Kodi Wokana Khristu Amachita Zotani?
Yankho la m’Baibulo
Wokana Khristu sikuti nthawi zonse amangokhala munthu mmodzi kapena gulu limodzi la anthu basi. Tikutero chifukwa Baibulo limanena kuti pali “okana Khristu ambiri.” (1 Yohane 2:18) Mawu akuti “wokana Khristu,” anatengedwa kumawu achigiriki omwe amatanthauza “wotsutsana ndi Khristu.” Choncho mawuwa amatanthauza aliyense amene amachita zotsatirazi:
Amatsutsa zoti Yesu ndi Khristu (Mesiya) kapena zoti ndi mwana wa Mulungu.—1 Yohane 2:22.
Amatsutsa Khristu, yemwe anadzozedwa ndi Mulungu.—Salimo 2:1, 2; Luka 11:23.
Amanena kuti ndi Khristu.—Mateyu 24:24.
Amazunza otsatira a Khristu. Yesu amaona kuti zimene anthu amachitira otsatira ake zimakhala ngati akuchitira iyeyo.—Machitidwe 9:5.
Amati ndi Mkhristu koma amachita zinthu zachinyengo komanso samvera malamulo.—Mateyu 7:22, 23; 2 Akorinto 11:13.
Ngakhale kuti Baibulo limati anthu amene amachita zimenezi ndi okana Khristu, limagwiritsanso ntchito mawu akuti “wokana Khristu” ponena za anthu onse pamodzi amene amachita zimenezi. (2 Yohane 7) Wokana Khristu anayamba kupezeka nthawi ya atumwi. Masiku ano kulinso wokana Khristu ndipo Baibulo linalosera zimenezi kalekale.—1 Yohane 4:3.
Mmene tingadziwire okana Khristu
Amalimbikitsa mfundo zabodza zokhudza Yesu. (Mateyu 24:9, 11) Mwachitsanzo, anthu amene amaphunzitsa za Utatu kapena zoti Yesu ndi Mulungu Wamphamvu Yonse, amakhala akutsutsa zimene Yesu anaphunzitsa. Iye anati: “Atate ndi wamkulu kuposa ine.”—Yohane 14:28.
Anthu okana Khristu amakana zimene Yesu ananena pa nkhani ya mmene Ufumu wa Mulungu umagwirira ntchito. Mwachitsanzo, atsogoleri achipembedzo ena amanena kuti Khristu amalamulira pogwiritsa ntchito maboma amene alipo masiku ano. Koma izi n’zosemphana ndi zimene Yesu ananena. Iye anati: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.”—Yohane 18:36.
Amati Yesu ndi Ambuye wawo, koma samvera malamulo ake. Mwachitsanzo, samvera lamulo lake loti tizilalikira uthenga wabwino wa Ufumu.—Mateyu 28:19, 20; Luka 6:46; Machitidwe 10:42.