Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?

N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?

Zimene Baibulo limanena

 Yesu anafa n’cholinga choti anthu akhululukidwe machimo awo komanso kuti adzakhale ndi moyo wosatha. (Aroma 6:23; Aefeso 1:7) Imfa ya Yesu inasonyezanso kuti munthu akhoza kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale pamene akukumana ndi mayesero aakulu.—Aheberi 4:15.

 Taonani mmene imfa ya munthu mmodzi inathandizira kuti zinthu zosiyanasiyana zitheke.

  1.   Yesu anafa ‘kuti machimo athu akhululukidwe.’—Akolose 1:14.

     Adamu, yemwe anali munthu woyamba kulengedwa, anali wangwiro kapena kuti wopanda uchimo. Komabe, iye anasankha kusamvera Mulungu. Kusamvera kwake, kapena kuti kuchimwa kwake, kunakhudza kwambiri ana ake onse. Baibulo limati: “Mwa kusamvera kwa munthu mmodziyo, ambiri anakhala ochimwa.”—Aroma 5:19.

     Nayenso Yesu anali wangwiro, koma sanachimwepo. Choncho iye anali woyenera kukhala “nsembe yophimba machimo athu.” (1 Yohane 2:2) Monga mmene uchimo wa Adamu unapangitsira kuti anthu onse akhale ochimwa, imfa ya Yesu inachititsa kuti anthu onse amene angakhulupirire mwa iye akhale opanda uchimo.

     Tinganene kuti Adamu anagulitsa mtundu wonse wa anthu ku uchimo. Popereka moyo wake m’malo mwa anthu onse, Yesu anagulanso mtundu wa anthu kuti akhale ake. Chifukwa cha zimenezi, Baibulo limati: “wina akachita tchimo, tili ndi mthandizi wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.”—1 Yohane 2:1.

  2.   Yesu anafa “kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha”—Yohane 3:16.

     Adamu analengedwa m’njira yoti akhale ndi moyo mpaka kalekale, koma anafa chifukwa cha tchimo lake. Kudzera mwa Adamu ‘uchimo unalowa m’dziko ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’—Aroma 5:12.

     Mosiyana ndi zimenezi, imfa ya Yesu inapangitsa kuti anthu onse amene angakhulupirire iye asakhalenso ochimwa komanso kuti chilango cha imfa chichotsedwe. Baibulo limafotokoza bwino zimenezi ndipo limati: ‘Monga mmene uchimo unalamulira monga mfumu pamodzi ndi imfa, momwemonso kukoma mtima kwakukulu kulamulire monga mfumu kudzera m’chilungamo. Zimenezi zichitike kuti moyo wosatha ubwere kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.’—Aroma 5:21.

     Panopa anthu amakhala ndi moyo kwa zaka zochepa. Komabe, Mulungu walonjeza kuti adzapereka moyo wosatha kwa anthu olungama komanso kuukitsa akufa kuti nawonso adzapindule ndi nsembe imene Yesu anapereka.—Salimo 37:29; 1 Akorinto 15:22.

  3.   Yesu ‘anakhala womvera mpaka imfa,’ ndipo umenewu ndi umboni woti munthu akhoza kukhala wokhulupirika kwa Mulungu pamene akukumana ndi mayesero.—Afilipi 2:8.

     Ngakhale kuti maganizo komanso thupi la Adamu linali zangwiro, iye sanamvere Mulungu chifukwa chosirira mwadyera chinthu chimene sichinali chake. (Genesis 2:16, 17; 3:6) Kenako Satana, yemwe ndi mdani wamkulu wa Mulungu, ananena kuti palibe munthu amene angamvere Mulungu popanda zifukwa za dyera makamaka ngati moyo wake uli pangozi. (Yobu 2:4) Komabe, Yesu yemwe anali munthu wangwiro, anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu mpaka pamene anafa imfa yowawa komanso yochititsa manyazi. (Aheberi 7:26) Zimene Yesu anachitazi zinapereka yankho ku bodza limene Satana ananena. Munthu akhoza kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale atakumana ndi mayesero a mtundu uliwonse.

