Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

N’chifukwa Chiyani Kuwerenga ndi Kofunika Kwambiri kwa Ana?​—Mbali Yoyamba: Kodi Zomwe Zingawathandize Ndi Zowerenga Kapena Zoonera?

N’chifukwa Chiyani Kuwerenga ndi Kofunika Kwambiri kwa Ana?​—Mbali Yoyamba: Kodi Zomwe Zingawathandize Ndi Zowerenga Kapena Zoonera?

 Kodi ana anu amakonda kuchita chiyani pa nthawi yopuma, kuonera mavidiyo kapena kuwerenga mabuku? Mukuganiza kuti angathamangire kutenga chiyani pakati foni ndi buku?

 Kwa zaka zambiri, anthu sakukondanso zowerenga chifukwa chosokonezedwa ndi TV kapena zinthu zina zomwe amaonera pa intaneti. Mayi wina dzina lake Jane Healy analemba m’buku lake la mu 1990 kuti: “M’kupita kwa nthawi anthu adzasiya kuwerenga.”​—Endangered Minds.

 Nthawi imeneyo zinkamveka zokokomeza, zinkaoneka kuti ndi zosatheka kuti anthu asiyiretu kuwerenga. Koma patatha zaka 30 chilembereni bukuli, aphunzitsi a m’mayiko amene luso lazopangapanga lapita patsogolo, aona kuti ana ambiri alibe chidwi chowerenga poyerekezera ndi mmene anthu ankachitira zaka zam’mbuyomu.

Zimene zili munkhaniyi

 Kodi kuwerenga kumawathandiza bwanji ana?

  •   Kuwerenga kumathandiza munthu kuyerekezera zinthu. Mwachitsanzo, ukamawerenga nkhani ina yake, umayerekezera mmene mawu a anthu otchulidwa munkhaniyo ankamvekera komanso maonekedwe awo. Umayerekezeranso mmene malo omwe kunkachitikira nkhaniyo ankaonekera. Wolemba nkhani amangofotokoza mfundo zochepa zokutsogolera, koma zimadalira wowerengayo kuganizira zonsezi.

     Mayi wina dzina lake Laura ananena kuti “Ukamaonera filimu kapena vidiyo ina yake, umaona mmene munthu wina ankaganizira zokhudza mmene nkhaniyo iyenera kukhalira. Zimasangalatsa inde, koma zimenezi ndi zosiyana ndi zomwe zimachitika ukamawerenga. Umaganizira wekha zomwe zikuchitika potengera zomwe ukumvazo.”

  •   Kuwerenga kumalimbikitsa mwana kukhala ndi makhalidwe abwino. Mwana akamawerenga nkhani, amakulitsa luso loganiza lomwe limamuthandiza kuthana ndi mavuto. Komanso, kuwerenga kumathandiza ana kuti azikhala tcheru. Kuchita zimenezi kumawathandiza kuti azikhala oleza mtima, odziletsa komanso kuti azichitira anthu ena chifundo.

     Mwina mukudabwa kuti kuwerenga kungathandize bwanji mwana kuchitira ena chifundo. Koma ochita kafukufuku anapeza kuti kuwerenga nkhani pang’onopang’ono kumathandiza mwana kuti aziganizira mmene anthu otchulidwa munkhaniyo ankamvera. Zimenezi zimathandiza mwana kuti azichitira chifundo anthu omwe amakumana nawo tsiku ndi tsiku.

  •   Kuwerenga kumathandiza kuti munthu aziganiza mozama. Munthu amene akufuna kumvetsa nkhani, sawerenga mothamanga. Nthawi zinanso amatha kuwerenga chiganizo chinachake kangapo kuti amvetse zimene wolemba nkhaniyo akutanthauza. Akamachita zimenezi m’pamene amakwanitsa kukumbukira zomwe wawerenga komanso kupindula ndi nkhaniyo.​—1 Timoteyo 4:15.

     Bambo wina dzina lake Joseph ananena kuti: “Ukamawerenga, umatha kumva tanthauzo la chiganizo, kuyerekezera ndi zomwe ukudziwa kale, komanso kuganizira zomwe ukuphunzirapo. Pomwe mafilimu ndi mavidiyo sathandiza munthu kuchita zimenezi.”

 Mfundo yofunika kukumbukira: Ngakhale kuti zinthu ngati mafilimu ndi mavidiyo ndi zothandiza, koma ana anu sangadziwe zinthu zambiri ngati sapeza nthawi yowerenga.

 Mmene mungalimbikitsire mwana wanu kuti azikonda kuwerenga

  •   Muyambitseni adakali wamng’ono. Mayi wina yemwe ali ndi ana awiri dzina lake Chloe ananena kuti: “Tinayamba kuwerengera ana anthu nkhani zosiyanasiyana ndili woyembekezera ndipo tinapitiriza kuwawerengera atabadwa. Timaona kuti tinachita bwino kwambiri. Patapita nthawi, kuwerenga kunangokhala mbali ya moyo wawo.”

     Mfundo ya m’Baibulo: “Kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba oyera.”​—2 Timoteyo 3:15.

  •   Onetsetsani ku pakhomo panu pali zonse zofunika kuti ana anu aziwerenga. Muzikhala ndi mabuku oti ana anu azitha kuwawerenga nthawi iliyonse. Mayi wina wa ana 4 dzina lake Tamara ananena kuti: “Ndi bwino kupeza mabuku omwe ali ndi nkhani zomwe mwana wanu angasangalale nazo ndipo muziika mabukuwo pafupi ndi bedi lake.”

     Mfundo ya m’Baibulo: “Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”​—Miyambo 22:6.

  •   Chepetsani nthawi yogwiritsa ntchito intaneti. Bambo wina dzina lake Daniel ananena kuti ndi bwino kuti makolo azikhazikitsa nthawi yoti aliyense m’banjamo asagwiritse ntchito TV, foni kapenanso kompyuta. Iye ananena kuti: “Nthawi zina tinkakonza zoti aliyense asaonere TV, mwina madzulo a tsiku limodzi pa wiki inayake. Nthawi imeneyo inkakhala yowerenga, kaya tonse ngati banja kapena aliyense payekhapayekha.”

     Mfundo ya m’Baibulo: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—Afilipi 1:10.

  •   Muziwapatsa chitsanzo. Mayi wina wa ana awiri dzina lake Karina analimbikitsa makolo ena kuti: “Muziwerengera ana anu nkhani m’njira yoti azisangalala nayo. Muzisonyeza kuti mukusangalala ndi zomwe mukuwerengazo. Mukamakonda kuwerenga, ana anu adzatengeranso zomwezo.”

     Mfundo ya m’Baibulo: “Pitiriza kukhala wodzipereka powerenga pamaso pa anthu.”​—1 Timoteyo 4:13.

 Ndi zoona kuti si ana onse omwe adzakhale okonda zowerenga. Komabe zimene mungachite zingawathandize kuti akhale ndi mtima wokonda kuwerenga. Bambo wina wa ana awiri dzina lake David anafotokoza zomwe ankachita kuti: “Ndinkawerenga mabuku omwe ana anga ankakonda kuwerenga. Zimenezi zinkandithandiza kuti ndizidziwa zinthu zomwe amakonda komanso kuti tisamasowe nkhani zoti n’kukambirana. Tinkangokhala ngati tili ndi kagulu kokambirana zomwe tawerenga ndipo zinali zosangalatsa kwambiri.”