Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi ningacite ciani kuti nikhale paubwenzi na Mulungu?

Kodi ningacite ciani kuti nikhale paubwenzi na Mulungu?

MUTU 35

Kodi ningacite ciani kuti nikhale paubwenzi na Mulungu?

Jeremy anazindikila kufunika kokhala paubwenzi na Mulungu cifukwa ca mavuto amene anakumana nawo. Iye anati: “Pamene n’nali na zaka 12, bambo anga anacoka n’kutisiya na mayi. Tsiku lina usiku, n’nayamba kupemphela kwa Yehova kuti bambo angawo abwelele.”

Jeremy atathedwa nzelu, anayamba kuŵelenga Baibo, ndipo anakhudzidwa mtima kwambili ataŵelenga Salmo 10:14. Ponena za Yehova, vesiyi imati: “Waumphawi adzipeleka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.” Jeremy anati: “N’namva ngati Yehova akulankhula nane, kuniuza kuti iye ndiye mthandizi wanga; ndiye Bambo wanga. Ndipo palibe munthu wina aliyense amene angakhale bambo wabwino kwambili kuposa Yehova.”

KAYA mukukumana na mavuto ngati a Jeremy kapena ayi, Baibo imasonyeza kuti Yehova amafuna kuti mukhale naye paubwenzi. Ndipo imanena kuti: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yakobe 4:8) Taganizilani tanthauzo la mawu amenewa: Ngakhale kuti Yehova Mulungu simungamuone, ndipo simungafanane naye ngakhale pang’ono, iye akukupemphani kuti mukhale naye paubwenzi.

Koma pamafunika khama ndithu kuti mukhale paubwenzi na Mulungu. Tiyelekezele kuti mwabyala duwa lam’nyumba. Kodi lingakule lokha popanda kulisamalila? Kuti duwalo likule bwino, mungafunike kulithilila nthawi zonse ndiponso kuliika pamalo abwino. N’cimodzi-modzinso na kukhala paubwenzi na Mulungu. Kodi mungacite ciani kuti mukhale paubwenzi wolimba?

Kuphunzila Baibo N’kofunika

Anthu ogwilizana amafunika kulankhulana ndiponso kumvetselana. N’zimenenso zimafunika munthu akakhala paubwenzi na Mulungu. Tikamaŵelenga ndiponso kuphunzila Baibo timakhala tikumvetsela zimene Mulungu akutiuza.—Salmo 1:2, 3.

Mwina imwe simukonda kuŵelenga. Acinyamata ambili amaona kuti ni bwino kuonela TV, kucita masewela ena ake kapena kuceza ni anzawo m’malo moŵelenga. Koma ngati mukufuna kukhala paubwenzi na Mulungu, muyenela kucita zonse zimene iye akufuna kuti mutsatile. Mufunika kumvetsela zimene iye akunena mwa kuphunzila Mawu ake.

Komabe, musade nkhawa. Kuŵelenga Baibo si nchito yolemetsa. Ngakhale kuti mwacibadwa mwina simukonda kuŵelenga, n’zotheka kuti muzisangalala mukamaŵelenga Baibo. Cinthu coyamba cimene muyenela kucita ndico kupatula nthawi yoti muziŵelenga Baibo. Mtsikana wina dzina lake Lais anati: “Nili na ndandanda ya zinthu zimene niyenela kucita. Nimaŵelenga Baibo caputala imodzi m’mawa uliwonse nikangouka.” Maria, yemwe ali na zaka 15, nayenso ali na ndandanda yake. Iye anati: “Nimaŵelenga Baibo pang’ono madzulo aliwonse nisanagone.”

Kuti mukhale na ndandanda yanu yophunzilila Baibo, onani  bokosi imene ili patsamba 292. Ndiyeno, lembani m’munsimu nthawi imene mukuona kuti mungamaphunzile Mawu a Mulungu kwa mphindi pafupifupi 30 kapena kuposelapo.

․․․․․

Kukonza ndandanda ni ciyambi cabe. Mukayamba kuphunzila Baibo, mwina mudzaona kuti nkhani zake zina ni zovuta kuŵelenga. N’kutheka kuti mungagwilizane na zimene ananena mnyamata wina wazaka 11, dzina lake Jezreel. Iye anati, “Nkhani zina za m’Baibo n’zovuta kuzimvetsa ndipo n’zosasangalatsa kwenikweni.” Ngakhale mutakhala na maganizo otelowo, musasiye kuŵelenga Baibo. Nthawi zonse muziona kuti kuphunzila Baibo ni njila imene bwenzi lanu, Yehova Mulungu akukulankhulilani. Mukamacita khama kwambili, m’pamene mudzaone kuti kuphunzila Baibo n’kosangalatsa komanso kopindulitsa kwambili.

