Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Mumaganiza Kuti Mudzapulumuka mwa Kulalikira Kunyumba ndi Nyumba?

Kodi Mumaganiza Kuti Mudzapulumuka mwa Kulalikira Kunyumba ndi Nyumba?

 Ayi. N’zoona kuti nthawi zambiri timalalikira kunyumba ndi nyumba koma sitimakhulupirira kuti tidzapulumuka chifukwa chochita zimenezi. (Aefeso 2:8) N’chifukwa chiyani tikutero?

 Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti munthu wina wachifundo walonjeza kuti adzapereka mphatso ya mtengo wapatali kwa munthu aliyense amene adzapezeke pamalo enaake pa tsiku limene munthuyo watchula. Ndiye inuyo mutakhala kuti mukukhulupirira kuti munthuyo adzachitadi zimene walonjeza, kodi mungapite kumaloko pa tsiku limene munthuyo wanena? N’zosakayikitsa kuti mungapiteko ndiponso mungauze anzanu komanso achibale anu za mwayiwo kuti nawonso akalandire nawo mphatsoyo. Simunganene kuti mwalandira mphatsoyo chifukwa chopita kumaloko pa tsiku limene ananenalo koma chifukwa chakuti munthuyo anafuna kukupatsani mphatsoyo.

 Mofanana ndi zimenezi, anthu a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lake loti adzapereka moyo wosatha kwa anthu onse amene amamumvera. (Aroma 6:23) Choncho timachita khama kuuza anthu ena zimene timakhulupirira n’cholinga choti nawonso adzalandire mphatso imene Mulungu walonjezayi. Koma sitimakhulupirira kuti tidzapulumuka chifukwa cholalikira. (Aroma 1:17; 3:28) Ndipotu palibe chinthu chilichonse chimene munthu angachite choti asinthanitse ndi mphatso ya moyo wosatha imene Mulungu adzatipatse. Iye anatipulumutsa chifukwa cha chifundo chake osati chifukwa cha zinthu zabwino zimene tinachita.—Tito 3:5.