthuwo chakudya.—Genesis 41:55, 56.

Koma njala inafika poipa m’madera oyandikana ndi dziko la Iguputo. Azichimwene ake a Yosefe ankakhala ku Kanani, ndipo nawonso anayamba kuvutika ndi njala. Yakobo, yemwe pa nthawiyo anali wokalamba, anamva kuti ku Iguputo kuli chakudya. Choncho anauza ana ake kuti apite ku Iguputo kukagula tirigu.—Genesis 42:1, 2.

Yakobo anatumiza ana ake 10 kuti apite ku Iguputo. Mwana wake womaliza anali Benjamini, koma sanamulole kuti apite nawo. Anachita zimenezi chifukwa ankakumbukira zomwe zinachitika atatumiza Yosefe kuti akaone azichimwene ake, komwe ankadyetsa ziweto. Yosefe atapita sanabwerenso. Azichimwene akewo anabwera ndi chovala cha Yosefe chili chong’ambika komanso chili magazi okhaokha. Zimenezi zinachititsa Yakobo kukhulupirira kuti Yosefe anadyedwa ndi chilombo.—Genesis 37:31-35.

“NTHAWI YOMWEYO YOSEFE ANAKUMBUKIRA”

Atayenda kwa masiku ambiri, ana a Yakobo anafika ku Iguputo. Atafunsa komwe angakagule chakudya, anauzidwa kuti apite kwa mkulu waboma wotchedwa Zafenati-panea. (Genesis 41:45) Kodi atamuona anazindikira kuti ndi Yosefe? Ayi ndithu. Anangoona kuti apeza munthu waudindo waukulu basi. Choncho “anamugwadira n’kumuweramira mpaka nkhope zawo pansi.”—Genesis 42:5, 6.

Koma Yosefe anawazindikira azichimwene akewo. Atawaona akumugwadira posonyeza ulemu, anakumbukira zomwe analota zaka zambiri m’mbuyomo. Nkhaniyi imati: “Nthawi yomweyo Yosefe anakumbukira maloto” onena kuti azichimwene ake adzamugwadira, amene Yehova anamulotetsa ali mnyamata. (Genesis 37:2, 5-9; 42:7, 9) Ndiye kodi Yosefe anatani? Kodi anathamanga n’kuwakumbatira? Kapena anaganiza zowabwezera zoipa zomwe anamuchitira zija?

Yosefe anaona kuti si bwino kuwabwezera. Komabe anaonanso kuti si bwino kuwakumbatira pa nthawiyi. Anadziwa kuti Yehova ndi amene akuchititsa zonsezi pofuna kukwaniritsa cholinga chake. Anali atalonjeza kuti adzapangitsa kuti ana a Yakobo akhale mtundu waukulu. (Genesis 35:11, 12) Azichimwene ake a Yosefe akanakhala kuti anali adakali achiwawa, odzikonda komanso osakhulupirika, cholinga cha Yehova chikanasokonekera. Komanso Yosefe akanapanga zinthu mopupuluma, mwina zikanabweretsa mavuto ena m’banja lawo, mwinanso kuika pachiswe moyo wa bambo awo ndi wa Benjamini. Komanso pa nthawiyi Yosefe sankadziwa ngati bambo ake ndi Benjamini adakali moyo. Choncho anaona kuti ndi bwino kuti adekhe kaye. Anadziwa kuti zimenezi zimuthandiza kudziwa ngati azichimwene ake anasintha makhalidwe awo oipa komanso zidzamuthandiza kudziwa zomwe Yehova akufuna kuti iyeyo achite.

Mwina zimene zinachitikira Yosefe, sizingakuchitikireni inuyo ndendende. Koma masiku ano anthu a m’mabanja ambiri amadana komanso amachitirana nsanje. Zoterezi zikachitika, anthu ambiri amaganiza zobwezera. Koma ndi bwino kutsanzira Yosefe. Ndi bwinonso kuganiza zomwe tingachite kuti tisangalatse Yehova zoterezi zikachitika. (Miyambo 14:12) Musaiwale kuti kukhala pa mtendere ndi anthu a m’banja lathu komanso ndi Mulungu n’kofunika kwambiri.—Mateyu 10:37.

