Baibulo Lingakuthandizeni Kukhala Ololera
“Kulolera ndi khalidwe limene lingachititse kuti m’dzikoli mukhale mtendere.”—UNESCO Declaration of Principles on Tolerance, 1995.
Koma kukhala osalolera kungachititse kuti anthu akhale amwano komanso akhale ndi chidani mumtima. Nthawi zambiri zimenezi zimachititsa kuti anthu azinyoza, kusala ndiponso kuchitira zachiwawa anthu ena.
Komabe anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya zimene kulolera kumatanthauza. Anthu ena amakhulupirira kuti munthu wololera amafunika kumavomereza zilizonse zimene anthu amachita. Pomwe ena amayendera maganizo amene Baibulo limalimbikitsa kuti munthu wololera amalemekeza ufulu wa munthu aliyense wosankha mfundo zomwe aziyendera komanso kukhulupirira, ngakhale zitakhala kuti sakugwirizana nazo.
Koma kodi n’zoona kuti Baibulo lingathandize anthu kukhala ololera masiku ano?
Zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kulolera
Baibulo limalimbikitsa anthu kukhala ololera. Limati: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” (Afilipi 4:5) Baibulo limatilimbikitsa kukhala oganizira ena, kumawalemekeza komanso kuwachitira zachilungamo. Anthu omwe amatsatira malangizo amenewa mwina sangagwirizane ndi mfundo zimene munthu wina amatsatira, koma amalola kuti munthuyo azichita zimene wasankha.
Komabe, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu ali ndi mfundo zomwe amafuna kuti anthu azitsatira. Limati: “[Mulungu] anakuuza munthu iwe zimene zili zabwino.” (Mika 6:8) Limafotokoza malangizo omwe Mulungu amapatsa anthu kuti anthuwo azikhala osangalala.—Yesaya 48:17, 18.
Mulungu sanatipatse udindo woweruza ena. Baibulo limanena kuti, “Wopereka Malamulo komanso Woweruza alipo mmodzi yekha . . . Ndiye iwe ndiwe ndani kuti uziweruza mnzako?” (Yakobo 4:12) Mulungu amalola kuti munthu aliyense payekha azikhala ndi ufulu wosankha zochita ndipo aliyense amakumana ndi zotsatira za zomwe wasankha.—Deuteronomo 30:19.
Zimene Baibulo limanena pa nkhani yolemekeza ena
Baibulo limanena kuti tiyenera “kulemekeza aliyense.” (1 Petulo 2:17, New Jerusalem Bible) Choncho anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo amalemekeza anthu onse posatengera zimene anthuwo amakhulupirira komanso zimene amachita. (Luka 6:31) Zimenezi sizikutanthauza kuti anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo amavomereza zikhulupiriro zilizonse kapena maganizo alionse omwe anthu ena ali nawo, kapenanso zimene anthuwo asankha. Koma m’malo mowachitira zamwano kapena kusawalemekeza, amayesetsa kutsanzira mmene Yesu ankachitira zinthu ndi anthu.
Mwachitsanzo, nthawi ina Yesu anakumana ndi mayi yemwe anali wosiyana naye chipembedzo. Mayiyu ankakhalanso ndi mwamuna woti sanali wake ndipo Yesu sankavomereza khalidwe limeneli. Komabe, iye analankhula naye mwaulemu.—Yohane 4:9, 17-24.
Mofanana ndi Yesu, Akhristu amakhala okonzeka kufotokoza zifukwa zimene zimawachititsa kukhulupirira zinazake kwa anthu omwe angafune kumvetsera, koma amachita zimenezi “mwaulemu kwambiri.” (1 Petulo 3:15) Baibulo limauza Akhristu kuti asamakakamize ena kutsatira zomwe Akhristuwo amakhulupirira. Limati munthu wotsatira Khristu “sayenera kukangana ndi anthu. Koma ayenera kukhala wodekha kwa onse,” kuphatikizapo omwe amasiyana nawo zimene amakhulupirira.—2 Timoteyo 2:24.
Zimene Baibulo limanena pa nkhani yodana ndi ena
Baibulo limatiuza kuti ‘tiziyesetsa kukhala mwamtendere ndi anthu onse.’ (Aheberi 12:14) Munthu amene amayesetsa kukhala mwamtendere sadana ndi ena. Ngakhale kuti sachita zinthu zosemphana ndi mfundo zomwe amatsatira, iye amachita chilichonse chomwe angathe kuti azikhala mwamtendere ndi ena. (Mateyu 5:9) Ndipotu Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti azikonda adani awo pochita zinthu mokoma mtima kwa anthu omwe amawachitira zoipa.—Mateyu 5:44.
N’zoona kuti Baibulo limati Mulungu “amadana” kapena “amanyansidwa ” ndi zinthu zomwe zimachotsera anthu ulemu kapenanso kuwavulaza. (Miyambo 6:16-19) Koma Baibulo palembali limagwiritsa ntchito mawu akuti “amanyansidwa” ponena za kudana kwambiri ndi zinthu zoipa. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu ndi wofunitsitsa kukhululukira anthu omwe akufuna kusintha zomwe amachita n’kumatsatira mfundo zake.—Yesaya 55:7.
Mavesi a m’Baibulo onena za kulolera ndiponso kulemekeza ena
Tito 3:2: “Akhale ololera ndipo azikhala ofatsa kwa anthu onse.”
Munthu wololera amachita zinthu modekha kwa anthu osiyana naye maganizo, zomwe zimachititsa kuti anthu azilemekezana.
Mateyu 7:12: “Choncho zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”
Tonsefe timasangalala anthu ena akatichitira zinthu mwaulemu ndiponso akamaganizira mmene tikuonera zinthu komanso mmene tikumvera. Kuti mudziwe zambiri zokhudza lamulo limene Yesu anaphunzitsali, lomwe ndi lotchuka, onani nkhani yakuti “Kodi Yesu Anapereka Lamulo Lotani Lokhudza Kuchita Zinthu ndi Ena?”
Yoswa 24:15: “Sankhani lero amene mukufuna kumʼtumikira.”
Tikamalemekeza ufulu wa ena wosankha zochita, timalimbikitsa mtendere.
Machitidwe 10:34: “Mulungu alibe tsankho.”
Mulungu sasankha aliyense chifukwa cha chikhalidwe, kuti ndi mwamuna kapena mkazi komanso dziko lomwe akuchokera. Anthu omwe akufuna kutsanzira Mulungu amalemekeza munthu aliyense.
Habakuku 1:12, 13: ‘Mulungu sangalekerere khalidwe loipa.’
Sikuti Mulungu amangololera zilizonse. Iye sadzalola kuti anthu azingochita makhalidwe oipa mpaka kalekale. Kuti mudziwe zambiri, onerani vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?
Aroma 12:19: “Siyirani malo mkwiyo wa Mulungu. Chifukwa Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine,’ watero Yehova.” a
Yehova Mulungu sanapatse aliyense udindo wobwezera. Iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika pa nthawi yake. Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Zinthu Zopanda Chilungamo Zidzatha Padzikoli?”
a Yehova ndi dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?”