Mafunso okhudza imfa ya Yesu

  •   N’chifukwa chiyani Yesu anayenera kuzunzidwa komanso kufa n’cholinga choti awombole anthu? N’chifukwa chiyani Mulungu sanangothetsa chilango cha imfa?

     Lamulo la Mulungu limanena kuti: “Malipiro a uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Mulungu sanamubisile Adamu lamulo limeneli koma anamuuza momveka bwino kuti chilango cha kusamvera ndi imfa. (Genesis 3:3) Adamu atachimwa, Mulungu, “amene sanganame,” anachitadi zimene anamuuza Adamu. (Tito 1:2) Adamu anapatsira ana ake uchimo komanso malipiro a uchimowo, omwe ndi imfa.

     Ngakhale kuti anthu ochimwa ndi oyenera kulandira chilango cha imfa, Mulungu anawapatsa “chuma cha kukoma mtima kwake kwakukulu.” (Aefeso 1:7) Zimene Mulungu anachita potumiza Yesu monga nsembe yangwiro n’cholinga chowombola anthu, zinasonyeza chilungamo komanso chifundo chachikulu chimene ali nacho.

  •   Kodi Yesu anafa liti?

     Yesu anafa pa “ola la 9” kuwerengera kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa, kapena cha m’ma 3 koloko masana patsiku la Pasika wa Ayuda. (Maliko 15:33-37, mawu a mmunsi) Pa makalenda a masiku ano, deti limenelo limafanana ndi tsiku Lachisanu, pa 1 April, 33 CE.

  •   Kodi Yesu anafera kuti?

     Yesu anaphedwera “kumalo otchedwa Chibade, koma pa Chiheberi amatchedwa, Gologota” (Yohane 19:17, 18) M’nthawi ya Yesu, malowa anali “kunja kwa chipata” cha mzinda wa Yerusalemu. (Aheberi 13:12) Malowa ayenera kuti anali pa phiri, chifukwa Baibulo limanena kuti pamene Yesu ankaphedwa, anthu ena ankaonerera ali “chapatali ndithu.” (Maliko 15:40) Komabe, masiku ano ndi zovuta kudziwa malo enieni amene panali Gologota.

  •   Kodi Yesu anafa bwanji?

     Ngakhale kuti anthu ambiri amakhulupirira kuti Yesu anapachikidwa pamtanda, Baibulo limanena kuti: “Iye ananyamula machimo athu m’thupi lake pamtengo.” (1 Petulo 2:24) Olemba Baibulo anagwiritsira ntchito mawu awiri a Chigiriki pofotokoza chinthu chimene Yesu anaphedwerapo. Mawuwa ndi stau·rosʹ komanso xyʹlon. Akatswiri amanena kuti mawu amenewa amatanthauza mtengo umodzi woongoka.

  •   Kodi imfa ya Yesu iyenera kukumbukiridwa motani?

     Usiku wa tsiku limene Ayuda ankapanga mwambo wa pachaka wa Pasika, Yesu anayambitsa mwambo wosavuta ndi ophunzira ake ndipo anawalamula kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (1 Akorinto 11:24) Kenako Yesu anaphedwa patangodutsa maola ochepa.

     Olemba Baibulo anayerekezera Yesu ndi mwanawankhosa amene ankaperekedwa nsembe pamwambo wa Pasika. (1 Akorinto 5:7) Chikondwerero cha Pasika chinkakumbutsa Aisiraeli kuti anamasulidwa ku ukapolo. Nawonso mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu Khristu umakumbutsa Akhristu kuti anamasulidwa ku uchimo ndi imfa. Mwambo wa Pasika unkachitika kamodzi pachaka, pa Nisani 14 malinga ndi kalenda yotsatira tsiku limene mwezi waoneka. Mofanana ndi zimenezi, Akhristu oyambirira ankachitanso Chikumbutso kamodzi pachaka.

     Patsiku lofanana ndi Nisani 14, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse amakumbukira imfa ya Yesu.