Kodi Yesu Amatipulumutsa Bwanji?
Yankho la m’Baibulo
Yesu atapereka moyo wake ngati nsembe ya dipo, anathandiza kuti anthu okhulupirika apulumuke. (Mateyu 20:28) N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Yesu ndi “Mpulumutsi wa dziko.” (1 Yohane 4:14) Limanenanso kuti: “Chipulumutso sichipezeka mwa munthu wina aliyense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo, limene laperekedwa kwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”—Machitidwe 4:12.
Yesu ‘analawa imfa m’malo mwa munthu aliyense’ amene angasonyeze chikhulupiriro mwa iye. (Aheberi 2:9; Yohane 3:16) Kenako “Mulungu anamuukitsa kwa akufa” ndipo anabwerera kumwamba komwe anakakhalanso ndi moyo wauzimu. (Machitidwe 3:15) Panopo Yesu amatha “kupulumutsa kwathunthu anthu amene akufika kwa Mulungu kudzera mwa iye, chifukwa adzakhalabe ndi moyo nthawi zonse ndipo aziwachonderera kwa Mulungu.”—Aheberi 7:25.
N’chifukwa chiyani Yesu amafunika kuchonderera m’malo mwathu?
Anthu tonse ndife ochimwa. (Aroma 3:23) Uchimo uli ngati chotchinga pakati pa anthufe ndi Mulungu ndipo timafa chifukwa chakuti ndife ochimwa. (Aroma 6:23) Koma Yesu ndi “mthandizi” wa onse amene amakhulupirira nsembe ya dipo yomwe anapereka. (1 Yohane 2:1) Yesu amathandiza anthu powachonderera kwa Mulungu kuti amve mapemphero awo. Ndipo Mulungu amakhululukira anthuwo chifukwa cha nsembe ya Yesu. (Mateyu 1:21; Aroma 8:34) Yesu akamachonderera, Mulungu amamva chifukwa amaona kuti zopemphazo ndi zogwirizana ndi chifuniro chake. Mulungu anatumiza mwana wake padzikoli “kuti mwa iye, dziko lipulumutsidwe.”—Yohane 3:17.
Kodi kungokhulupirira Yesu n’kokwanira kuti tidzapulumuke?
Ayi. Pali zambiri zomwe zimafunika kuti tidzapulumuke osati kungokhulupirira Yesu kokha. (Machitidwe 16:30, 31) Baibulo limati: “Monga mmene thupi lopanda mzimu limakhalira lakufa, nachonso chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.” (Yakobo 2:26) Kuti tidzapulumuke tiyenera:
Kuphunzira za Yesu ndi Atate wake yemwe ndi Yehova.—Yohane 17:3.
Kusonyeza kuti timakhulupirira Yesu komanso Yehova —Yohane 12:44; 14:1
Kusonyeza chikhulupiriro chathu pomvera malamulo omwe amatipatsa. (Luka 6:46; 1 Yohane 2:17) Yesu anaphunzitsa kuti si aliyense amene adzamutchule kuti “Ambuye” amene adzapulumuke. Koma okhawo amene “akuchita chifuniro cha Atate [wake] wakumwamba.”—Mateyu 7:21.
Kupitiriza kusonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro ngakhale kuti timakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Yesu anasonyeza kuti zimenezi ndi zofunika kwambiri pamene ananena kuti: “Amene adzapirire mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.”—Mateyu 24:13.