“NDIKUYESANI”

Yosefe anakonza zowayesa azichimwene akewo kuti aone ngati anasintha. Anayamba ndi kuwalankhula mwaukali kudzera mwa womasulira. Anawauza azichimwene akewo kuti ndi akazitape ndipo abwera kudzaona dziko lawolo. Koma iwo anakanitsitsa kuti si akazitape ndipo anamuuza zoti ali ndi mng’ono wawo yemwe watsala kunyumba. Yosefe atamva kuti mng’ono wake adakali moyo, anasangalala kwambiri. Komabe anayesetsa kuugwira mtima kuti asadziwike kuti wasangalala ndi zomwe wamvazo. Kenako anawauza kuti: “Ndikuyesani.” Ndiyeno anawauza kuti adzabwere ndi mng’ono wawoyo kuti adziwe ngati akunena zoona. Atakambirana nawo kwa kanthawi, anawauza kuti apite kukatenga mng’ono wawoyo, koma mmodzi wa iwo atsale ndipo akhale mkaidi.—Genesis 42:9-20.

Azichimwene ake a Yosefe anayamba kukambirana za nkhaniyi m’chinenero chawo. Ankaganiza kuti zonsezi zikuchitika chifukwa cha zoipa zomwe anachita zija. Koma sankadziwa kuti Yosefe akumva chinenero chawocho. Ankakambirana kuti: “Ndithudi, izi zikuchitika chifukwa cha zimene tinachitira m’bale wathu uja. Pajatu tinaona kusautsika kwake pamene anatichonderera kuti timumvere chisoni, koma ife sitinalabadire. N’chifukwa chake tsokali latigwera.” Yosefe atamva zimenezi, anapita payekha kukalira. (Genesis 42:21-24) Komabe anadziwa kuti munthu akazindikira kuti akukumana ndi mavuto chifukwa cha zoipa zomwe anachita, si chizindikiro choti walapa. Choncho anapitirizabe kuwayesa.

Kenako azichimwene akewo ananyamuka ndipo Simiyoni anatsala. Koma Yosefe anatenga ndalama zomwe anthuwa ankafuna kugulira tirigu n’kuziika m’matumba awo a tirigu. Atafika kwawo, anafotokozera Yakobo zonse zomwe zinachitika. Itakwana nthawi yoti apitenso ku Iguputo, anachonderera Yakobo kuti awalole kutenga Benjamini. Atafika ku Iguputoko, anauza mtumiki wa Yosefe kuti anapeza ndalama m’matumba awo ndipo analonjeza kuti abweza ndalamazo. Komabe Yosefe anaona kuti zimenezi sizokwanira kumuthandiza kudziwa kuti asintha. Choncho anaganiza zopitirizabe kuwayesa. Chifukwa choti Yosefe anasangalala kwambiri kuona Benjamini, anawakonzera phwando. Koma anayesetsa kuti azichimwene ake asadziwe kuti wachita zimenezi chifukwa chosangalala. Kenako anawapatsa tirigu wambiri ndipo iwo anayamba ulendo wobwerera kwawo. Koma Yosefe anaika kapu yake yasiliva m’thumba la Benjamini.—Genesis 42:26–44:2.

Azichimwene akewo atanyamuka, Yosefe anauza mtumiki wake kuti awatsatire. Atawapeza, anawauza kuti aba kapu ya Yosefe. Kenako anayamba kufufuza kapuyo m’matumba awo ndipo anaipeza m’thumba la Benjamini. Zitatere, onse anabwereranso kwa Yosefe. Apa Yosefe anapeza mpata woti ayesenso azichimwene akewo. Yuda ndi amene ankalankhula m’malo mwa onsewa. Anachonderera Yosefe kuti awakhululukire mpaka anafika ponena kuti awatenge onse kuti akhale akapolo a ku Iguputo. Koma Yosefe anakana n’kunena kuti Benjamini yekha ndiye akhale kapolo wake chifukwa ndi amene wapezeka ndi kapu, enawo azipita.—Genesis 44:2-17.

Koma Yuda atamva zimenezi, anamva chisoni kwambiri moti anayankha kuti: “M’bale wake wa mimba imodzi anamwalira, moti anatsala yekha, ndipo bambo amam’konda kwambiri.” Ziyenera kuti zinamukhudza kwambiri Yosefe atamva mawu amenewa chifukwa anadziwa kuti akunena za iyeyo. Yosefe anali mkulu wake wa Benjamini ndipo mayi awo anali a Rakele. Mayi awowo anamwalira pamene ankabereka Benjamini. Mofanana ndi bambo ake, a Yakobo, Yosefe ayenera kuti ankakumbukirabe mayi ake chifukwa ankawakonda kwambiri. Yosefe ankakonda kwambiri Benjamini chifukwa anali ana a mayi mmodzi.—Genesis 35:18-20; 44:20.

