JULY 5, 2019
PORTUGAL
Zokhudza Msonkhano wa Mayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Lisbon, Portugal
Masiku: 28 mpaka 30 June, 2019
Malo: Sport Lisboa e Benfica Stadium ku Lisbon, Portugal
Zinenero: Chingelezi, Chipwitikizi (cha ku Portugal), Chinenero Chamanja cha ku Portugal, Chisipanishi
Chiwerengero cha Osonkhana: 63,390
Chiwerengero cha Obatizidwa: 451
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,300
Nthambi Zoitanidwa: Angola, Australia, Brazil, Canada, Central America, Ghana, India, Mozambique, Senegal, Spain, United States, Venezuela
Zina Zomwe Zinachitika: A Santos anali mmodzi mwa madalaivala omwe ankayendetsa mabasi omwe alendo opita kumsonkhanowu anakwera. M’bale amene ankayang’anira basiyo ataitanira a Santos kumsonkhano, iwo anati: “Ndikufuna kupita. Kungoyambira nthawi imene ndinayamba kugwira ntchito ndi inu, ndimakhala ndi mtendere umene sindingathe kuufotokoza. Sindikudziwa kuti mtendere umenewu umachokera kuti, koma mumandipangitsa kukhala ndi mtendere. Popeza kuti ndikakhala ku sitediyamuko tsiku lonse, ndikufuna kukapezeka pamsonkhanowo.” Atapanga nawo msonkhanowo, a Santos ananena kuti anasangalala kwambiri ndi msonkhanowo. Iwo amakhala m’mudzi winawake womwe uli kunja kwa mzinda wa Lisbon. Ali pamsonkhanopo, a Santos anakumana ndi m’bale wina yemwe amakhala m’mudzi woyandikana ndi wawo. Iwo anavomera kukakumana ndi m’baleyo onse akabwerera kumudzi kwawo.
Abale ndi alongo a ku Portugal akupereka moni kwa alendo omwe angofika kumene pabwalo la ndege
Alendo afika ku ofesi ya nthambi ya Portugal komwe akukaona malo
M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku loyamba la msonkhanowu
Abale ndi alongo akuimba nyimbo m’chinenero chamanja cha ku Portugal
Mmodzi mwa alongo athu akubatizidwa
Mtsikana wa ku Portugal akujambulitsa pomwe pali zithunzi za Kalebe ndi Sofiya
Alendo akuimba nyimbo yomaliza ya msonkhano
Alendo ochokera m’mayiko osiyanasiyana omwe ali muutumiki wanthawi zonse wapadera akubayibitsa anthu pamapeto pa msonkhano
Alendo akulalikira m’malo opezeka anthu ambiri limodzi ndi m’bale wa ku Portugal
Abale ndi alongo a ku Portugal akuvina gule wachikhalidwe posangalatsa alendo
Abale ndi alongo omwe amapanga zosangalatsa zosiyanasiyana madzulo akubayibitsa anthu