Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani Yothetsa Banja?
Timatsatira kwambiri zimene Baibulo limanena pa nkhani ya ukwati komanso kuthetsa banja. Pamene Mulungu ankayambitsa ukwati, ankafuna kuti mwamuna ndi mkazi azikhala limodzi kwa moyo wawo wonse. Baibulo limanena kuti banja likhoza kutha pokhapokha ngati wina m’banjamo wachita chigololo.—Mateyu 19:5, 6, 9.
Kodi a Mboni amathandiza mabanja amene akukumana ndi mavuto?
Inde, ndipo amachita zimenezi pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana monga:
Mabuku. Nthawi zambiri mabuku athu amakhala ndi nkhani zimene zingathandize mabanja, ngakhale amene akuoneka ngati sangayambenso kuyenda bwino. Mwachitsanzo, onani nkhani yakuti “Khalanibe Okhulupirika Muukwati Wanu,” “Kodi Mungatani Kuti Muzikhululukirana,” komanso yakuti “Zimene Mungachite Kuti Muyambirenso Kukhulupirirana.”
Misonkhano. Kumisonkhano yathu ya mpingo, yadera komanso yachigawo, timaphunzira malangizo a m’Baibulo amene angathandize mabanja.
Akulu. Akulu amathandiza mabanja amene akukumana ndi mavuto ndipo amachita zimenezi pogwiritsa ntchito malemba monga Aefeso 5:22-25.
Kodi akulu ayenera kuvomereza ngati wa Mboni akufuna kuthetsa banja?
Ayi. Ngati banja limene likukumana ndi mavuto litapempha akulu kuti alithandize, akuluwo sakuyenera kusankhira zochita banjalo.(Agalatiya 6:5) Komabe, ngati munthu angathetse banja pa zifukwa zosagwirizana ndi zimene Baibulo limanena, sangakhale ndi mwayi wochita utumiki wapadera mu mpingo komanso alibe ufulu wokwatira kapena kukwatiwanso.—1 Timoteyo 3:1, 5, 12.
Kodi a Mboni amaiona bwanji nkhani yopatukana?
Baibulo limalimbikitsa anthu okwatirana kuti ayenera kukhalabe limodzi ngakhale pamene zinthu sizikuyenda bwino. (1 Akorinto 7:10-16) Mavuto ambiri akhoza kuthetsedwa popemphera mochokera pansi pa mtima, kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo komanso kusonyezana chikondi.—1 Akorinto 13:4-8; Agalatiya 5:22.
Komabe, Akhristu ena amasankha kupatukana ngati akukumana ndi mavuto aakulu kwambiri monga:
Kulephera kusamalira banja mwadala.—1 Timoteyo 5:8.
Nkhanza—Salimo 11:5.
Ngati moyo wauzimu uli pangozi. Mwachitsanzo, mwamuna kapena mkazi yemwe si wa Mboni angakakamize mnzake wa mu ukwati yemwe ndi wa Mboni kuti achite zina zake zosemphana ndi malamulo a Mulungu. Zikatero, amene akukakamizidwayo akhoza kusankha kuti apatukane ndi mnzakeyo chifukwa kuchita zimenezi ndi njira yokhayo imene ingamuthandize kuti ‘amvere Mulungu monga wolamulira, osati anthu.’—Machitidwe 5:29.