Pemphelo N’lofunika

Pemphelo ni mphatso yamtengo wapatali kwambili cifukwa ni njila imene timalankhulila na Mulungu. Mungalankhule na Yehova Mulungu nthawi iliyonse, kaya masana kapena usiku. Iye ni wokonzeka kukumvetselani nthawi zonse. Komanso amafunitsitsa kumva zimene mukufuna kunena. N’cifukwa cake Baibo imakulimbikitsani kuti: “Pa ciliconse, mwa pemphelo na pembedzelo, limodzi ni ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6.

Mogwilizana na lembali, pali zinthu zambili zimene mungafune kuuza Yehova. Zina mwa zinthu zimenezi ni mavuto amene mukukumana nawo. Mungamuuzenso zinthu zina zimene mumayamikila. Mwacibadwa, anzanu akakucitilani zabwino mumawayamikila. Conco, mungacitenso zomwezo kwa Yehova, yemwe wakucitilani zinthu zambili kuposa mnzanu wina aliyense.—Salmo 106:1.

Lembani pa mizele iyi zina mwa zinthu zimene zimakucititsani kuyamikila Yehova.

․․․․․

N’zodziŵikilatu kuti pali zinthu zosiyana-siyana zimene zimakudetsani nkhawa. Lemba la Salmo 55:22 limati: “Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiliziza: Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”

Lembani pa mizele yotsatilayi zinthu zimene zikukudetsani nkhawa zomwe mukufuna kumazichula m’pemphelo.

․․․․․

Zocitika pa Moyo Wanu

Kuti mukhale paubwenzi na Mulungu pali cinthu cinanso cimene simuyenela kucinyalanyaza. Wamasalmo Davide analemba kuti: “Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino.” (Salmo 34:8) Pamene Davide anali kulemba Salmo 34 anali atangokumana na mavuto aakulu kwambili. Panthawi imeneyo amathawa Mfumu yoipa Sauli, ndipo n’zodziŵikilatu kuti zimenezi zinali zosokoneza maganizo kwambili. Koma iye anali kubisala pakati pa Afilisti omwe anali adani ake. Poopa kuphedwa, Davide ananamizila kuti anali wamisala ndipo anapulumuka.—1 Samueli 21:10-15.

Apatu Davide anapulumukila mkamwa mwa mbuzi. Komabe, sanadzitame kuti anapulumuka cifukwa ca nzelu zake. M’malo mwake, iye anatamanda Yehova kuti ni amene anam’thandiza. Cakumayambililo kwa Salmo 34, iye analemba kuti: “Ndinafuna Yehova ndipo anandivomela, nandilanditsa m’mantha anga onse.” (Salmo 34:4) Conco, kucokela pa zimene zinam’citikila pamoyo wake, Davide anatha kulimbikitsa anthu ena kuti, “Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino.”

Kodi mungachule cinacake cimene cinakucitikilanipo cosonyeza kuti Yehova amakukondani? Ngati cilipo, cilembeni m’munsimu. Kumbukilani izi: M’posafunika kuti cinthuco cicite kukhala cozizwitsa. Ganizilani zinthu zabwino, ngakhale zooneka ngati zing’ono-zing’ono, zimene zimacitika pamoyo wanu.

․․․․․

Mwina makolo anu anakuphunzitsani Baibo. Ngati ni conco, amenewo ni madalitso. Komabe, imwe pamwekha muyenela kucita khama kuti mukhale paubwenzi na Mulungu. Ngati panopa simunakhalebe paubwenzi na Mulungu, mungathe kugwilitsa nchito mfundo za m’nkhani ino kuti zikuthandizeni kucita zimenezo. Yehova adzadalitsa khama lanu. Baibo imati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; funafunanibe, ndipo mudzapeza.”—Mateyo 7:7.

ŴELENGANI ZAMBILI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 38 NA 39

M’MUTU WOTSATILA

Kodi zimakuvutani kuuza ena za Mulungu? Onani zimene zingakuthandizeni kuti muzitha kuuza ena zimene mumakhulupilila.

LEMBA LOFUNIKILA

“Odala ndi anthu amene amazindikila zosowa zawo zauzimu.”Mateyu 5:3.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ŵelengani Baibo masamba anayi tsiku lililonse, ndipo mudzaimaliza pakutha caka cimodzi.

