Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Chinenero China?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Chinenero China?

 Kuphunzira chinenero china kumafunika khama komanso kudzichepetsa. Kodi kuchita zimenezi kumathandizadi? Achinyamata ambiri angayankhe kuti inde. Nkhaniyi ifotokoza chifukwa chake iwo amachita zimenezi.

 N’chifukwa chiyani anthu ena amaphunzira chinenero china?

 Anthu ambiri amaphunzira chinenero china chifukwa ndi mbali ya maphunziro amene akuchita. Ena amaphunzira chifukwa amaona kuti kuchita zimenezi kuwathandiwa iwowo. Mwachitsanzo:

  •   Mtsikana wina wa ku Australia dzina lake Anna, anaganiza zophunzira Chilativiya chomwe ndi chinenero cha mayi ake. Iye anati: “Banja lathu likukonzekera kupita ku Latvia ndipo ndikufuna kuti ndizikatha kulankhulana ndi abale anga kumeneko.”

  •   Gina, yemwe ndi wa Mboni za Yehova ndipo amakhala ku United States, anaphunzira Chinenero Chamanja cha ku America n’kusamukira ku Belize n’cholinga choti awonjezere utumiki wake. Iye anafotokoza kuti: “Munthu yemwe ali ndi vuto losamva amakhala ndi anthu ochepa kwambiri omwe angathe kulankhula nawo. Anthu amene ali ndi vuto losamva amayamikira ndikawauza kuti ndinaphunzira Chinenero Chamanja cha ku America kuti ndiwathandize kuphunzira Baibulo m’chinenero chawo.”

 Kodi mukudziwa? Baibulo linaneneratu kuti uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu udzalalikidwa “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse.” (Chivumbulutso 14:6) Pokwaniritsa ulosi umenewu, achinyamata ambiri a Mboni za Yehova aphunzira chinenero china kuti awonjezere utumiki wawo m’dziko lawo kapena ku dziko lina.

 Kodi pamakhala mavuto otani?

 Kuphunzira chinenero china sikophweka. Mtsikana wina dzina lake Corrina ananena kuti: “Poyamba ndinkaganiza kuti kuphunzira chinenero china kumatanthauza kungophunzira mawu atsopano. Koma ndinapeza kuti kumaphatikizapo kuphunzira chikhalidwe chatsopano komanso kaganizidwe katsopano. Kunena zoona, kuphunzira chinenero china kumatenga nthawi.”

 Kuphunzira chinenero china kumafunanso kudzichepetsa. Mnyamata wina dzina lake James yemwe anaphunzira Chisipanishi anati: “Umafunika kuphunzira kudziseka wekha chifukwa umalakwitsa zinthu zambiri. Koma ndi mmene zimakhalira ukamaphunzira.”

 Mfundo yofunika kwambiri: Ngati mungakwanitse kulimbana ndi zinthu zomwe zingakubwezereni m’mbuyo, komanso kusachita manyazi mukalakwitsa nthawi zina, simungavutike kuphunzira chinenero china.

 Zimene zingakuthandizeni: Musamataye mtima ngati mukuona kuti anzanu akuphunzira mwamsanga kuposa inuyo. Baibulo limati: “Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”—Agalatiya 6:4.

 Kodi pamakhala mapindu otani?

 Pali mapindu ambiri amene amabwera chifukwa chophunzira chinenero china. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Olivia anati: “Ukaphunzira chinenero china, umatha kucheza ndi anthu ambiri a chinenerocho ndipo umapeza mabwenzi atsopano.”

 Mtsikana wina dzina lake Mary anaona kuti kuphunzira chinenero china kunamuthandiza kuti asamadzikayikire. Iye anati: “Zimandivuta kusangalala ndi chilichonse chimene ndikuchita, koma chifukwa choti tsopano ndikuphunzira chinenero china, ndimasangalala kwambiri ndikaphunzira mawu atsopano. Zimandithandiza kumva bwino.”

 Gina, yemwe tamutchula poyamba uja, waona kuti kuphunzitsa anthu Baibulo m’chinenero chamanja kwamuthandiza kuti azisangalala kwambiri akamachita utumiki wake. Iye ananena kuti: “Anthu amasangalala kwambiri ndikayamba kuyankhula nawo m’chinenero chawo ndipo ndaona kuti limeneli ndi dalitso lalikulu.”

 Mfundo yofunika kwambiri: Kuphunzira chinenero china kungakuthandizeni kuti musamadzikayikire, kuti mupeze mabwenzi atsopano, komanso kungakuchititseni kuti utumiki wanu uzikhala wothandizadi kwa ena. Imeneyi ndi njira yothandiza kwambiri yofikitsira uthenga wabwino “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.”—Chivumbulutso 7:9.