Zokhudza Malamulo
Eni Ake
© 2014 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Inc. All rights reserved.
Webusaiti ino inapangidwa ndi bungwe la Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc. (“Watchtower”). Nkhani komanso zinthu zonse zimene zili pawebusaitiyi ndi za bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Inc. kupatulapo ngati tasonyeza kuti zachokera kwina.
Zizindikiro
Zizindikiro za Adobe komanso Acrobat ndi za bungwe la Adobe Systems Incorporated. Ndipo zizindikiro za iTunes komanso iPod ndi za bungwe la Apple Inc. Zizindikiro zina zonse ndi za mabungwe amene asonyezedwawo.
Zoyenera Kutsatira Pogwiritsa Ntchito Webusaitiyi
Mfundo zimene zafotokozedwa m’munsimu ndi zimene muyenera kutsatira pogwiritsa ntchito webusaitiyi. Mukamagwiritsa ntchito webusaitiyi ndiye kuti mwavomereza kutsatira mfundo zonse zomwe zafotokozedwazo. Koma ngati simukugwirizana ndi mfundo zonse kapena zina mwa mfundozi, musagwiritse ntchito webusaitiyi.
Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite pawebusaitiyi? Mukhoza kuwerenga, kuonera, kupanga dawunilodi komanso kusindikiza nkhani, mabuku, nyimbo, zithunzi ndi mavidiyo kuti muzigwiritsa ntchito inuyo osati kuti mugulitse. Koma simukuyenera kuchita zinthu zimene zafotokozedwa m’munsizi komanso zinthu zilizonse zosemphana ndi malamulo a mmene mungagwiritsire ntchito webusaitiyi. Zinthu zimene simukuyenera kuchita ndi:
Kutenga zinthu za pawebusaitiyi n’kuika pa intaneti (kapena pawebusaiti ina, ngakhalenso pamalo ochezera pa Intaneti);
Kufalitsanso zinthu za pawebusaitiyi pogwiritsa ntchito mapulogalamu ena kapena kugwiritsa ntchito zinthu za pawebusaitiyi ngati mbali ya mapulogalamu ena a pakompyuta;
Kupanganso, kukopera, kapena kuchotsa zinthu zina za pawebusaitiyi n’cholinga chopanga malonda (ngakhale kuti simupeza phindu pa malondawo), kuphatikizapo kugawa mapulogalamu a pakompyuta amene aikidwa, kulumikizidwa kapena kupangidwa linki (kaya otheka kusinthidwa kapena osatheka kusinthidwa) pa webusaitiyi;
Kutsegula webusaitiyi n’cholinga chopanga ndi kufalitsa zinthu zokhudza mmene webusaitiyi inapangidwira, zogwiritsira ntchito pokonza webusaitiyi ndiponso pofuna kutenga mosayenera zinthu zina (zomwe zikuphatikizapo kutenga zinthu zambiri pofuna kuzifalitsa ndi dzina lanu, komanso kuchita zilizonse mosayenera) zomwe zili pawebusaitiyi;
Kugwiritsira ntchito molakwika webusaitiyi kapena zimene zaikidwapo, monga kutsegula webusaitiyi komanso kugwiritsa ntchito zimene zaikidwapo mosemphana ndi njira yovomerezeka yogwiritsira ntchito zinthuzo;
Kugwiritsira ntchito webusaitiyi m’njira imene ingayambitse mavuto kapena kulepheretsa anthu kulowa pawebusaitiyi; kapena kuigwiritsa ntchito m’njira iliyonse yosemphana ndi malamulo, yachinyengo, ndiponso yosayenera. Simukuyeneranso kugwiritsa ntchito webusaitiyi pofuna kuchita zinthu zosemphana ndi malamulo, zachinyengo ndiponso zosayenera;
Kugwiritsa ntchito webusaitiyi ndi cholinga chilichonse chokhudzana ndi zamalonda.
Chilango Chomwe Mungalandire
Bungwe la Watchtower lili ndi ufulu wochita zinthu zina zimene inuyo mwaletsedwa kuchita pawebusaitiyi. Koma ngati inuyo mwaphwanya mfundo zomwe zafotokozedwazi mwa njira iliyonse, bungwe la Watchtower ngati litaona kuti ndi koyenera likhoza kukupatsani chilango monga kukusiyitsani kaye kulowa pawebusaitiyi, kukuletsani kugwiritsa ntchito webusaitiyi, kupangitsa kuti makompyuta onse amene mumagwiritsirapo ntchito adiresi yanu ya IP asamathe kutsegula webusaitiyi, kuuza eni a kampani ya intaneti imene mumagwiritsa ntchito kuti akutsekeni n’cholinga choti musamathe kutsegula webusaitiyi. Ndipo ngati n’koyenera bungweli likhozanso kukutengerani kukhoti.
Kusintha Zoyenera Kutsatira
Bungwe la Watchtower likhoza kumasintha Zoyenera Kutsatira pa nkhani yogwiritsa ntchito webusaitiyi. Mfundo zatsopano Zoyenera Kutsatira zidzayamba kugwira ntchito zikangoikidwa pawebusaitiyi. Tikukupemphani kuti muziona tsamba la Zoyenera Kutsatira kawirikawiri n’cholinga choti muzidziwa zimene zasintha.
Khoti Lozenga Mlandu
Mukalephera kutsatira Mfundo Zoyenera Kutsatirazi ndipo ngati pakufunika kukutengerani kukhoti, mlanduwo udzazengedwa motsatira malamulo a State of New York, U.S.A., ngakhale malamulowa atakhala osiyana ndi a m’dziko lanu. Komanso mlandu udzazengedwera kukhoti la ku State of New York, U.S.A.
Ngati Mfundo Ina Siikufunika Kutsatiridwa
Ngati khoti lanena kuti mfundo imodzi pa mfundo zoyenera kutsatira pogwiritsa ntchito webusaitiyi, sikugwira ntchito, ndi yoti munthu sangaimbidwe nayo mlandu ataiphwanya kapena ndi yosemphana ndi malamulo, mfundo zina zonse zipitiriza kugwira ntchito ndipo muyenera kuzitsatira. Munthu ataphwanya mfundo ina ndipo bungwe la Watchtower lasankha kuti lisamuimbe mlandu kapena kumutengera kukhoti, sizikutanthauza kuti mfundoyo yasiya kugwira ntchito kapenanso kuti bungweli lilibe ufulu woimba mlandu munthuyo.
Mgwirizano
Mfundo Zoyenera Kutsatira zomwe zafotokozedwazi ndi mgwirizano wa inuyo ndi bungwe la Watchtower pa nkhani ya mmene mungagwiritsire ntchito webusaitiyi, ndipo zikulowa m’malo mwa mgwirizano umene munapanga m’mbuyomu ndi bungweli pa nkhani yogwiritsa ntchito webusaitiyi.