KODI MUDZIŴA . . .

Yehova amakukondani, ndipo umboni wa zimenezi ni wakuti mukuŵelenga buku lino komanso kutsatila malangizo ocokela m’Baibo omwe ali m’bukuli.—Yohane 6:44.

ZOTI NICITE

Kuti nizipindula kwambili n’kamaphunzila Baibo nizicita izi ․․․․․

Kuti nizipemphela nthawi zonse nizicita izi ․․․․․

Zimene nikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ni izi ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi mungacite ciani kuti muzisangalala kwambili pophunzila Baibo?

● N’cifukwa ciani Yehova amafunitsitsa kumvetsela mapemphelo a anthu opanda ungwilo?

● Kodi mungatani kuti mapemphelo anu azikhala ocokela pansi pamtima?

[Mau okopa]

Nili mwana, mapemphelo anga amakhala ongobweleza-bweleza. Palipano nikamapemphela, nimayesetsa kuchula zinthu zabwino na zoipa zimene zanicitikila patsikulo. Popeza kuti zocitika za tsiku na tsiku zimasiyana, zimenezi zimanithandiza kuti mapemphelo anga asamakhale ongobweleza-bweleza.”​—Anatelo Eve

[Bokosi/Cithunzi]

phunzilani Baibo mozama

1. Sankhani nkhani inayake imene mukufuna kuŵelenga m’Baibo. Pemphelani kwa Yehova kuti akuthandizeni kumvetsa nkhaniyo.

 2. Ŵelengani nkhaniyo mofatsa. Pamene mukuŵelenga, yelekezelani kuti munalipo pamene nkhaniyo inali kucitika, ndipo mukuona zimene zikucitika, mukumva mawu a anthu osiyana-siyana ochulidwa m’nkhaniyo, mukumva fungo la zinthu zimene zikuchulidwa, na zina zotelo.

3. Ganizilani zinthu zimene mwaŵelengazo. Dzifunseni mafunso monga aya:

● N’cifukwa ciani Yehova anafuna kuti nkhaniyi ilembedwe m’Mawu ake?

● Kodi ni anthu ati ochulidwa m’nkhaniyi omwe ni oyenela kutengela citsanzo cawo, nanga ni ati osayenela kuwatengela?

● Kodi m’nkhaniyi nikuphunzilamo ciani?

● Kodi nkhaniyi ikuniphunzitsa zotani zokhudza Yehova?

4. Pemphelani mwacidule kwa Yehova. M’fotokozeleni zimene mwaphunzila m’Baibo komanso zimene mukufuna kucita pogwilitsa nchito mfundozo. Nthawi zonse muziyamikila Yehova cifukwa ca mphatso imene wakupatsani imene ni Mawu ake, Baibo!

[Cithunzi]

Mawu anu ndiwo nyali ya kumapazi anga, ndi kuunika kwa panjila panga.”—Salmo 119:105.

[Bokosi/Cithunzi]

muzitsogoza zinthu zofunika kwambili

Kodi mumalephela kupemphela cifukwa cosowa nthawi? Kodi simupeza nthawi yophunzila Baibo? Ngati ni conco, ndiye kuti muli na vuto lolephela kuzindikila zinthu zofunika kwambili pamoyo.

Citani izi: Ikani miyala ingapo m’ndowa. Ndiyeno, thilanimo mcenga mpaka kudzaza bwino-bwino.

Kenako, khuthulilani mcenga na miyalayo pamalo abwino. Lomba tengani mcengawo na kuuthilanso m’ndowamo, kenako ikanimo miyala ija. N’zacidziŵikile kuti miyalayo sikwanamo cifukwa cakuti munayambila mcenga.

Kodi tikuphunzilapo ciani? Baibo imanena kuti: “Mutsimikizile kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Mukamaika zinthu zing’ono-zing’ono, monga zosangalatsa patsogolo, simudzatha kupeza nthawi yocitila zinthu zauzimu, zomwe ni zofunika kwambili. Koma mukatsatila malangizo a m’Baibo, mudzapeza kuti muli na nthawi yokwanila yocitila zinthu zauzimu ndiponso zosangalatsa. Kuti muthe kucita zimenezi, mufunika kuonetsetsa kuti mukutsogoza zinthu zofunika kwambili.

[Cithunzi]

Duwa lam’nyumba limafunika kulisamalila kuti likule bwino. N’cimodzi-modzinso na ubwenzi wanu na Mulungu