Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Mulungu Analemberatu Nthawi Yomwe Munthu Adzamwalire?

Kodi Mulungu Analemberatu Nthawi Yomwe Munthu Adzamwalire?

Yankho la m’Baibulo

 Ayi. Baibulo silisonyeza kuti Mulungu analemberatu nthawi imene munthu adzamwalire koma limanena kuti nthawi zambiri anthufe timafa chifukwa cha “zinthu zosayembekezereka.”​—Mlaliki 9:11.

Si paja Baibulo limati “pali nthawi ya kufa”?

 Inde. Lemba la Mlaliki 3:2 limati pali “nthawi yobadwa ndi nthawi ya kufa. Nthawi yobzala ndi nthawi yozula chimene chinabzalidwa.” Koma lembali likusonyeza zimene zimachitika pa moyo wa munthu, chifukwa munthu amabadwa kenako amamwalira. (Mlaliki 3:1-8) Apa lembali likusonyeza kuti Mulungu sanalemberetu nthawi yoti munthu adzamwalire ngati mmene mlimi sangakakamizire mbewu kumera. Koma mfundo yake ndi yakuti tiyenera kupewa kutanganidwa ndi zinthu zosafunika kwenikweni mpaka kufika poiwala Mlengi.​—Mlaliki 3:11; 12:1, 13.

N’zotheka kukhala ndi moyo wotalikirapo

 Ngakhale kuti moyo wathu ndi wosadalirika, n’zotheka kukhala ndi moyo wotalikirapo ngati titamasankha zinthu mwanzeru. Baibulo limanena kuti: “Lamulo la munthu wanzeru ndilo kasupe wa moyo, chifukwa limapulumutsa munthu kumisampha ya imfa.” (Miyambo 13:14) Nayenso Mose anauza Aisiraeli kuti ngati angamvere malamulo a Yehova, ‘masiku amoyo wawo adzatalika.’ (Deuteronomo 6:2) Mosiyana ndi zimenezi, tikhoza kufupikitsa moyo wathu ngati tingamachite zinthu mosaganiza bwino.​—Mlaliki 7:17.

 Ngakhale titamachita zinthu mwanzeru bwanji, n’zosatheka kuthawa imfa. (Aroma 5:12) Komabe zinthu zidzasintha, chifukwa Baibulo limalonjeza kuti “imfa sidzakhalaponso.”​—Chivumbulutso 21:4.