Yuda anapitiriza kuchonderera Yosefe kuti asatenge Benjamini n’kukhala kapolo wake. Mpaka anauza Yosefe kuti atenge iyeyo m’malo mwa Benjamini. Kenako ananena mawu okhudza mtima kwambiri. Anati: “Ndingathe bwanji kupita kwa bambo anga ndilibe mwanayu? Ayi, sindikufuna kukaona bambo anga akuzunzika ndi chisoni.” (Genesis 44:18-34) Zimenezi zinasonyezeratu kuti Yuda anasintha kwambiri. Zinasonyeza kuti analapa zoipa zomwe anachitira Yosefe zija komanso kuti tsopano anali wachifundo ndi woganizira ena.

Yosefe anaona kuti azichimwene ake azindikira kulakwa kwawo

Apa Yosefe analephera kupirira. Choncho anauza anthu onse kuti atuluke n’kutsala azichimwene ake okha. Kenako anadziulula kwa azichimwene akewo kuti: “Ndine Yosefe!” Azichimwene akewo anadabwa kwambiri ndi zimenezi. Koma Yosefe anawakumbatira posonyeza kuti anawakhululukira. (Genesis 45:1-15) Apatu Yosefe anasonyeza kuti ankatsanzira Yehova, yemwe amakhululuka ndi mtima wonse. (Salimo 86:5) Kodi inunso mumakhululuka ndi mtima wonse?

“UKADALI NDI MOYO”

Farao atamva zomwe zinachitikazi, anauza Yosefe kuti aitane bambo ake ndi banja lawo lonse kuti asamukire ku Iguputo. Choncho pasanapite nthawi, banja lonse la Yakobo linabwera ku Iguputo ndipo Yosefe anasangalala kwambiri kukumananso ndi bambo ake. Yakobo ataona Yosefe, analira ndipo ananena kuti: “Ndingathe kufa tsopano chifukwa ndaona nkhope yako, popeza ukadali ndi moyo.”—Genesis 45:16-28; 46:29, 30.

Koma sikuti Yakobo anafadi nthawi yomweyo. Iye anakhalanso ndi moyo zaka zina 17. Atatsala pang’ono kumwalira anadalitsa ana ake onse 12. Yosefe analandira madalitso omwe mwana woyamba kubadwa ankalandira. Anamuuza kuti mitundu iwiri ya Isiraeli idzachokera kwa iye. Yuda, yemwe anali wa nambala 4 kubadwa anadalitsidwanso kwambiri chifukwa anasonyeza mtima wolapa. Anamuuza kuti Mesiya adzachokera kubanja lake.—Genesis chaputala 48 ndi 49.

Kenako Yakobo anamwalira ali ndi zaka 147. Zitatero, azichimwene ake a Yosefe anayamba kuchita mantha kuti mwina Yosefe akhoza kuwabwezera. Koma Yosefe amawatsimikizira mokoma mtima kuti sawabwezera. Anawauza kuti asadziimbe mlandu popeza chinali cholinga cha Yehova kuti banja lawolo lipite ku Iguputo. Kenako anawafunsa kuti: “Kodi ine ndatenga malo a Mulungu?” (Genesis 15:13; 45:7, 8; 50:15-21) Yosefe ankadziwa kuti Yehova ndiye woweruza wachilungamo. Choncho anaona kuti palibe chifukwa chokhaulitsira anthu omwe Yehova wawakhululukira.—Aheberi 10:30.

Kodi inuyo zimakuvutani kukhululuka? Zimakhaladi zovuta kukhululukira munthu, makamaka ngati watilakwira mwadala. Koma tikamayesetsa kukhululukira munthu amene walapa, zimathandiza kuti munthuyo komanso ifeyo, tikhale ndi mtendere wa mumtima. Timasonyezanso kuti tikutsanzira chikhulupiriro cha Yosefe komanso kuti tikutsanzira Yehova, yemwe ndi wachifundo.

^ ndime 4 Onani nkhani zakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2014, November 1, 2014 ndi ya February 1, 2015.