Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kuonerera Zinthu Zolaula?
Zimene mungachite
Zindikirani cholinga cha zinthu zolaula. Zinthu zolaula ndi njira imene Satana akugwiritsa ntchito pofuna kunyoza zinthu zimene Yehova analenga kuti zikhale zolemekezeka. Mukamvetsa kuti cholinga cha zithunzi zolaula n’chimenechi mungathe kuyamba ‘kudana n’choipa.’—Salimo 97:10.
Ganizirani zotsatira zake. Zithunzi zolaula zimachotsera ulemu anthu amene ajambulidwawo komanso munthu amene akuzionayo. N’chifukwa chaketu Baibulo limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.”—Miyambo 22:3.
Tsimikizani mtima. Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika, anenana kuti: “Ndachita pangano ndi maso anga. Choncho ndingayang’anitsitse bwanji namwali?” (Yobu 31:1) Nanunso mungathe kutsimikiza mtima kuchita zotsatirazi:
Sindidzagwiritsa ntchito Intaneti ndili pamalo a ndekha.
Ngati chithunzi cholaula chitatulukira mwadzidzidzi, ndizichitseka nthawi yomweyo.
Ngati nditayambiranso khalidweli, ndiziuza munthu wina wachikulire amene ndimagwirizana naye.
Pemphererani za nkhaniyi. Wamasalimo anapemphera kwa Yehova Mulungu kuti: “Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.” (Salimo 119:37) Mulungu amafuna kuti zinthu zizikuyenderani bwino, ndipo ngati mutapemphera iye akhoza kukupatsani mphamvu yokuthandizani kuti muchita zoyenera—Afilipi 4:13.
Uzaniko munthu wina. Nthawi zambiri, kuuza nkhaniyi munthu amene mumamudalira kumathandiza kwambiri kuti musiye khalidweli.—Miyambo 17:17.
Muzikumbukira mfundo iyi: Nthawi iliyonse mukapewa kuona zinthu zolaula, ndiye kuti mukupambana pa nkhondoyi. Nthawi iliyonse mukakwanitsa kupewa kuonerera zolaula, muzimuuza Yehova, ndiponso muzimuthokoza chifukwa chokupatsani mphamvu zimene zakuthandizani kupewa zimenezo. Mukapewa kuonerera zinthu zolaula, mumasangalatsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11