Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Thai Liang Lim/E+ via Getty Images

KHALANI MASO

Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Mwana Wanu?—Mmene Baibulo Lingathandizire Makolo

Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Mwana Wanu?—Mmene Baibulo Lingathandizire Makolo

 Achinyamata ambiri akusokonekera maganizo ndipo malo ochezera a pa intaneti ndi amene akuchititsa kwambiri zimenezi.”—Dr. Vivek Murthy, dokotala wamkulu wa maopaleshoni ku America, New York Times, June 17, 2024.

 Kodi makolo angateteze bwanji ana awo ku mavuto amene amabwera chifukwa chogwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti? Baibulo limapereka malangizo othandiza.

Zimene makolo angachite

 Ganizirani mfundo za m’Baibulo izi.

 “Wochenjera amaganizira zotsatira za zimene akufuna kuchita.”—Miyambo 14:15.

 Poganizira mavuto omwe amabwera chifukwa chogwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, musamakakamizike kulola mwana wanu kuti azigwiritsa ntchito malowa. Musafulumire kumulola kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, mpaka atakula ndithu moti akhoza kumatsatira malamulo omwe munamuikira okhudza kuchuluka kwa nthawi yomwe angamalowe pamalowa, kusankha bwino anthu ocheza nawo komanso kupewa zinthu zosayenera.

 “Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu”—Aefeso 5:16.

 Ngati mwalola mwana wanu kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, muzimuikira malamulo oti azitsatira ndipo muzimufotokozera mmene malamulowo angamutetezere. Muzichita chidwi ndi mmene mwanayo akuchitira zinthu. Ngati wayamba khalidwe lina lachilendo, zingasonyeze kuti akufunika kuti asamagwiritse ntchito kwambiri malo ochezera a pa intaneti.

Phunzirani Zambiri

 Baibulo limanena kuti tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1-5) Koma limaperekanso malangizo othandiza kwambiri. Nkhani zoposa 20 zomwe zili ndi malangizo ochokera m’Baibulo othandiza makolo ndi ana awo zingapezeke pa nkhani iyi yonena zokhudza kuvutika maganizo kwa achinyamata.